Ezek. 42 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyumba ziŵiri pafupi ndi Nyumba ya Mulungu

1Pambuyo pake munthu uja adapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto, nandiloŵetsa m'nyumba ina yoyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto.

2Nyumba yakumpotoyi m'litali mwake inali ya mamita makumi asanu, muufupi mwake inali ya mamita 25.

3Kuyang'anana ndi bwalo lam'kati la mamita khumi, ndiponso kuyang'anana ndi chiwundo cha bwalo lakunja, panali makonde atatu osanjikana.

4Kumaso kwa zipindazo kunali njira yam'kati, muufupi mwake mamita asanu, m'litali mwake mamita makumi asanu. Makomo ake adaaloza kumpoto.

5Zipinda zam'mwamba zinali zazifupi m'mimbamu kupambana zam'munsi ndi zapakati, chifukwa njira zake zam'kati zidaalanda malo ambiri.

6Zonse zinali zosanjikana patatu, ndipo zinalibe nsanamira monga za mabwalo. Motero zipinda zam'mwamba zinali zochepera kuyerekeza ndi zapakati ndi zapansi.

7Khoma lakunja, kutalika kwake mamita 25, linkatsatana ndi zipinda kutsogolo kwake pambali pa bwalo lakunja.

8Zipinda za m'mbali mwa bwalo lakunja m'litali mwake zinali za mamita 25. Koma zokhala m'mbali mwa Nyumba ya Mulungu ija m'litali mwake zinali za mamita makumi asanu.

9Pansi pa zipinda zimenezi panali khoma lake chakuvuma, kuchokera ku bwalo lakunja kumene khoma la bwalo linkayambira.

10Mbali yakumwera, kuyang'anana ndi bwalo ndi nyumbayo, kunali zipinda zina, ndipo kumaso kwake kunali njira.

11Zipinda zimenezi m'litali mwake ndi muufupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zolingana ndi zoyang'ana kumpoto zija. Makomo ake ndi zitseko zake zinalinso zolingana.

12Ndipo kunsi kwa zipinda zakumwera, kunali khomo lake mbali ya kuvuma kumene ankaloŵerako. Kunalinso khoma logaŵa zipinda.

13Tsono munthu uja adandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakumwera zoyang'anana ndi khonde nzoyera. M'menemo ansembe okhala kufupi ndi Chauta amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. M'menemo adzaikamo zopereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakudya, nsembe yopepesera machimo, ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi oyera.

14Ansembe ataloŵa m'malo oyerawo, sadzatulukamo kupita m'bwalo lakunja popanda kusiya m'menemo zovala zimene amavala potumikira zija. Zimenezi nzoyera. Ayenera kuvala zina asanafike pa anthu.”

Miyeso ya bwalo la Nyumba ya Mulungu

15Atamaliza kuyesa m'kati mwa Nyumba ya Mulungu, munthu uja adatuluka nane pa chipata chopenya kuvuma. Pamenepo adayesa bwalo lonse.

16Adayesa mbali yakuvuma ndi bango loyesera lija, kutalika kwake kunali kwa mamita 250.

17Kenaka adatembenuka nayesa mbali yakumpoto ndi bango lakelo, kutalika kwake kunali kwa mamita 250.

18Adatembenuka nayesa mbali yakumwera ndi bango lake. Kutalika kwake kunali kwa mamita 250.

19Adatembenukanso nayesa kuzambwe ndi bango lake. Kutalika kwake kunali kwa mamita 250.

20Motero adayesa mbali zonse zinai. Panali khoma lozungulira bwalo lonselo, m'litali mwake linali la mamita 250, muufupi mwakenso mamita 250. Khomalo linali lolekanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help