1Uzisamala mayendedwe ako ukamapita ku Nyumba ya Mulungu. Kuli bwino kupita kumeneko kukaphunzirako, kupambana kukangopereka nsembe chabe ngati anthu opusa, amene sadziŵa kuti akuchita zoipa.
2Usamafulumira kulankhula, ndipo usamalumbira msanga kwa Mulungu mumtima mwako. Paja Mulungu ali Kumwamba, iwe uli pansi pano, tsono usamachulukitsa mau ai.
3Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oipa, ndipo kuchuluka kwa mau kumadzetsa uchitsiru.
4 Mas. 66.13, 14 Ukalumbira chinthu kwa Mulungu, usachedwe kuchichita, chifukwa Mulungu sakondwera nazo zitsiru. Zimene wazilumbira, uzichitedi.
5Kuli bwino kusalumbira kanthu kwa Mulungu, kupambana kuti ulumbire koma osachita.
6Pakamwa pako pasakuchimwitse, kuti choncho usayenerenso kukauza wansembe wa Mulungu kuti, “Ai, ndinkangonena!” Chifukwa chiyani ufuna kuputa Mulungu? Kodi ukufuna kuti aononge zimene wazigwirira ntchito?
7Maloto akachuluka pamachulukanso zokamba zachabechabe. Koma iwe uzilemekeza Mulungu.
Moyo ndi wopanda phindu8Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo.
9Alimi onse amatengako dzinthu dzam'minda, koma ndi mfumu yokha imene imaona phindu lake la mindayo.
10Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.
11Chuma chikachuluka, odya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani? Si kumangoziyang'ana basi?
12Wantchito amagona tulo tabwino, ngakhale adye pang'ono kapena kudya kwambiri. Koma wolemera, chuma sichimgonetsa tulo.
13Pansi pano pali choipa china chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndachiwona: Chuma chopweteka mwiniwake yemwe.
14Ndiye chuma chimenecho chikamwazika moipa, munthuyo nkukhala ndi ana, amachita kusoŵa choŵapatsa ana akewo.
15Yob. 1.21; Mas. 49.17; 1Tim. 6.7 Monga momwe munthu adabadwira m'mimba mwa mai wake opanda kanthu, chonchonso adzapita maliseche. Pa zonse zimene adakhetsera thukuta, palibe nchimodzi chomwe chimene adzatenge m'manja mwake.
16Chimenechinso nchoipa chomvetsa chisoni kwambiri: kuti munthu adzapita monga momwe adabwerera. Nanga phindu lake nchiyani, popeza kuti iyeyo adagwira pachabe ntchito yolemetsa?
17Masiku ake onse moyo wake unali wodzaza ndi mdima ndi chisoni, unali moyo wa mavuto, matenda ndi nkhaŵa.
18Tsono chimene ndimachiwona kuti nchabwino ndi choyenera ndi ichi: kumadya, kumamwa, ndi kumakondwerera ntchito zonse zolemetsa zimene munthu umagwira pansi pano, pa masiku oŵerengeka a moyo wako amene Mulungu wakupatsa. Nchokhachi chimene ungati nchako, choyenera kulandira.
19Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.
20Munthu wotereyu sadzaganizako kwenikweni za kuchepa kwa masiku a moyo wake, chifukwa chakuti Mulungu wamdzaza ndi chimwemwe mu mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.