2 Am. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Antioko wachisanu achita chipangano ndi Ayuda

1Patapita zaka zitatu, Yudasi ndi anthu ake adamva kuti Demetriyo, mwana wa Seleuko, adakocheza ku dooko la Tripoli ndi gulu lalikulu ndi zombo zambiri,

2ndipo kuti adalanda dziko lonse, nkupha Antioko ndi nkhoswe yake Lisiyasi.

3Alikimo, amene kale adaali mkulu wa ansembe onse nkudziipitsa dala nthaŵi zosokonezeka zija, adamvetsa kuti sangathenso kukhala pa mtendere kapena kugwiranso ntchito za pa guwa loyera.

4Tsono adapita kwa mfumu Demetriyo chaka cha 151, nkukamupatsa chisoti chaufumu chagolide ndi kanjedza, ndiponso nthambi za olivi zimene ankazoloŵera kuzipereka ku Nyumba ya Mulungu. Pa tsikulo sadachite kanthu kena.

5Koma adapeza mpata wokwaniritsira zolinga zake zopenga, pa tsiku limene Demetriyo adamuitana ku msonkhano wa aphungu ake, namufunsa za maganizo a Ayuda ndi za zofuna zao.

6Pamenepo Alikimo adayankha kuti, “Ayuda otchedwa Asidea, amene mtsogoleri wao ndi Yudasi Makabeo, akulimbikitsa nkhondo, akuutsa zaupandu, choncho dziko likulephera kukhala pa mtendere.

7Nchifukwa chake ine atandichotsa pa ukulu umene ndidaulandira kwa makolo anga, ndikunenatu udindo wokhala mkulu wa ansembe onse, ndabwera kuno.

8Poyamba ndifuna kusamala ndi mtima woona zonse zokhudza inu amfumu, ndipo ndifuna kuthandizanso anzanga a ku dziko lakwathu, chifukwa dziko lathu lonse likuvutika nazo kwambiri zamisala za anthu ameneŵa.

9Inuyo amfumu, mukuzidziŵa bwino zimenezi, tsono ndikukupemphani chifundo chanu chimene chikudziŵika ndi onse.

10Ndithudi nthaŵi yonse imene Yudasiyo adzakhale ndi moyo, nkosatheka kuti dziko lonse likhale pa mtendere.”

11Iyeyo atanena mau ameneŵa, aphungu ena a mfumu amene ankadana ndi Yudasi, nawonso adakolezera kwambiri ukali wa Demetriyo.

12Motero mfumu Demetriyo adaitana Nikanore, amene ankalamulira gulu la njovu, namuika kuti akhale bwanamkubwa ku Yudeya, nkumutumiza kumeneko.

13Adamlamula kuti akaphe Yudasi ndi kumwaza anthu ake, ndipo kuti akaike Alikimo kuti akhale mkulu wa ansembe onse ku Nyumba ya Mulungu yaulemuyo.

14Tsono akunja onse a m'dziko la Yudeya, amene adaathaŵa nkhondo ya Yudasi, adasonkhana nkudzagwirizana ndi Nikanore, nkumaganiza kuti iwowo adzakhala pabwino chifukwa cha masautso ndi matsoka ogwera Ayuda.

Nikanore ayanjana ndi Yudasi

15 1Am. 7.27, 28 Ayuda atamva kuti Nikanore akubwera ndi nkhondo, ndipo kuti akunja ambiri ali naye, adadzithira fumbi kumutu nkuyamba kupemphera kwa Ambuye amene adadzisankhira mpingo kuti ukhalepo mpakampaka, amenenso amateteza anthu ake modabwitsa.

16Tsono mtsogoleri wao ataŵalamula, ankhondo adanyamukadi kumeneko nakamenyana nawo adaniwo pafupi ndi mudzi wa Desau.

17Simoni, mbale wa Yudasi, adayamba ndiye kumenyana ndi Nikanore. Pa kanthaŵi chabe ankaoneka ngati akulephera chifukwa cha mabweredwe odzidzimutsa a adani.

18Ngakhale zinali choncho, Nikanore atazindikira kuti anthu a Yudasi akuwonetsa kulimba mtima ndiponso kuti akuchita chamuna zedi pofuna kupulumutsa dziko lao, adaopa kumaliza nkhaniyi pokhetsa magazi.

19Motero adatuma Posidoniyo ndi Teodote ndi Matatiasi, kuti akapangane zoyanjana ndi Ayuda.

20Atakambirana bwino mfundo zonse, mtsogoleri wao adaŵadziŵitsa anthu ake, ndipo ataona kuti onse agwirizana, adavomerezana za chipangano.

21Adasankhula tsiku loti atsogoleri aŵiriwo adzakomane paokha. Padafika galeta limodzi kuchokera ku magulu ankhondowo, ndipo adakhazika mipando yaulemu pamalo pabwino.

22Koma Yudasi anali atabisa ankhondo ena m'malo oyenera, kuwopa kuti mwina adani ao nkuŵachita zina monyenga. Koma aŵiriwo adacheza bwino.

23Nikanore adakhala ku Yerusalemu osachita kanthu koipa, ndipo adaŵabweza anthu onse aja amene adaasonkhana kudzakhala mbali yake.

24Ankafuna kuti Yudasi azikhala naye nthaŵi zonse, ndipo aŵiriwo analidi abwenzi enieni.

25Nikanore adalangiza Yudasi kuti akwatire, kuti akhale ndi ana. Yudasi adakwatiradi, ndipo adakhazikika nayamba kukhala ngati anthu ena onse.

26Alikimo uja ataona kuti Nikanore ndi Yudasi akumvana bwino, adatenga mau a chipangano chao chija nkupita nawo kwa Demetriyo. Adamuuza kuti Nikanore sanalinso wokhulupirika, chifukwa adasankha Yudasi woukira boma uja kuti adzakhale mfumu iyeyo atafa.

27Mfumu idapsa mtima, ndipo zosinjirira zimene munthu woipayo ankanena zidaautsa ukali wake. Motero mfumu Demetriyo adalembera Nikanore kalata yonena kuti adakwiya nacho chipanganocho, ndipo adamlamula kuti mwamsanga atumize Makabeo ku Antiokeya ali womangidwa.

28Nikanore ataulandira uthengawo, adavutika mumtima mwake; adamva chisoni chifukwa choumirizidwa kuphwanya chipanganocho, pamene Yudasi sadachite kanthu kalikonse kosalungama.

29Koma kunali kosatheka kuti alikane lamulo la mfumu. Tsono adayamba kufunafuna nthaŵi yoyenera yoti amtchere msampha Yudasi.

30Koma Makabeo adazindikira kuti Nikanore sankamuchitiranso ulemu monga kale, ndipo kuti akakumana naye ankamuumira mtima. Tsono adamvetsa kuti kuuma mtima kwakeko kunali kosamufunira zabwino. Choncho adasonkhanitsa anthu ake ambiri, nakabisala kutali ndi Nikanore.

31 1Am. 7.29, 30 Nikanore ataona kuti Yudasi adamchita ndale, adapita ku Nyumba yaikulu ndi yoyera ya Mulungu, pamene ansembe ankapereka nsembe monga mwa masiku onse, ndipo adaŵalamula kuti ampereke munthuyo kwa iye.

32Iwowo adatsimikiza ndi kulumbira kuti sankadziŵa konse kumene kunali munthu amene ankamufunayo. Apo Nikanore adatambalitsa dzanja lake kuloza malo opatulika koposa aja nati,

33“Mukapanda kumpereka Yudasi kwa ine kuti ndimmange, ndidzaigumula Nyumba ya Mulunguyi, guwali nkuligwetsa pansi. Ndipo pa malo omwe ano ndidzamangapo nyumba ya Dionizio, mulungu wathu.”

34Atanena mau amenewo, adachoka. Pamenepo ansembe adakweza manja kumwamba, nayamba kupemphera kwa Mulungu, yemwe adakhala akuteteza mtundu wathu nthaŵi zonse. Adati,

35“Ambuye mwini zonse, simusoŵa kanthu konse. Kudakukomerani kuti pano pakhale Nyumba yokhalamo Inu pakati pa ife.

36Tsono Inu Woyera uja, Ambuye a kuyera konse, Nyumba imene tangoiyeretsa kumeneyi muisunge bwino kuti isaipitsidwenso.”

Imfa ya Razise

37Munthu wina dzina lake Razise, mmodzi mwa akuluakulu a mu Yerusalemu, adamneneza kwa Nikanore. Adamneneza kuti anali munthu wokonda anzake am'dzikomo, kuti anthu ankamulemekeza ndipo kuti ankatchedwa tate wa Ayuda.

38Nthaŵi zakale pamene Ayuda sankayenderana ndi anthu a mitundu ina, adaazengedwapo mlandu chifukwa cha chipembedzo Chachiyuda, mwakuti sadaope kudziika wathunthu m'zoopsa chifukwa cha Chiyuda.

39Pofuna kuwonetsa kuti ankadana ndi Ayuda, Nikanore adatuma ankhondo opitirira 500 kuti akamugwire.

40Ankaganiza kuti adzavuta Ayuda, akammanga ameneyo.

41Pamene ankhondowo anali pafupi kulanda nsanja, nkumathyola chitseko cha bwalo, adaitanitsa moto, nkutentha zitseko zonse. Razise poona kuti amzinga, adadzibaya ndi lupanga lake.

42Adasankhula kufa mwaulemu, osati kugwa m'manja mwa anthu ochimwa ndi kupirira manyozo osayenerana ndi ulemu wake.

43Koma chifukwa cha mfulumira, sadadzibaye moyenera ndi lupanga, nakanika kufa; nthaŵi imeneyo ankhondo aja nkumaloŵera pa khomo. Pamenepo iye adalimba mtima, adathamanga nakakwera pa khoma nkudziponya pansi pakati pa anthuwo.

44Onsewo adafutuka pang'ono, nasiya mpata, iye nkugwera pampatapo.

45Akupumabe koma ali ndi ukali, adadzambatuka, magazi ali chuchuchu, mabala aakulu akumpweteka m'thupi, adathamangira pakati pa anthuwo, naimirira pa chimwala chotsekera.

46Atataya magazi ake onse tsopano, adatulutsa matumbo ake, naŵagwira m'manja mwake. Adaŵaponyera anthuwo, akupemphera kwa Mwini moyo ndi mpweya kuti amubwezere zimenezi. Adafa motero.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help