Hag. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ulemerero wa Nyumba ya Mulungu yatsopano

1Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, pa tsiku la 21, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga.

2Uthengawu, wopita kwa Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndiponso kwa ena onse, udati,

3Eza. 3.12 “Kodi alipo ena mwa inu amene adaaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Monga simukuwona kuti tsopano ulemererowo watheratu?

4Komabe Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, usataye mtima iwe Zerubabele, usataye mtima iwe Yoswa, mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, musataye mtima inu nonse. Yambani ntchito, pakuti Ine ndili nanu ndithu.

5Eks. 29.45, 46 Musachite mantha, popeza kuti mzimu wanga uli pakati panu, monga momwe ndidalonjezera pamene munkatuluka ku Ejipito.

6 Ahe. 12.26 “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Patapita nthaŵi pang'ono, ndidzagwedeza mlengalenga ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda.

7Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu ndipo chuma cha anthu onse chidzabwera, motero Nyumba imeneyi ndidzaidzaza ndi ulemerero waukulu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

8Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanga.

9Choncho ulemerero wa Nyumba yachiŵiriyi udzaposa ulemerero wa Nyumba yoyamba ija. Ndipo ndidzakhazikitsa ufulu ndi mtendere pa malo ano. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Za kuipitsidwa

10Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinai, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga uwu wakuti,

11“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Mupemphe ansembe kuti agamule nkhani iyi:

12Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo ukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezinso zidzasanduka zopatulika? Ansembewo adayankha kuti, ‘Iyai.’ ”

13 Num. 19.11-22 Apo Hagai adaŵafunsanso kuti, “Nanga ngati munthu amene adaipitsidwa pokhudza mtembo, akhudzanso zimenezi, ndiye kuti zimenezinso zidzaipitsidwa?” Ansembe adayankha kuti, “Inde, zidzaipitsidwa.”

14Hagai adanena kuti, “Zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Nchimodzimodzinso ndi anthu ameneŵa, nchimodzimodzinso ndi mtundu umenewu pamaso panga. Zonse zimene amachita ndi zonse zimene amapereka ku nsembe nzoipitsidwa.

Za madalitso akutsogolo

15“ ‘Tsopano muganizire zimene zinkachitika asanayambe kumanganso Nyumba ya Chauta.

16Pamene munthu ankayembekeza kupeza miyeso ya tirigu makumi aŵiri ankangopeza khumi yokha. Akabwera kuti adzatunge miyeso makumi asanu mu mtsuko wa vinyo, ankangopeza makumi aŵiri okha.

17Ndidaononga mbeu zanu zonse ndi chinsikwi, chinoni ndi matalala. Komabe simudaganize zolapa,’ akutero Chauta.

18“Lero ndi tsiku la 24, mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku limene maziko a Nyumba ya Chauta aikidwa. Muganizirepo tsono,

19mulibe chakudya chambiri m'nkhokwe. Mpesa, mkuyu, makangaza ndiponso mtengo wa olivi zikali zosabereka. Koma kuyambira lero ndidzakudalitsani.”

Lonjezo la Chauta kwa Zerubabele

20Tsiku limenelo, tsiku la 24 la mwezi, Chauta adapatsanso Hagai kachiŵiri uthenga uwu wakuti,

21“Umuuze Zerubabele bwanamkubwa wa ku Yuda, kuti ndidzagwedeza mlengalenga ndi dziko lapansi.

22Ndidzagwetsa mafumu a mitundu ya anthu akunja ndi kuwononga mphamvu za maufumu ao. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake. Akavalo adzafa, ndipo okwerapo ao adzaphana.

23“Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Pa tsiku limenelo iwe Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Salatiyele, ndidzakutenga ndipo ndidzakusandutsa wolamulira m'dzina langa, pakuti ndiwe amene ndakusankhula. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help