1 Aro. 10.16; Yoh. 12.38 “Ndani wazikhulupirira zimene tamvazi?
Ndani wazindikira mphamvu za Chauta pa zimenezi?
2Pajatu mtumiki wake uja adakula
ngati chiphukira pamaso pa Mulungu,
ndiponso ngati muzu m'nthaka youma.
Iye analibe maonekedwe enieni
kapena nkhope yabwino,
kuti ife nkumamuyang'ana.
Analibe kukongola koti ife nkukokeka naye.
3Iye uja anthu adamnyoza ndipo adamkana.
Anali munthu wamasautso, wozoloŵera zoŵaŵa.
Anali ngati munthu amene anzake
amaphimba kumaso akamuwona.
Anthu adamnyoza, ndipo ife sitidamuyese kanthu.
4 Mt. 8.17 “Ndithudi, iye adapirira masautso
amene tikadayenera kuŵamva ifeyo,
ndipo adalandira zoŵaŵa
zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo.
Koma ife tinkaganiza kuti
ndi Mulungu amene akumlanga,
ndi kumkantha ndi kumsautsa.
5 1Pet. 2.24 Koma adambaya chifukwa cha machimo athu,
ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu.
Chilango chimene chidamgwera iye
chatipatsa ife mtendere,
ndipo mabala ake atichiritsa.
6 1Pet. 2.25 Tonse tidaasokera ngati nkhosa.
Aliyense mwa ife ankangodziyendera.
Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.
7 Chiv. 5.6 Ntc. 8.32, 33 “Anthu adamsautsa ndi kumzunza,
koma iye sadalankhule kanthu.
Monga momwe amachitira mwanawankhosa
wopita naye kuti akamuphe,
ndiponso monga momwe nkhosa imakhalira duu poimeta,
nayenso adangokhala chete.
8Adamgwira mwankhanza namuzenga mlandu,
ndipo adapita naye kukamupha.
Mwa anthu anzake ndani adalabadako
zoti iye adachotsedwa m'dziko la anthu amoyo?
Ndani adalabadako kuti iye uja
adalangidwa chifukwa cha machimo a anthu?
9 1Pet. 2.22 Adamkonzera manda ake pakati pa manda a achifwamba.
Adamuika m'manda pakati pa anthu olemera,
ngakhale iye sadachitepo chosalungama
chilichonse ndipo
sadanene bodza lililonse.”
10Komabe ndi Chauta yemwe
amene adaafuna kuti amuzunze,
ndipo adamsautsadi.
Iye adapereka moyo wake
kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo.
Choncho adzaona zidzukulu zake,
adzakhala ndi moyo wautali,
ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye.
11Atatha mazunzo akewo,
adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira.
Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo
adzasenza machimo a anthu onse
kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.
12 Mk. 15.28; Lk. 22.37 Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu.
Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu,
popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa,
ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo.
Adasenza machimo a anthu ambiri,
ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.