Mas. 110 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu yosankhidwa ndi ChautaSalmo la Davide.

1 Mt. 22.44; Mk. 12.36; Lk. 20.42, 43; Ntc. 2.34, 35; 1Ako. 15.25; Aef. 1.20-22; Akol. 3.1; Ahe. 1.13; 8.1; 10.12, 13 Chauta adauza Mbuye wanga kuti,

“Khala ku dzanja langa lamanja,

mpaka nditasandutsa adani ako

kukhala ngati chopondapo mapazi ako.”

2Chauta adzakuza ufumu wako wamphamvu

kuchokera ku Ziyoni.

Adzati,

“Khala mfumu yolamulira adani ako.”

3Anthu ako adzadzipereka mwaufulu,

pa tsiku limene udzaonetse mphamvu zako pa phiri loyera.

Anyamata ako adzabwera kwa iwe mu unyinji wao,

monga m'mene mame amabwerera m'mamaŵa.

4 Ahe. 5.6; 6.20; 7.17, 21 Chauta walumbira

ndipo sadzasintha maganizo ake akuti,

“Ndiwe wansembe mpaka muyaya,

unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”

5Ambuye ali pambali pako.

Adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wao.

6Adzalanga mitundu ya anthu akunja,

adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo.

Adzagonjetsa olamulira a pa dziko lonse lapansi.

7Adzamwa mu mtsinje wam'njira,

ndipo adzaŵeramutsa mutu monyadira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help