Mphu. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chidakwa sichilemera, ngakhale chikhale pa ntchito.

Munthu wonyoza zinthu zazing'ono, amanka naagwa

pang'onopang'ono.

2Zoledzeretsa ndiponso akazi zimaononga anthu anzeru.

Munthu wokonda akazi adama amatha manyazi moipa.

3Potsiriza pake adzakhala chakudya cha mphutsi ndi

nyongolotsi,

kupanda manyazi kwakeko kudzamuphetsa.

Kulankhula zachabe nkoipa

4Kukhulupirira munthu msanga kumaonetsa mtima

wosaganiza bwino,

ndipo kuchimwa kumapweteka wochimwa yemweyo.

5Munthu wokondwerera machimo

adzalangidwa.

6Koma wodana ndi ukazitape

zoipa zimamuchepera.

7Usamabwerezabwereza zimene udamva,

ndipo sudzapeza mavuto.

8Kaya ndi bwenzi wako kaya ndi mdani wako,

usamkambire,

usaulule pokhapokha ngati nkuchimwa kukhala chete.

9Mwina ena nkumva mau akowo nayamba kusakukhulupirira,

pambuyo pake nkudzadana nawe.

10Ngati wamva mphekesera, zithere mwa iwe.

Usachite mantha, sungaphulike nazo.

11Chitsiru chikamva kanthu, chimamva kupweteka mu mtima

ngati kupweteka kwa mkazi pobala mwana.

12Mumtima mwa chitsiru mukaloŵa nkhani,

ndiye ngati mpaliro wazika m'ntchafu.

Usakhulupirire zonse zakumva

13Umfunse bwenzi wako, mwina mwake sadachite kanthu,

ndipo ngati adachita kanthu,

ndiye kuti sadzachitanso.

14Umfunse mnzako, mwina mwake sadanene kanthu.

Ngati adanenadi, sadzanenanso.

15Umfunse bwenzi lako, poti osinjirira ngambiri.

Usakhulupirire zonse zokuuza anthu.

16Mwina munthu amalankhula padera mosafuna.

Kodi ndani asanachimwe konse polankhula.

17Usanaopseze mnzako, uyambe wamufunsa bwino,

uleke Malamulo a Mulungu Wopambanazonse agwire ntchito.

18Kuwopa Ambuye ndiye chiyambi choti atikomere mtima,

ngati uli ndi luntha Ambuye amakukonda.

19Kudziŵa Malamulo a Ambuye ndiye mwambo wopatsa moyo.

Amene amachita zokomera Ambuye, amadya za mtengo wa moyo wosatha.

Za nzeru zoona ndi zonyenga

20Nzeru nkuwopa Ambuye,

nzeru nkutsata Malamulo ndi kudziŵa kuti Mulungu

ndiye Wamphamvuzonse.

21Wantchito wouza mbuye wake kuti, “Sindichita

zimene mukufuna,”

ngakhale pambuyo pake achitebe,

zimamupsetsa mtima munthu womsunga uja.

22Komatu kukhala wodziŵa pa zoipa si nzeru,

malangizo a anthu ochimwa sangakuphunzitse zanzeru.

23Pali kuchenjera kwina kumene anthu amadana nako

ndipo pali zitsiru zina zongokhala zopanda nzeru.

24Ndi bwino kukhala woopa Mulungu uli wopanda nzeru

kupambana kukhala ndi nzeru zambiri uli wophwanya Malamulo.

25Pali kuchenjera kwina kwenikweni ndithu koma

kosalungama,

palinso anthu opotoza zoona kuti zinthu ziŵayendere bwino.

26Pali tambwali woyenda ŵeraŵera kuwonetsa chisoni,

pamene mumtima mwake ali wonyenga.

27Amaphimba nkhope namadziwonetsa ngati wosamva,

koma ngati palibe wina woyang'ana, amakuchenjerera.

28Pali ena amene sachimwa chifukwa chosoŵa mphamvu,

koma akangopeza danga, amachita ndithu zoipa.

29Munthu ungathe kumdziŵira maonekedwe,

ndipo munthu wanzeru amazindikirika

ndi pamaso pomwe.

30Zovala za munthu ndi kasekedwe kake

ndiponso kayendedwe,

zonsezi zimaonetsa mkhalidwe wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help