Yob. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yob. 4.17 Tsono Yobe adayankha kuti,

2“Inde, ndikudziŵa kuti zimenezi ndi zoona,

koma nanga munthu angathe bwanji kukhala wolungama

pamaso pa Mulungu?

3Kodi wina aliyense angathe kutsutsana ndi Mulungu?

Ai sangathe kutsutsana naye,

chifukwa Mulungu ali ndi mafunso ambiri osayankhika.

4Mulungu ndi wanzeru, ndipo ndi wamphamvu kwambiri.

Palibe munthu amene angathe kulimbana naye,

popanda kupwetekerapo.

5Iyeyo amasendeza mapiri, iwo osadziŵako,

amaŵagubuduza ali wokwiya.

6Ndiye amene amagwedeza dziko lapansi ndi zivomezi,

ndipo mizati yake imanjenjemera.

7 Bar. 3.34, 35 Ndiye amene angalamule dzuŵa kuti lisatuluke m'maŵa,

ndi kuletsa nyenyezi kuti zisaŵale usiku.

8Ndi Mulungu yekha amene adayala zakuthambo,

ndiye amayenda pa mafunde apanyanja.

9 Yob. 38.31; Amo. 5.8 Ndiye amene adalenga nyenyezi za

Mlalang'amba ndi Akamwiniatsatana,

Nsangwe ndi Kumpotosimpita.

10Ndiye amene amachita zazikulu zosamvetseka,

ndiye amene amachita zodabwitsa zosaŵerengeka.

11Ndithu Mulungu akapita pafupi ndi ine,

sindimuwona konse. Akandidutsa, ine sindimpenya.

12Akamalanda zinthu, ndani angathe kumletsa?

Ndani angathe kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’

13“Mulungu sabweza ukali wake,

adaononga adani ake othandizana ndi Rahabu,

chilombo choipa chija.

14Nanga ineyo ndingathe kumuyankha bwanji?

Mau okangana naye ndingaŵapeze kuti?

15Ngakhale ndine wosachimwa,

sindingathe kumuyankha Mulungu.

Ndiyenera kungopempha chifundo

kwa Iye amene akundizenga mlandu.

16Ngakhale ndikadamuitana, Iye nkuvomera,

sindikhulupirira kuti akadamvadi mau angawo.

17Paja amandikantha ndi mavuto onga mphepo yamkuntho,

amandipweteka ndi mabala ambiri,

popanda nchifukwa chomwe.

18Mulungu sandilola kuti ndipume,

koma amandichulukitsirachulukitsira zoŵaŵa.

19Kodi ine nkulimbana ndi Mulungu, mphamvu zonse zija?

Kodi ine nkutsutsana ndi Mulungu pa bwalo la milandu?

Ndani angamuzenge mlandu?

20Ngakhale ndine wosalakwa,

komabe zolankhula zanga zikhoza kunditsutsa.

Ngakhale ndine wopanda cholakwa,

akadandipezabe kuti ndine wolakwa.

21Ine ndiye ndilibe mlandu,

koma sindidziyenereza, moyo wanga ndimaunyoza.

22Palibe chabwino ai. Nchifukwa chake ndikuti,

Mulungu amaononga anthu oipa ndi anthu abwino omwe.

23Pamene munthu wosachimwa afa mwadzidzidzi,

Mulungu amangoseka tsoka la munthu wosachimwayo.

24Mulungu akapereka dziko m'manja mwa anthu oipa,

amaŵatseka maso anthu oweruza dzikolo.

Ngati si Iyeyo wachita zimenezi, nanga nkukhala yani?

25“Masiku anga ndi othamanga kwambiri

kupambana munthu waliŵiro.

Masikuwo amapita, ine osaona zabwino.

26Amayenda ngati zombo zaliŵiro zapanyanja,

ngati mphungu yogudukira nyama yoti idye.

27Mwina ndinganene kuti, ‘Ndidzaiŵala madandaulo anga,

nkhope yanga sidzakhalanso yachisoni,

ndipo ndidzasangalala.’

28Koma ndimaopabe kuti mavuto anga onse

adzabwereranso pa ine, pakuti ndikudziŵa kuti

Mulungu sadzavomereza kuti ine ndine wosalakwa.

29Ngati ndine wolakwa ndithu,

chabwinotu, zagwa zatha!

30Ngakhale ndisambe thupi lonse

ndi madzi oyera kwambiri,

ndi kusamba m'manja ndi sopo,

31Mulungu adzandiponyabe pa dzala,

ndipo zovala zanga zomwe zidzachita nane nyansi.

32Zoona, Mulungu si munthu ngati ine,

kuti ndingakangane naye,

sindingathe kutsutsana naye pa mlandu.

33Palibe mkhalapakati woti nkutiweruza aŵirife,

woti nkugamula mlandu pakati pa Mulungu ndi ine.

34Mulungu asandilange ndi ndodo yake,

kuwopa Iye kusandidetse nkhaŵa.

35Motero ndidakatha kulankhula osamuwopa,

koma monga zilirimu, sindingathe konse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help