1Chauta adauza Mose kuti,
2“Ulipsire Amidiyani chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, tsono pambuyo pake udzafa.”
3Mose adauza Aisraele kuti, “Amuna ena pakati panupa mutenge zida zankhondo, kuti mukamenyane ndi Amidiyani, kuti Chauta aŵalipsire.
4Mutumize ku nkhondo anthu chikwi chimodzi pa fuko lililonse la Israele.”
5Choncho pa anthu a Aisraele ambirimbiri aja, Mose adatumiza anthu chikwi chimodzi pa fuko lililonse, ndipo onse anali 12,000 pamodzi.
6Mose adaŵatumiza ku nkhondo anthuwo, chikwi chimodzi pa fuko lililonse, pamodzi ndi Finehasi mwana wa wansembe Eleazara, iyeyu atanyamula zipangizo za ku malo opatulika ndi malipenga ochenjeza m'manja mwake.
7Aisraelewo adamenyana nkhondo ndi Amidiyani, monga momwe Chauta adaalamulira Mose, ndipo adapha amuna onse.
8Adapha mafumu a ku Midiyani pamodzi ndi anthu ao omwe. Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a ku Midiyani. Adaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori.
9Ndipo adagwira akazi a ku Midiyani ukapolo, pamodzi ndi ana ao. Adalandanso ng'ombe zao, nkhosa zao, ndi chuma chao chonse.
10Adatentha mizinda yonse imene iwo ankakhalamo, ndi zithando zao zonse,
11natenga zonse zimene adalanda kunkhondoko, anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
12Tsono adabwera nawo akapolowo, pamodzi ndi zonse zimene adalandazo, kwa Mose, kwa wansembe Eleazara ndi kwa mpingo wonse wa Aisraele, ku zithando za ku zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko.
Ankhondo abwerera13Mose ndi wansembe Eleazara, pamodzi ndi atsogoleri a mpingo, adakaŵachingamira kunja kwa zithando.
14Ndipo Mose adakwiyira akulu ankhondowo, atsogoleri olamulira ankhondo zikwi ndiponso atsogoleri olamulira ankhondo mazana, amene ankachokera ku nkhondo.
15Mose adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwaŵasiya amoyo akazi onse?
16Num. 25.1-9 Paja akazi ameneŵa adatsata uphungu wa Balamu, nasokeretsa Aisraele kuti asachitenso zokhulupirika pamaso pa Chauta ku Peori kuja, kotero kuti mliri udagwera mpingo wa Chauta.
17Nchifukwa chake tsono iphani mwana wamwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense amene adadziŵapo ndi mwamuna.
18Koma atsikana amene sadagone ndi mwamuna, muŵasunge akhale anu.
19Tsono aliyense mwa inu amene wapha munthu, kapena amene wakhudza mtembo, akhale kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mudziyeretse inuyo pamodzi ndi akapolo anu.
20Muyeretse chovala chilichonse, chinthu chilichonse chachikopa, chinthu chilichonse chopangidwa ndi ubweya wambuzi, ndi chinthu chilichonse chopangidwa ndi mtengo.”
21Tsono wansembe Eleazara adauza ankhondo amene adaapita ku nkhondowo kuti, “Lamulo limene Chauta walamula Mose ndi ili:
22Izi zokha, golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, chiwaya ndi mtovu,
23zonse zimene sizingathe kupsa ndi moto, muziike pa moto, ndipo zidzayeretsedwa. Komabe ziyeretsedwenso ndi madzi oyeretsera, ndipo chilichonse chimene chingathe kupsa ndi moto, muchiviike m'madzi omwewo.
24Muchape zovala zanu pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, ndipo mudzayeretsedwa. Pambuyo pake muloŵe ku mahema.”
Kugaŵana zofunkha25Chauta adauza Mose kuti,
26“Iwe, ndi wansembe Eleazara, pamodzi ndi atsogoleri a mabanja a mpingo, muŵerenge zofunkha zimene adalanda pa nkhondo, anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
27Ndipo mugaŵe zofunkhazo magawo aŵiri, lina la ankhondo amene adaapita ku nkhondo, lina la mpingo wonse.
28Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Chauta, pa zofunkha mazana asanu aliwonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, pa ng'ombe, pa abulu ndi pa nkhosa.
29Mutenge zimenezo pa gawo la ankhondowo ndipo mupatse wansembe Eleazara, kuti zikhale zopereka zanu kwa Chauta.
30Ndipo pa gawo la Aisraele, mtengeko chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, pa anthu, ng'ombe, abulu, nkhosa ndi pa nyama zonse zoŵeta, ndipo mupatse Alevi amene amayang'anira Chihema cha Chauta.”
31Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adachitadi zomwe Chauta adalamula Mose.
32Zofunkha zotsala zimene ankhondowo adalanda zinali izi: nkhosa 675,000,
33ng'ombe 72,000,
34abulu 61,000,
35ndi atsikana amene sadagonepo ndi amuna 32,000 pamodzi.
36Gawo la ankhondo amene adapita ku nkhondo linali nkhosa 337,500,
37ndipo gawo la Chauta linali nkhosa 675.
38Ng'ombe zinalipo 36,000, ndipo 72 zinali gawo la Chauta.
39Abulu analipo 30,500, ndipo 61 anali gawo la Chauta.
40Anthu analipo 16,000, ndipo 32 anali gawo la Chauta.
41Mose adapereka kwa wansembe Eleazara gawo limene linali loyenera kulipereka kwa Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Moseyo.
42Mose adagaŵa zofunkha napatsa Aisraele theka limodzi, kuchotsa pa zofunkha zonse zobwera ndi ankhondo aja.
43Tsono gawo la Aisraele linali ili: nkhosa 337,500,
44ng'ombe 36,000,
45abulu 30,500,
46ndiponso anthu 16,000.
47Pa gawo la Aisraelelo, Mose adatengako chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo adapatsa Alevi amene ankayang'anira Chihema cha Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
48Pamenepo akulu a nkhondo amene ankayang'anira ankhondo onse, ndiye kuti atsogoleri olamulira ankhondo zikwi, ndi atsogoleri olamulira ankhondo mazana, adabwera kwa Mose.
49Adauza Moseyo kuti, “Atumiki anufe taŵerenga ankhondo amene tikuŵalamulira, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene akusoŵa.
50Ndipo ife tabwera ndi zopereka kwa Chauta zimene munthu aliyense adapeza, monga golide, zibangiri, zikono, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda, kuti achitire mwambo wopepesera machimo athu pamaso pa Chauta.”
51Apo Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golide kwa atsogoleriwo, pamodzi ndi zinthu zonse zosula.
52Golide yense amene iwo adapereka kwa Chauta kuchokera kwa atsogoleri a ankhondo zikwi, ndi kwa atsogoleri a ankhondo mazana, anali wolemera makilogaramu 200 yense pamodzi.
53(Ankhondo aja anali atatenga zofunkha, aliyense zakezake.)
54Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golideyo kwa atsogoleri a ankhondo zikwi ndi a ankhondo mazana, namuika m'chihema chamsonkhano, kuti akhale chikumbutso cha Aisraele pamaso pa Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.