Yob. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Apo Elifazi wa ku Temani adayankha kuti,

2“Kodi munthu wanzeru angalankhule zachabechabe motere?

Kodi angathe kutulutsa mau opandapake

ongouluka ngati mphepo?

3Kodi angathe kulankhula zinthu zopandapake,

kapena kunena mau opanda phindu?

4Koma iwe ukufuna kuti anthu asamaope Mulungu,

ukufuna kuti aleke kusinkhasinkha za Mulungu.

5Tchimo lako likuwonekera ndi kalankhulidwe kako,

koma umafuna kudzilungamitsa

ndi kuchenjera pakamwa kwako.

6Choncho ndi mau ako omwe amene akukutsutsa, osati ine.

Pakamwa pako pomwe pakuchita umboni wokuzenga mlandu.

7“Kodi munthu woyamba kubadwa ndiwe?

Kodi udaalipo pamene Mulungu ankalenga mapiri?

8Kodi uli m'gulu la alangizi a Mulungu?

Kodi ukuyesa wanzeru ndiwe wekha?

9Kodi nchiyani chimene umadziŵa iwe,

chosachidziŵa ife?

Kodi chilipo chimene umamvetsa iwe,

chosachimvetsa ife?

10Pakati pa ife pano tili ndi anthu aimvi ndi okalamba,

amvulazakaletu kupambana bambo wako.

11Kodi akukuchepera mau othuzitsa mtima

ochokera kwa Mulunguŵa,

kapena mau okulankhula mofatsaŵa?

12“Nanga chifukwa chiyani ukupsa mtima?

Chifukwa chiyani ukutituzulira maso?

13Chifukwa chiyani ukufuna kulimbana ndi Mulungu?

Chifukwa chiyani ukumnyoza ndi pakamwa pako?

14 Yob. 25.4-6 Kodi munthu nchiyani kuti angathe kukhala wosachimwa?

Kapena wobadwa kwa mkazi nchiyani,

kuti angakhale wopanda uchimo pamaso pa Mulungu?

15Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake.

Ngakhale akumwamba omwe sali angwiro pamaso pake.

16Nanji tsono munthu,

amene ali wonyansa ndi wachabechabe,

amene kuchita zoipa kuli ngati kumwa madzi!

17“Undimve, ine ndikufotokozera,

zimene ndidazimva ndikuuza.

18Zoonazo adandiphunzitsa ndi anthu anzeru,

sadandibisire zimene adamva kwa makolo ao.

19Dziko lao linali lopanda anthu achilendo,

amene adakaŵachotsa mu njira yake ya Mulungu.

20Munthu woipa amakhala akuvimvinika ndi zoŵaŵa

masiku onse a moyo wake.

Munthu wankhalwenso adzavutika zaka zake zonse.

21Amamva mau oopsa m'makutu mwake,

pamene akuyesa kuti ali pabwino,

achifwamba adzamthira nkhondo.

22Sakhulupirira kuti angathe kupulumuka

ku mdima wa imfa,

akuyenera kuphedwa ndithu basi.

23Amangoyendayenda paliponse,

kunka nafuna chakudya nkumati, ‘Kodi chili kuti?’

Amadziŵa kuti tsiku lamdima lili pafupi.

24Masautso ndi nthumanzi zimamchititsa mantha kwambiri.

Zimenezi zimamgudukira koopsa, monga imachitira mfumu

imene yakonzekera kukamenya nkhondo.

25Zonsezi zamugwera chifukwa adaukira Mulungu.

Adafuna kulimbana ndi Mphambe.

26Adatenga chishango chake mwaliwuma,

ndipo adathamanga kuti akalimbane ndi Mulungu.

27“Ngakhale nkhope yake ndi yokulupala,

ngakhale m'chiwuno mwake muli monenepa kwambiri,

28munthuyo adzasauka m'mizinda yoonongeka.

Adzakhala m'nyumba zosayenera kukhalamo anthu,

chifukwa zidaonongeka pa nkhondo.

29Iyeyo sadzalemera, chuma chake sichidzakhalitsa.

Minda yake sidzaberekanso pa dziko lapansi.

30Iyeyo sadzatuluka m'mavuto, adzakhala ngati mtengo

umene nthambi zake zapsa ndi moto,

Umene maluŵa ake adzachotsedwa ndi mpweya wa Mulungu.

31Asadzinyenge pokhulupirira zinthu zoipa zachabe,

poti zinthu zachabezo ndizo zidzakhale malipiro ake.

32Adzafota nthaŵi isanakwane,

ndipo nthambi yake sidzaphukanso.

33Adzakhala ngati mtengo wamphesa

umene umayoyola zipatso zake zisanapse.

Adzakhala ngati mtengo wa olivi

umene wayoyola maluŵa ake.

34Anthu osamvera Mulungu adzakhala opanda zidzukulu.

Olandira ziphuphu moto udzapsereza nyumba yao.

35Ameneŵa ndiwo amalingalira zaupandu namachita zoipa.

Mtima wao umaganizira zonyenga nthaŵi zonse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help