Lk. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za Yesu ndi Zakeyo

1Yesu adaloŵa m'Yeriko, ulendo wake wobzola mzindawo.

2Kudafika munthu wina, dzina lake Zakeyo. Iyeyo anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera.

3Ankafunitsitsa kuwona Yesu kuti ngwotani. Koma pakuti Zakeyoyo anali wamfupi, adalephera kumuwona chifukwa cha kuchuluka kwa anthu.

4Tsono adathamangira kutsogolo, nakakwera mu mkuyu kuti amuwone, chifukwa Yesu ankayenera kudzera pamenepo.

5Ndiye pamene Yesu adafika pamalopo, adayang'ana m'mwamba, namuuza kuti, “Zakeyo, fulumira, tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala nao kunyumba kwako.”

6Pompo Zakeyo adafulumira, natsika, kenaka nkukamlandiradi Yesu mokondwa kwambiri.

7Poona zimenezi, anthu onse adayamba kung'ung'udza. Adati, “Wakakhala kunyumba kwa munthu wochimwa.”

8Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.”

9Apo Yesu adamuuza kuti, “Chipulumutso chafika m'banja lino lero, popeza kuti ameneyunso ndi mwana wa Abrahamu.

10 ankafuna kumupha,

48koma adaasoŵa chochita, chifukwa anthu onse ankatengeka nawo mtima mau ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help