1M'maŵa mwake Holofernesi adalamula ankhondo ake ndi ena onse othandizana naye kuti anyamuke, akalande mipata ya pakati pa mapiri ndi kumenya nkhondo ndi anthu a ku Betuliya.
2Gulu lake linali la anthu 170,000 oyenda pansi ndi 12,000 okwera pa akavalo, osaŵerengera anthu apansi oyang'anira katundu. Onse pamodzi anali chinamtindi chachikuludi cha anthu.
3Adamanga zithando zankhondo m'chigwa pafupi ndi Betuliya, pafupi ndi kasupe wa madzi. Zithando zao zankhondo zidalanda malo aakulu: m'mimba mwake kuchokera ku Dotani mpaka ku Balibaimu, m'litali mwake kuchokera ku Betuliya mpaka ku Kiyamoni, mzinda woyang'anana ndi Esdreloni.
4Aisraele ataona kuchuluka kwao adachita mantha aakulu, nayamba kuuzana kuti, “Anthu ameneŵa adzaononga dziko lonse. Mapiri aatali, zigwa ndi zitunda sizidzatha kuŵaimitsa anthu ochuluka chotereŵa.”
51Am. 12.28, 29Tsono aliyense adatenga zida, nasonkha moto pa nsanja, nkuchezera usiku wonse ali maso.
6Pa tsiku lachiŵiri lake Holofernesi adatsogolera gulu lake lankhondo lokwera pa akavalo, Aisraele ku Betuliya akumuwona bwino lomwe.
7Adakayendera malo oloŵera mu mzinda wao. Adakaonanso akasupe kumene ankatungako madzi. Adalanda akasupewo nakhazikapo asilikali olonda, iye nkubwerera kwa ankhondo ake.
8Tsono atsogoleri onse a ku Edomu ndi Mowabu, ndi atsogoleri ankhondo a m'mbali mwa nyanja, adabwera kwa iye. Adadzamuuza kuti,
9“Mverani zimene tikukuuzani inu mbuye wathu ndipo mupulumutse gulu lanu lankhondo kuti asaligonjetse.
10Aisraele ameneŵa sakhulupirira zida zao zankhondo, koma amaŵapulumutsa ndi mapiri aatali kumene amakhala, poti nkovuta kuŵakwera mapiri ameneŵa.
11Tsono inu mbuye wathu Holofernesi, musati mumenyane nawo nkhondo moŵalunjika, ndipo choncho palibe ndi mmodzi yemwe mwa asilikali anu amene adzaphedwe.
12Ingokhalani m'zithando zanu zankhondo, anthu anu akhale pafupi nanu. Komabe atumiki anufe tilanda kasupe wa patsinde pa phiri,
13chifukwa ndiko kumene anthu a ku Betuliya amatungako madzi akumwa. Tsono akamva ludzu, adzapereka mzinda wao kwa inu. Ife ndi anthu onse tidzakwera mapiri oyandikana nafe. Tidzakhala kumeneko kuti titsimikize kuti wina aliyense asatuluke mu mzinda.
14Iwowo, akazi ao, ndi ana ao adzafa ndi njala. Asanaphedwe ndi lupanga, miseu yao idzadzaza ndi mitembo yao.
15Motero mudzaŵalipsira chifukwa choti adakugalukirani m'malo mokulandirani mwamtendere.”
16Holofernesi ndi akuluakulu ake onse adakondwa nawo mau ameneŵa, motero adalamula kuti zichitikedi.
17Asilikali a ku Mowabu aja adaphatikizana ndi ankhondo 5,000 a ku Asiriya, nakamanga zithando zankhondo ku chigwa, nkukalanda zitsime zimene Aisraele ankamwamo.
18Pambuyo pake Aedomu ndi Aamoni adakamanga zithando kumapiri moyang'anana ndi Dotani. Ena adaŵatuma kumwera ndi kuvuma kumaloŵera cha ku Akraba, mzinda woyandikana ndi Kusi, pafupi ndi mtsinje wa Mokomuri. Gulu lotsala la Aasiriya lidakamanga zithando zao ku chigwa. Adadzaza dziko lonselo ndi zithando zao zochuluka zedi ndi katundu wao, chifukwa cha unyinji wa ankhondowo.
19Tsono Aisraele adafuula kwa Ambuye, Mulungu wao, poti adaatayiratu mtima, chifukwa adani ao adaaŵazinga, kuchita kusoŵa populumukira.
20Gulu lonse lankhondo la Aasiriya, oyenda pansi, okwera pa akavalo ndi pa magaleta, adazinga mzinda wa Aisraelewo pa masiku 34. Madzi adatheratu m'mitsuko ya anthu a ku Betuliya.
21Zitsime zao zinkayamba kuphwa. Madzi ankacheperachepera kotero kuti panalibe tsiku limene panali madzi okwanira, chifukwa aliyense ankachita kumgaŵira pang'onopang'ono.
22Ana ao adayamba kufooka, akazi ndi anyamata nkumakomoka ndi ludzu. Ankangogwa pansi m'miseu ndi m'njira zamumzinda. Analibiretu mphamvu konse.
23Tsono anthu onse, anyamata, akazi ndi ana adasonkhana kwa Uziya ndi kwa akuluakulu a mumzindamo. Adafuula kwambiri pamaso pa akuluakuluwo kuti,
24“Mulungu agamule mlandu pakati pa inu ndi ife. Mwatilakwira kwambiri posayanjana ndi Aasiriya.
25Tsopano tilibe ndi mmodzi yemwe wotithandiza. Mulungu watipereka m'manja mwao. Adzatipeza titafa ndi ludzu, dziko litadzaza ndi mitembo yathu.
26Inu ingogonjani kwa anthu a Holofernesi, lilekeni gulu lake lankhondo lifunkhe mzindawu.
27Nkwabwino kuti ifeyo tigulidwe. Inde tidzakhala akapolo, komabe tidzakhala tili moyo, ndipo sitidzaonerera ana athu alikufa kapena akazi athu akuthatha ndi imfa.
28Dziko lakumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zathu zokutsutsani pamaso pa Mulungu wathu, Ambuye a makolo athu, amene akutilanga chifukwa cha machimo athu ndi machimo a makolo athu. Tikupempha kuti zoopsa zimene tanenazi zisatigwere lero lino.”
29Tsono gulu lonse la anthu lidalira chokweza, nkuyamba kupemphera kwa Ambuye, Mulungu wao.
30Pamenepo Uziya adaŵauza kuti, “Limbani mtima abale anga! Tiyembekeze masiku asanu ena. Ambuye, Mulungu wathu, adzatichitiranso chifundo, ndithudi sadzatisiya.
31Koma masikuwo akatha osalandira chithandizo, ndidzachitadi zimene mwapemphazi.”
32Atanena zimenezo, Uziya adaŵabweza anthuwo aliyense ku malo ake. Choncho ena adapita ku malinga ao, ena ku nsanja zao. Akazi ndi ana adaŵabweza kwao. Koma mumzinda monsemo munali chisoni chachikuludi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.