1Kuli bwino kudya mkute wouma pali bata,
kuposa kuchita madyerero m'nyumba m'mene muli mikangano.
2Kapolo wochita zinthu mwanzeru
adzalamula mwana wa mfulu wochita zamanyazi,
kapoloyo adzagaŵana nawo choloŵa ngati mmodzi mwa
abale.
3Siliva amamuyesera m'chitofu,
golide amamuyesera m'ng'anjo,
koma mitima amaiyesa ndi Chauta.
4Wochita zoipa amamvera malangizo oipa,
wabodza amamvera zochoka m'kamwa monyenga.
5Amene amalalatira mmphaŵi, amanyoza Mlengi wake.
Amene amakondwerera tsoka la mnzake adzalangidwa.
6Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,
ulemerero wa ana ndi atate ao.
7Kulankhula kwabwino sikuyenerana ndi chitsiru.
Nanji kulankhula kwabodza, kodi kungayenerane ndi mfumu?
8Chiphuphu chili ngati mankhwala amwai
kwa wochiperekayo,
kulikonse kumene amapita, amalemera.
9Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi,
koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
10Munthu wanzeru amamva kamodzi,
munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.
11Munthu woipa mtima amangofuna zoukira.
Tsono adzamtumira wamthenga wankhalwe.
12Kuli bwino kukumana ndi chimbalangondo
cholandidwa ana,
kupambana kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.
13Munthu akamabwezera zoipa kwa zabwino,
tsoka silidzachoka pabanja pake.
14Chiyambi cha mkangano chili ngati kukhamulira madzi,
ndiye uzichokapo ndeu isanabuke.
15Woweruza munthu woipa mtima kuti ndi wosalakwa,
amanyansa Chauta,
nayenso wopasa mlandu munthu wosalakwa amaipira Chauta.
16M'manja mwa wopusa mungakhalirenji ndalama
zogulira nzeru,
chikhalirecho mutu wake suyenda bwino?
17 Mphu. 6.7-10 Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse,
ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza
pa mavuto.
18Munthu wopanda nzeru amapereka chikole,
ndipo amasanduka chigwiriro pamaso pa mnzake.
19Wokonda zolakwa amakonda mkangano.
Wokonda kulankhula zonyada amadziitanira chiwonongeko.
20Munthu wa mtima woipa zake sizimuyendera bwino.
Ndipo wa pakamwa ponena zoipa amagwa m'tsoka.
21Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake,
bambo wake wa chitsiru sakhala ndi chimwemwe.
22Mtima wosangalala umakhala ngati mankhwala abwino,
koma mtima woziya umaumitsa thupi.
23Munthu woipa amalandira chiphuphu cham'seri,
ndipo amapotoza chigamulo cha mlandu.
24Munthu wanzeru amaika mtima pa nzeru,
koma chitsiru chimangoti maso mwalamwala pa dziko lonse.
25Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake,
ndipo amapweteka mtima wa amai ake amene adambala.
26Kulipitsa munthu wosalakwa nkoipa.
Si chilungamo kukwapula anthu abwino.
27Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu,
munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.
28 Mphu. 20.5 Nchitsiru chomwe chikakhala chete,
chimakhala ngati munthu wanzeru.
Chikasunga pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.