1 Eks. 25.31-40; 37.17-24 Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aroni kuti, pamene ukuika nyale, uike zisanu ndi ziŵiri, ndipo ziwunikire patsogolo pa choikaponyale.”
3Aroni adaikadi nyalezo. Adaziika kuti ziwunikire patsogolo pa choikaponyale, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
4Choikaponyalecho adachipanga motere: chinali chagolide, ndipo kuyambira patsinde pake mpaka ku maluŵa ake, chinali chosula. Adapanga choikaponyalecho potsata chitsanzo chomwe Chauta adaaonetsa Mose.
Alevi aŵapereka kwa Chauta5Chauta adauza Mose kuti,
6“Upatule Alevi pakati pa Aisraele, ndipo uŵayeretse.
7Kuŵayeretsa kwake uchite motere: uŵawaze madzi oyeretsera machimo ao. Amete m'thupi monse ndi lumo, ndipo achape zovala kuti adziyeretse.
8Tsono iwowo atenge mwanawang'ombe wamphongo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya wosalala wosakaniza ndi mafuta. Iweyo utenge mwanawang'ombe wina wamphongo woperekera nsembe yopepesera machimo.
9Ubwere ndi Alevi pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo usonkhanitse mpingo wonse wa Aisraele.
10Pamene ukuŵapereka Aleviwo pamaso pa Chauta, Aisraele asanjike manja ao pa Alevi.
11Kenaka Aroni apereke Aleviwo pamaso pa Chauta, kuti akhale chopereka choweyula cha Aisraele, kuti ntchito ya Alevi ikhaledi yotumikira Chauta.
12Pambuyo pake Alevi asanjike manja ao pamitu ya ng'ombe zamphongo, ndipo iwe upereke kwa Chauta ng'ombe imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Inayo uipereke kuti ikhale nsembe yopsereza, kuchitira mwambo wopepesera machimo a Alevi.
13Uŵauze Aleviwo kuti azitumikira Aroni ndi ana ake aamuna, ndipo uŵapereke kwa Chauta ngati chopereka choweyula.
14“Umu ndi m'mene upatulire Alevi pakati pa Aisraele, ndipo adzakhala anga.
15Pambuyo pake Aleviwo adzaloŵa kuti atumikire m'chihema chamsonkhano, utaŵayeretsa ndi kuŵapereka ngati chopereka choweyula.
16Ndithudi, iwoŵa aperekedwa kwathunthu kwa Ine pakati pa Aisraele. Ndaŵatenga kuti akhale anga m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa, ana achisamba onse a Aisraele.
17Eks. 13.2 Ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisraele ndi anga, ana a anthu ndi a nyama omwe. Ndidaŵapatula onseŵa kuti akhale anga, pa tsiku limene ndidapha ana onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito.
18Tsono pakati pa Aisraele ndaŵatenga Alevi m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa.
19Aleviwo ndaŵatenga pakati pa Aisraele ndi kuŵapereka ngati mphatso kwa Aroni ndi ana ake aamuna, kuti azidzatumikira m'malo mwa Aisraele, m'chihema chamsonkhano. Azikachita mwambo wopepesera machimo a Aisraele, kuti mliri ungaŵagwere Aisraele amene ayandikire pafupi ndi malo opatulika.”
20Umu ndimo m'mene Mose ndi Aroni ndi mpingo wonse wa Aisraele, adaŵachitira Alevi. Aisraele adachitira Aleviwo zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
21Alevi adadziyeretsa ku zoipa, ndipo adachapa zovala zao. Aroni adaŵapereka kuti akhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta, naŵachitira mwambo wopepesera machimo ao, kuti aŵayeretse.
22Pambuyo pake Alevi adapita kukagwira ntchito zao m'chihema chamsonkhano, ndipo ankatumikira Aroni ndi ana ake. Choncho Aleviwo adaŵachitira monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
23Chauta adauza Mose kuti,
24“Ntchito za Alevi ndi izi: kuyambira anthu a zaka 25 ndi opitirirapo, azipita kukagwira ntchito yotumikira m'chihema chamsonkhano.
25Akafika zaka makumi asanu aleke ntchito yotumikira, ndipo asatumikirenso.
26Koma azithandiza abale ao m'chihema chamsonkhano ndi kumayang'anira ntchitoyo, koma asatumikire. Umu ndimo m'mene udzachitire poŵagaŵira ntchito zao Aleviwo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.