Deut. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mizinda yopulumukirako(Num. 35.9-28; Yos. 20.1-9)

1 Yos. 20.1-9 Chauta, Mulungu wanu, ataononga eniake a dziko limene akukupatsanilo, ndipo inu mutalanda mizinda yao pamodzi ndi nyumba zao, nkukhazikika kumeneko,

2mudzapatule mizinda itatu m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsenilo.

3Mudzakonze miseu yake, ndipo mudzaligaŵe patatu dzikolo. Choncho kudzakhala malo amene munthu wopha mnzake adzatha kuthaŵirako.

4Nali lamulo lokhalira munthu wopha mnzake, amene angapulumutse moyo wake pothaŵira kumeneko: Munthu akapha mnzake mwangozi, osati chifukwa cha chidani, athaŵire ku mzinda uliwonse mwa mizinda imeneyo kuti apulumuke.

5Mwachitsanzo, anthu aŵiri apita ku thengo limodzi kukadula mitengo. Wina podula mtengo, nkhwangwa nkuguluka, nipha mnzakeyo. Iye angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, napulumuka.

6Akapanda kutero, mwina chifukwa cha kutalika kwa mtunda, wachibale wofuna kumlipsira adzamthamangira mwaukali, nkumugwira wothaŵayo namupha, ngakhale ali wosayenera kuphedwa, chifukwa paja popha munthu mwangozi analibe chidani chilichonse ndi amene adafayo.

7Nchifukwa chake ndikukulamulani kuti mupatule mizinda itatu.

8Chauta, Mulungu wanu, akadzakuza dziko lanu monga momwe adalonjezera makolo anu, ndipo akadzakupatsani dziko lonse limene adalonjeza,

9pamenepo mudzapatulenso mizinda ina itatu. Adzakuwonjezerani dziko ndithu, malinga mukamakachita zonse zimene ndikukulamulani, ndiye kuti kukonda Chauta, Mulungu wanu, ndi kuchita zonse zimene akukuphunzitsani.

10Muzidzachita zimenezi kuti musadzalakwe pakupha anthu osachimwa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo.

11Mwina mwake munthu adana ndi mnzake, ndipo amkhalizira namupha mwadala, nkuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti apulumuke.

12Zikatero, akuluakulu akwao adzamuitanitse kuchokera ku mzinda wakewo, ndi kukampereka kwa woyenera kumlipsira uja kuti aphedwe ndithu.

13Musamchitire chifundo. Mchotseni pakati pa Aisraele munthu wopha mnzake wosalakwa, kuti zinthu zikuyendereni bwino.

Za malire akale

14 Deut. 27.17 M'choloŵa chomwe mudzakhala mutalandira m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakaŵafutuze malire a mnzanu amene anthu akale adakhazika.

Za mboni

15 Num. 35.30; Deut. 17.6; Mt. 18.16; Yoh. 8.17; 2Ako. 13.1; 1Tim. 5.19; Ahe. 10.28 Mboni imodzi sikwanira kumtsimikiza munthu kuti wachimwadi kapena kuti wapalamuladi mlandu pakuchita cholakwa chakutichakuti. Chofunika nchakuti pakhale mboni ziŵiri kapena zitatu zotsimikiza kuti munthuyo walakwadi.

16Munthu wina akaneneza mnzake momnamizira kuti walakwa,

17aŵiri onsewo abwere, adzaimirire pamaso pa Chauta. Kumeneko aŵaweruze ansembe ndi aweruzi amene ali pa ntchito nthaŵi imeneyo.

18Aweruziwo adzafufuze za mlanduwo. Akapeza kuti munthu uja ndi mboni yachabe ndipo kuti waneneza mnzake monama,

19amlange pomchita choipa chimene iyeyo anati achite mnzake. Mwa njira imeneyi, mudzachotsa choipa chimenechi pakati pa inu.

20Tsono wina aliyense akadzamva zimene zachitika, adzakhala ndi mantha, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzachitenso choipa choterechi.

21Eks. 21.23-25; Lev. 24.19, 20; Mt. 5.38 Musachite chifundo. Chilango chake chikhale chakuti moyo ulipe moyo, diso lilipe diso, dzino lilipe dzino, dzanja lilipe dzanja, ndipo phazi lilipe phazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help