Owe. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Debora ndi Baraki.

1Ehudi atamwalira, Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta.

2Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanani, amene ankalamulira ku Hazori. Mtsogoleri wa ankhondo ake anali Sisera amene ankakhala ku Haroseti-Goimu.

3Tsono Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize, pakuti Sisera anali ndi magaleta achitsulo okwanira 900, ndipo adaazunza Aisraele mwankhalwe zaka makumi aŵiri.

4Nthaŵi imeneyo Debora mneneri wamkazi, mkazi wa Lapidoti, ndiye amene ankatsogolera Aisraele.

5Iye ankakhala patsinde pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Betele, m'dziko lamapiri la Efuremu, ndipo Aisraele ankabwera kwa iye kuti aŵaweruze.

6Deborayo adatuma munthu kuti akaitane Baraki, mwana wa Abinowamu, wa ku Kedesi m'dziko la Nafutali. Baraki atabwera, Debora adamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akukulamula kuti, ‘Pita ukasonkhanitse anthu ako ku phiri la Tabori, ndipo utenge anthu 10,000 m'fuko la Nafutali ndi m'fuko la Zebuloni.

7Ine ndidzamkopa Sisera, mtsogoleri wa ankhondo a Yabini, kuti adzakumane nanu ku mtsinje wa Kisoni, atatenga magaleta ake ndi ankhondo ake, ndipo ndidzampereka m'manja mwanu.’ ”

8Baraki adayankha kuti, “Mukapita, nanenso ndipita, koma mukapanda kupita, inenso sindipita.”

9Debora adati, “Chabwino, ndipita nanu, komatu inu simudzalandirapo ulemu mutapambana, pakuti Chauta adzapereka Sisera m'manja mwa munthu wamkazi.” Tsono Debora adanyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki.

10Baraki adaitana mafuko a Zebuloni ndi a Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu amene adamtsata analipo 10,000, ndipo Debora adapita nawo limodzi.

11Nthaŵi imeneyo Mkeni wina, dzina lake Hebere, anali atadzipatula mwa Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, ndipo adakamanga hema lake kutali, pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu, pafupi ndi Kedesi.

12Tsono pamene Sisera adamva kuti Baraki, mwana wa Abinowamu, wapita ku phiri la Tabori,

13adaitanitsa magaleta ake achitsulo 900 onse aja ndi anthu onse amene anali naye. Iwo adanyamuka kuchokera ku Haroseti-Goimu mpaka ku mtsinje wa Kisoni.

14Debora adauza Baraki kuti, “Dzukani, ndi lero tsiku limene Chauta wapereka Sisera m'manja mwanu. Kodi suja Chauta wakutsogolerani kale?” Pamenepo Baraki adatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumtsata.

15Ndipo Chauta adasokoneza Sisera ndi magaleta ake onse, pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi ankhondo ake ankaŵatsata pambuyo alikupha anthu ambiri. Sisera adatsika pa galeta lake nayambapo kuthaŵa pansi.

16Baraki adalondola magaletawo ndi ankhondowo mpaka ku Haroseti-Goimu, ndipo ankhondo onse a Sisera adaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka.

17Koma Sisera adathaŵa pansi mpaka kukafika ku hema la Yaele, mkazi wa Hebere, Mkeni uja, pakuti panali mtendere pakati pa Yabini, mfumu ya ku Hazori, ndi banja la Hebere Mkeniyo.

18Yaele adatuluka kukachingamira Sisera, namuuza kuti, “Loŵani mommuno mbuyanga, loŵani. Musaope kanthu.” Choncho adaloŵa m'hemamo ndipo adamfunditsa bulangete.

19Siserayo adamuuza mkaziyo kuti, “Pepani ndithu mai, patseniko madzi akumwa pang'ono, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo adatsekula thumba lachikopa la mkaka nampatsa kuti amwe, namfunditsanso bulangete.

20Kenaka adauza mkazi uja kuti, “Mukaime pakhomo pa hema, ndipo munthu aliyense akabwera ndi kukufunsani kuti, ‘Kodi muli munthu m'menemo?’ Mumuuze kuti, Ai, mulibe.”

21Koma Yaele, mkazi wa Hebere, adakatenga chikhomo cha hema, nakatenganso nyundo m'manja mwake, ndipo adayenda monyang'ama napita kwa Sisera uja. Pamene iyeyo anali m'tulo chifukwa chotopa, mkazi uja adakhomera chikhomo chija m'litsipa mwake. Chidatulukira kwinaku mpaka kuloŵa m'nthaka, iye kufa nkukhala komweko.

22Pamene Baraki adabwera akulondola Sisera, Yaele adatuluka kukamchingamira, namuuza kuti, “Loŵani, ndikuwonetseni munthu amene mukumfunayo.” Iye adaloŵa m'hema la mkaziyo, ndipo adangoona Sisera ali thasa pansi atafa, chikhomo cha hema chili tototo m'litsipa mwake.

23Motero tsiku limenelo Mulungu adagonjetsa anthu a Yabini, mfumu ya ku Kanani, pamaso pa Aisraele.

24Ndipo Aisraele adapanikizabe Yabini, mfumu ya ku Kanani, mpaka kumuwonongeratu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help