1Chauta adauza Mose kuti,
2“Utenge Aroni ndi ana ake. Utengenso zovala, mafuta odzozera, ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziŵiri zamphongo, ndipo utengenso dengu la buledi wosafufumitsa.
3Tsono usonkhanitse mpingo wonse pa khomo la chihema chamsonkhano.”
4Mose adachitadi zomwe Chauta adamlamula. Choncho mpingo wonse udasonkhana pa khomo la chihema chamsonkhano.
5Ndipo adauza mpingo wonsewo kuti, “Nazi zimene Chauta walamula kuti zichitike.”
6Apo Mose adabwera ndi Aroni ndi ana ake, naŵasambitsa.
7Kenaka adamuveka mwinjiro Aroniyo, ndi kummanga lamba m'chiwuno. Adamuveka mkanjo ndi chovala cha efodi, ndipo adammanganso lamba wa efodiyo m'chiwuno.
8Tsono adamuveka chovala chapachifuwa, ndipo m'chovalacho adaikamo zinthu zotchedwa Urimu ndi Tumimu.
9Ndipo adamuveka nduŵira kumutu. Kumaso kwa nduŵirayo adaikako mphande yagolide, chizindikiro chopatulira, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
10Pambuyo pake Mose adatenga mafuta odzozera, nadzoza chihema chamsonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali m'menemo, ndipo adazipatula.
11Adawazako mafuta ena kasanu ndi kaŵiri pa guwa, nalidzoza guwalo pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Adadzozanso mkhate pamodzi ndi phaka lake, kuti zikhale zopatulika.
12Mafuta ena odzozerawo adaŵathira pamutu pa Aroni, namdzoza, ndi kumsandutsa wopatulika.
13Kenaka adabwera ndi ana a Aroni aja naŵaveka miinjiro, naŵamanga malamba m'chiwuno, ndi kuŵaveka zikofiya kumutu.
14Pambuyo pake Mose adabwera ndi ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.
15Kenaka Mose adaipha natenga magazi ake ndi kuŵapaka ndi chala chake pa nyanga za guwa molizungulira, ndipo adaliyeretsa. Adathiranso magazi patsinde pa guwalo nalipatula. Motero adachita mwambo wopepesera machimo.
16Tsono Mose adatenga mafuta onse akumatumbo ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndi imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndipo adazitenthera paguwapo.
17Koma ng'ombe yamphongo ija, chikopa chake, nyama yake, ndi ndoŵe yake, zonsezi adazitenthera kunja kwa mahema, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
18Pambuyo pake adapereka nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosayo.
19Kenaka Mose adaipha nathira magazi ake pa guwa mozungulira.
20Atadula nkhosayo nthulinthuli, Mose adatentha mutu wake ndi nthuli zija ndi mafuta ake omwe.
21Tsono atatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, adazitenthanso. Motero adatentha nkhosa yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma, yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, monga momwe Iye adaalamulira Mose.
22Tsono Mose adapereka nkhosa ina yamphongo, yoyenerera pa mwambo wodzoza ansembe. Ndipo Aroni pamodzi ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
23Apo Mose adaipha, natengako magazi ake naŵapaka pa nsonga ya khutu la Aroni ku dzanja lamanja. Adapakanso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha ku phazi la dzanja lamanja.
24Pambuyo pake adabwera ndi ana a Aroni, ndipo Mose adapaka magazi pa nsonga za makutu ao a ku dzanja lamanja ndi pa zala zao zazikulu za ku dzanja lamanja, ndiponso pa zala zao zazikulu za ku phazi la ku dzanja lamanja. Kenaka Mose adathira magazi pa guwa molizungulira.
25Adatenga mafuta, mchira wamafuta, mafuta onse akumatumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ake omwe, ndi ntchafu ya ku dzanja lamanja.
26Ndipo m'dengu la buledi wosafufumitsa, lopatulikira Chauta, adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi wopaka mafuta ndi mtanda umodzi wa buledi wopyapyala. Zonsezo ataziika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija,
27adazikhazika m'manja mwa Aroni ndi m'manja mwa ana ake, ndipo adaziweyula kuti zikhale zopereka zoweyula kwa Chauta.
28Pambuyo pake Mose adazichotsa m'manja mwaomo nazitentha pa guwa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ija, kuti zikhale nsembe yopereka pa mwambo wodzoza ansembe, ya fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto yopereka kwa Chauta.
29Ndipo adatenga nganga naiweyula kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Chimenecho ndicho chigawo cha Mose cha nkhosa yamphongo yopereka pa mwambo wodzoza ansembe, potsata malamulo a Chauta kwa Mose.
30Tsono Mose adatengako mafuta odzozera aja ndi magazi amene anali pa guwa, nawaza Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zao. Umu ndimo m'mene Mose adapatulira Aroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zao.
31Mose adauza Aroni ndi ana ake kuti, “Muphike nyamayo pa khomo la chihema chamsonkhano, ndipo muidyere pomwepo, pamodzi ndi buledi amene ali m'dengu la zopereka pa mwambo wodzoza ansembe, potsata zimene Chauta adaalamula kuti, ‘Aroni pamodzi ndi ake ndiwo adzadye zimenezo.’
32Zotsala zake za nyamayo ndi za buledi zomwe, muzitenthe.
33Ndipo pa masiku asanu ndi aŵiri musatulukire kunja kwa chihema chamsonkhano, mpaka masiku a mwambo wodzoza ansembe atatha, poti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi aŵiri.
34Chauta adatilamula kuti tikuchiteni zimene takuchitanizi, kuti ukhale mwambo wopepesera machimo anu.
35Muzikhala pa khomo la chihema chamsonkhano usiku ndi usana, masiku asanu ndi aŵiri, ndipo muzichita zimene Chauta wakulamulani, kuti mungafe. Zimenezi nzimene Chauta wandilamula.”
36Tsono Aroni ndi ana ake adachitadi zonsezo, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.