1 Am. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Imfa ya Antioko Epifane

1Pa nthaŵi imene mfumu Antioko ankayendera zigawo za dziko zakumpoto, adamva za mzinda wina wa ku Persiya, dzina lake Elimaisi, umene unkatchuka chifukwa cha siliva ndi golide wake.

2Adaamvanso kumeneko kuti kuli nyumba ya milungu yao m'mene munali chuma chambiri, zishango zagolide, zovala zachitsulo zankhondo, ndi zida zimene adaazisiyamo Aleksandro, mwana wa Filipo, mfumu ya ku Masedoniya, amene anali woyamba kulamulira Agriki.

3Iyeyo tsono adapita komweko kuti akayese kulanda mzindawo pamodzi ndi chuma chake. Koma adalephera chifukwa anthu amumzindamo adaadziŵiratu cholinga chake,

4motero adalimbana naye mwamphamvu. Tsono iye adathaŵa ndi chisoni chachikulu, nkubwerera ku Babiloni.

5Akadali ku Persiya, wamthenga adafika kudzamdziŵitsa kuti magulu ake ankhondo amene adaakathira nkhondo ku Yudeya aonongeka.

6Adamusimbira kuti Lisiyasi amene adaapita ku nkhondo ndi gulu lamphamvu, adathaŵa Ayuda. Choncho Ayudawo adakulitsa mphamvu zao ndi zida zankhondo, ndi katundu ndiponso ndi chuma chambiri chimene adachifunkha atapambana magulu ankhondowo.

7 chosati nkubzala mbeu m'minda.

50Mfumu italanda Betizure, idaikako kaboma kankhondo kolonda mzindawo.

51Pambuyo pake adaniwo adamanga mahema ankhondo kuyang'anana ndi Nyumba ya Mulungu, nakhalako masiku ambiri. Adapangako makina amitundumitundu ankhondo ndi makina oponyera moto, mivi ndi miyala.

52Nawonso Ayuda okhala m'katimo adaimika makina ao, namenyana ndi adani masiku ambiri.

53Koma chakudya chaocho chidaaŵathera, chifukwa chaka chimenecho chinali chachisanu ndi chiŵiri chija, ndipo Ayuda okhala m'maiko a akunja, amene adaathaŵira ku Yudeya, anali atadya chakudya chotsala.

54Ayuda oŵerengeka okha adaatsala m'malo oyera, chifukwa njala idaachepetsa gulu lao, ndipo ambiri anali atabalalika, aliyense kunka kwao.

Mfumu ilola Ayuda kupembedza mwaufulu

55Paja panali Filipo, amene mfumu Antioko akali moyo adaamusankha kuti amlere mwana wake Antioko ndi kumlonga ufumu.

56Iyeyo atabwerako ku Persiya ndi ku Mediya, pamodzi ndi ankhondo omwe adaaperekeza mfumu, adaganiza zolanda ulamuliro wa dziko.

57Atamva zimenezo, Lisiyasi adaganiza zochoka mofulumira. Motero adauza mfumu, atsogoleri a ankhondo ndiponso ankhondo omwe kuti, “Ife kufooka kwathu kukunka kukukulirakulira tsiku ndi tsiku, chakudya tili nachochi nchochepa, ndipo malo amene taŵazinga ngolimba ndithu, ndiponso sitingaleke kusamala dziko lathu.

58Ndiye tiyeni tingoyanjana nawo anthuŵa ndi kupangana za mtendere ndi iwoŵa ndiponso ndi mtundu wao wonse.

59Tiyeni tiŵalole kuti azitsata miyambo yao monga kale. Adaatikwiyira ndi kuchita nkhondo zonse zija chifukwa cha miyamboyo, imene ife tidaithetsa.”

60Mau ameneŵa adakomera mfumu, motero idatumiza anthu kwa Ayuda kuti apangane za mtendere, iwowo nkuvomera.

61Tsono mfumu ndi atsogoleri ake ankhondo, onse adachita malumbiro, ndipo atatero, Ayuda adatuluka m'malinga ao ankhondo.

62Koma mfumu italoŵa m'chinyumba chankhondo cha ku phiri la Ziyoni, niwona malinga ake amphamvu, idaphwanya lumbiro lake. Idalamula kuti agumule malinga pozungulira ponse.

63Kenaka idachoka mofulumira kubwerera ku Antiokeya kumene idakapeza Filipo akulamulira mzindawo. Pamenepo idamenyana naye nkhondo, nkulanda mzindawo.

Mfumu Demetriyo amvana ndi Ayuda oipa
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help