Yob. 32 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsono anthu atatu aja adaleka osamulankhuzanso Yobe, chifukwa choti iyeyo adaadziwona kuti ndi wosachimwa.

2Koma Elihu, mwana wa Barakele, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, adapsera mtima Yobe chifukwa chodziyesa wolungama kupambana Mulungu.

3Adapseranso mtima abwenzi ake atatu aja, chifukwa choti sadathe kuyankha, ngakhale iwo omwe adaapeza kuti Yobeyo ndi wolakwa.

4Koma Elihu adadikira kuti alankhule ndi Yobe, chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.

5Tsono ataona kuti anthu atatuwo sadamuyankhe Yobe moyenera, adapsa mtima.

6Choncho Elihu, mwana wa Barakele wa fuko la Buzi, adayamba kulankhula, adati,

“Ine ndine wamng'ono, inuyo ndinu akuluakulu.

Nkuwona ndinkaopa, ndipo ndinkachita mantha

kuti ndikuuzeni zakukhosi.

7Ndinkati ayambe ndi akuluakulu aja kulankhula,

chifukwa amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.

8Koma mzimu wa Mphambe

ndiwo umaloŵa mwa anthu ndi kuŵapatsa nzeru.

9Sikuti ukalamba wokha ndiwo

umasandutsa anthu kuti akhale anzeru,

si kukhwima kokha kumene kumachititsa

kuti anthu azimvetsa zimene zili zoyenera.

10Nchifukwa chaketu ndikuti,

‘Mundimve, lekeni ndinenepo maganizo anga.’

11“Zoona, ndinkadikira mau anuwo,

ndinkafuna kumvetsera mau ogwira mtima

pamene inuyo munkafunafuna zanzeru zoti mulankhule.

12Ndidakumvetseranidi,

koma panalibe ndi mmodzi yemwe mwa inu

amene adatsutsa mau a Yobe,

panalibe amene adayankhako nkomwe.

13Chenjerani, musanene kuti,

‘Ife tapeza nzeru,

Mulungu ndiye angamgonjetse, osati munthu ai.’

14Yobe sadalankhule ndi ine,

ndipo ine sindimuyankha monga

m'mene mwamuyankhira inu.”

15“Iwowo asokonezeka, sakuyankhanso.

Alibe ndi mau omwe oti angalankhule.

16Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakulankhula,

kodi ndisayankhekonso poti iwo angoti phee?

17Ai, ine ndiyankhapo tsopano.

Nanenso ndilankhula zakukhosi.

18Pakuti ndili nawo mau ambiri,

mtima wanga ukundichichiza kuti ndilankhule.

19Ndithudi, maganizo adzaza mumtima mwanga

ali ngati vinyo wopanda pompungulira,

ineyo ndili ngati matumba atsopano achikopa

ofuna kuphulika ndi vinyo.

20Ndiyenera kulankhula kuti mtima utsike.

Pakufunika kuti ndiyankhepo pa nkhaniyi.

21Sindiwonetsa kukondera munthu wina aliyense,

sindilankhula zoshashalika.

22Ine sindidziŵa kulankhula mochenjera,

kuwopa kuti Mlengi wanga angandilange msanga.”

Elihu adzudzula Yobe kuti ndi wodzikuza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help