1Amaziya anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yehowadani wa ku Yerusalemu.
2Tsono adachita zolungama pamaso pa Chauta, komabe osati ndi mtima wangwiro ai.
3Tsono atangolandira mphamvu zonse zaufumu m'manja mwake, adapha anyamata ake amene adaapha mfumu ija, bambo wake.
4Deut. 24.16 Koma ana ao sadaŵaphe, potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a m'buku la Mose, m'mene Chauta adalamula kuti, “Atate sadzaphedwa chifukwa cha ana ao, kapena ana kuphedwa chifukwa cha atate ao. Koma munthu aliyense adzafera machimo ake.”
Amaziya ayambana nkhondo ndi Aedomu(2 Maf. 14.7)5Tsiku lina Amaziya adasonkhanitsa Ayuda naŵakhazika potsata mabanja ao. Adaŵapatsanso atsogoleri a anthu zikwi ndi a anthu mazana, ku Yuda konse ndi ku Benjamini komwe. Adasonkhanitsa anthu a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo. Anthuwo analipo 300,000, anthu osankhika, okhoza nkhondo, odziŵa kugwira mkondo ndi chishango.
6Adalembanso anthu ankhondo amphamvu ndi olimba mtima a ku Israele, okwanira 100,000, pa mtengo wa makilogramu 3,400 a siliva.
7Koma munthu wina wa Mulungu adadza kwa iye, namuuza kuti, “Inu amfumu, musapite ndi gulu lankhondo la ku Israele, pakuti Chauta sali nawo anthu ku Israele, ana a Efuremuŵa.
8Mukaganiza kuti mudzakhala ndi mphamvu kunkhondoko mwa njira imeneyi, Mulungu adzakugonjetsani pamaso pa adani. Pakuti Mulungu ndiye ali ndi mphamvu za kuthandiza ndi za kugonjetsa.”
9Amaziya adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Koma nanga bwanji za makilogramu a siliva aja amene ndapatsa gulu lankhondo la ku Israele?” Munthu wa Mulunguyo adayankha kuti, “Chauta angathe kukupatsani zambiri kupambana zimenezi.”
10Pamenepo Amaziya adalichotsa gulu lankhondo la ku Efuremu kuti libwerere kwao. Gulu lankhondolo lidaŵapsera mtima kwambiri anthu a ku Yudawo, ndipo lidapita kwao lili lokwiya kwabasi.
11Koma Amaziya adalimba mtima, ndipo adaŵatsogolera anthu ake kunka nawo ku Chigwa cha Mchere. Adakaphako anthu okwanira 10,000 a ku Seiri.
12Anthu a ku Yuda adagwira anthu ena amoyo okwaniranso 10,000. Adakwera nawo pamwamba pa thanthwe, naŵaponya pansi kuchoka pamenepo. Ndiye onsewo adangotekedzeka.
13Koma gulu lankhondo limene Amaziya adalibweza lija, osalilola kuti lipite nao ku nkhondo, lidakathira nkhondo mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya mpaka ku Betehoroni, naphako anthu okwanira 3,000 ku mizindayo, ndipo adatengako zofunkha zambiri.
14Tsono Amaziya atabwerako kuja adakapha Aedomuku, adabwera ndi milungu ya anthu a ku Seiri, naiika kuti ikhale milungu yake. Ndipo ankaipembedza ndi kumaifukizira lubani.
15Nchifukwa chake Chauta adamkwiyira Amaziya. Adatuma mneneri kwa iyeyo, kukamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukufuna milungu ya anthu, imene sidathe kuŵapulumutsa anthuwo m'manja mwanu?”
16Koma pamene mneneriyo ankalankhula, mfumu ija idamufunsa kuti, “Kodi iweyo tidakuika kuti ukhale phungu wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?” Mneneriyo adakhala chete kanthaŵi, kenaka adati, “Ndikudziŵa kuti Mulungu watsimikiza zoti akuwonongeni inu, chifukwa chakuti inuyo mwachita zimenezi osamvera uphungu wanga.”
Amaziya achita nkhondo ndi Israele(2 Maf. 14.8-20)17Nthaŵi ina Amaziya, mfumu ya ku Yuda, adachita upo. Adatumiza mau kwa Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, mwana wa Yehu, mfumu ya ku Israele, mau omuputa akuti, “Ubwere kuno, udzachione.”
18Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adabweza mau kwa Amaziya, mfumu ya ku Yuda, kuti “Padangotere, mtungwi wa ku Lebanoni udatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amkwatire.’ Koma chilombo cha ku Lebanoni chidadzera pamenepo nkuupondereza mtungwiwo.
19Inde, iwe ukuti wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza nkumadzitamira kupambana kwakoko. Koma ai tsono, khala kwanu komweko. Bwanji ukufuna kuutsa mavuto dala? Bwinotu, ungagwe, iweyo pamodzi ndi anthu a ku Yuda!”
20Koma Amaziya sadasamaleko zimenezi, pakuti ndi Mulungu yemwe adaafuna kuti aŵapereke anthuwo m'manja mwa adani ao, chifukwa chakuti iwowo ankapembedza milungu ya Aedomu.
21Motero Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adapita kukamenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda ku Betesemesi m'dziko la Yuda.
22Anthu a ku Yuda adagonjetsedwa ndi a ku Aisraele, ndipo wankhondo aliyense adathaŵira kwao.
23Tsono ku Betesemesiko Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adagwirako Amaziya mfumu ya ku Yuda, mwana wa Yowasi, mdzukulu wa Ahaziya, nabwera naye ku Yerusalemu. Ndipo Yehowasi adagumula khoma la Yerusalemu mamita 200, kuyambira ku chipata cha Efuremu mpaka ku chipata Chapangodya.
24Pamenepo adalanda golide ndi siliva yense ndi ziŵiya zonse zimene adazipeza m'Nyumba ya Chauta zosungidwa ndi Obededomu. Adatenganso chuma cha ku nyumba ya mfumu, nkugwira anthu ena ngati chikole, nabwerera ku Samariya.
25Amaziya mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, adakhala moyo zaka 15 atafa Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, mfumu ya ku Israele.
26Tsono ntchito zonse za Amaziya kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele.
27Kuyambira nthaŵi imene iye adafulatira Chauta, anthu adamchita chiwembu ku Yerusalemu, iyeyo nkuthaŵira ku Lakisi. Koma adaniwo adatuma anzao kuti amlondole ku Lakisiko, ndipo adakamphera komweko.
28Adamnyamulira pa kavalo, nadzamuika m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.