1Chauta akulankhula ndi wodzozedwa wake Kirusi
amene adamgwira dzanja lamanja,
kuti agonjetse mitundu ina ya anthu,
aŵathe mphamvu mafumu,
ndi kutsekula zitseko kuti zipata zisatsekeke.
2Akunena kuti,
“Ndidzayenda patsogolo pako,
ndi kusalaza zitunda.
Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuŵa,
ndipo ndidzathyolathyola mipiringidzo yake yachitsulo.
3Ndidzakupatsa chuma chosaoneka poyera
ndi katundu wa m'malo obisika.
Motero udzadziŵa kuti ndine Chauta,
Mulungu wa Israele,
amene ndikukuitana pokutchula dzina.
4Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobe,
chifukwa cha wosankhidwa wanga Israele,
ndikukuitana potchula dzina lako,
ndikukupatsa dzina laulemu
ngakhale iwe sukundidziŵa.
5Chauta ndine, palibenso wina,
kupatula ine palibe Mulungu wina.
Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziŵa.
6Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera
kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziŵe
kuti palibe wina koma Ine ndekha.
Chauta ndine, palibenso wina.
7“Ndimalenga kuŵala ndi mdima,
ndimadzetsa madalitso ndi tsoka.
Ndine, Chauta, amene ndimachita zonsezi.
8“Gwetsa mvula, iwe thambo, kuchokera kumwamba,
mitambo ikhuthule chilungamo chopulumutsa.
Dziko lapansi litsekuke kuti patuluke chipulumutso,
kuti chilungamo chimerepo.
Ndine, Chauta, amene ndidalenga zimenezi.”
Chauta, Mlengi ndi Muwongoleri wa zonse9 Yes. 29.16; Aro. 9.20 Tsoka kwa amene amakangana ndi mlengi wake,
ngakhale ali ngati phale chabe
pakati pa mapale anzake.
Kodi mtapo ungafunse munthu woumba kuti,
“Kodi ukuumba chiyani?”
Kapena kunena kuti,
“Woumbawe, ulibe luso!”
10Tsoka kwa wofunsa bambo wake kuti,
“Mwabereka chiyani,”
kapena mai wake kuti,
“Mwabala chiyani?”
11Chauta, Woyera uja wa Israele
ndiponso Mlengi wake, akunena kuti,
“Kodi iwe ungandifunse za ana anga,
kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
12Ndine amene ndidalenga dziko lapansi
ndi kulenga munthu kuti akhalemo.
Ndidayalika zakuthambo ndi manja anga,
ndipo tsopano ndimalamulira gulu lonse lamumlengalenga.
13Ndine amene ndidautsa Kirusi kuti
chilungamo chichitike.
Ndidzaongola mseu uliwonse umene adzadzeramo.
Adzamanganso mzinda wanga wa Yerusalemu
ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,
osapereka ndalama kapena mphotho,”
watero Chauta Mphambe.
14Chauta akuuza Aisraele kuti,
“Chuma cha ku Ejipito ndi malonda a ku Etiopiya
zidzakhala zanu.
Anthu a ku Saba, a msinkhu aatali,
adzabwera kwa inu ndi kukhala akapolo
anu ndipo azidzakutsatani.
Adzabwera ali omangidwa ndi maunyolo,
ndi kukugwadirani.
Adzakupembani ndi kunena kuti,
‘Mulungu ali ndi inu nokha,
palibenso wina ai.
Kupatula Iyeyo palibe mulungu wina.
15Ndithu inu muli ndi Mulungu wobisika,
amene ali Mulungu wa Israele ndiponso Mpulumutsi.
16Onse amene amapanga mafano,
adzaŵachititsa manyazi ndi kunyozetsa,
adzamwazikana atasokonezeka.
17Koma Israele amampulumutsa ndi Chauta,
ndipo chipulumutso chake chidzakhalapo mpaka muyaya,
Anthu ake sadzaŵachititsa manyazi konse,
sadzakhala onyozeka konse.’ ”
18Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba,
ndi Iyeyo Mulungu
amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi,
ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu.
Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu,
koma kuti likhale malo okhalamo anthu.
Iyeyo akunena kuti:
“Chauta ndine, palibenso wina ai.
19Sindidalankhule mwachinsinsi
pa malo ena m'dziko lamdima.
Sindidauze zidzukulu za Yakobe
kuti zizindifunafuna kumene kuli kopanda kanthu.
Ine Chauta ndimalankhula zoona,
ndimanena zolungama.”
Chauta ndi Mulungu wa onse20Chauta akuti,
“Musonkhane pamodzi ndipo mubwere.
Musendere pafupi, inu nonse amene mudapulumuka
kwa anthu a mitundu ina!
Ndi opanda nzeru amene amanyamula mafano amitengo,
namapemphera kwa milungu imene singathe kuŵapulumutsa.
21Kambani, fotokozani mlandu wanu.
Mupatsane nzeru nonse pamodzi.
Kodi ndani adaneneratu zimene zidzachitika?
Ndani adaloseratu kalekale zimenezo?
Kodi si Ineyo, Chautane?
Ndithu, kupatula Ine palibe Mulungu wina,
Mulungu wachilungamo ndi wopulumutsa.
Palibenso wina aliyense kupatula Ine.”
22“Inu anthu onse a pa dziko lapansi,
tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke.
Paja Ine ndine Mulungu, palibenso wina ai.
23 Aro. 14.11; Afi. 2.10, 11 Ndalumbira dzina langa lomwe,
pakamwa panga palankhula moona
mau amene sadzasinthika konse, akuti,
‘Bondo lililonse lidzandigwadira,
anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.’
24“Pokamba za Ine adzanena kuti,
‘Chilungamo ndiponso mphamvu
zimapezeka mwa Chauta yekha.
Onse amene ankamugalukira adzabwera
kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
25Koma mwa Chautayo zidzukulu zonse
za Israele zidzapambana ndi kupeza ulemerero.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.