Deut. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mose alandiranso malamulo(Eks. 34.1-10)

1Nthaŵi yomweyo Chauta adandiwuzanso kuti, “Semani miyala iŵiri monga yoyamba ija, ndipo upange bokosi lamtengo kuti uziikamo miyalayo, tsono ukwere kuphiri kuno kwa Ine.

2Ndipo pa miyala imeneyi ndidzalembapo zomwe ndidaalemba pa miyala yoyamba udaphwanya ija, tsono ukaike miyala imeneyi m'bokosimo.”

3Pompo ndidapanga bokosi la mtengo wakasiya, ndipo ndidasemanso miyala iŵiri monga yoyamba ija, ndipo ndidakwera phiri, nditatenga miyalayo.

4Pamenepo Chauta adalemba pa miyalayo mau omwewo amene adaalemba pa miyala ija. Mauwo ndiwo malamulo khumi amene adakupatsani pamene adalankhula nanu m'moto muja, pa tsiku limene mudasonkhana nonse kuphiri kuja. Chauta adandipatsa miyalayo,

5ndipo ndidatembenuka ndi kutsika phirilo. Tsono monga momwe Chauta adalamulira, ndidatsekera miyalayo m'bokosi limene ndidaapanga, ndipo ili m'menemo.

6 Num. 20.28; 33.38 (Aisraele adachoka ku Beeroti-Bene-Yaakani, napita ku Mosera. Aroni atamwalira adaikidwa komweko. Mwana wake Eleazara ndiye amene adaloŵa m'malo mwake, kukhala wansembe.

7Kuchokera kumeneko, Aisraele adapita ku Gudigoda napitirira mpaka ku Yotibata, dziko la mtsinje ya madzi ambiri.

8Num. 3.5-8 Nthaŵi imeneyo Chauta adasankha a fuko la Levi, kuti azinyamula Bokosi lachipangano, azikhala pamaso pa Chauta ndi kumatumikira, ndiponso kuti azidalitsa anthu m'dzina la Chauta. Ndiwo amene amachita zimenezi mpaka lero lino.

9Nchifukwa chake fuko la Levi silidalandireko dziko kapena choloŵa monga mafuko ena aja. Chauta ndiye choloŵa chao, monga momwe Chauta, Mulungu wanu, adalonjezera.)

10 Eks. 34.28 Ine ndidakhala paphiripo masiku makumi anai, usana ndi usiku, monga momwe ndidaachitira nthaŵi yoyamba ija. Chauta adandimveranso nthaŵi imeneyi navomera kuti sadzakuwonongani.

11Tsono adandiwuza kuti ndipite nanu, ndikhale mtsogoleri wanu, kuti potero muloŵe ndi kukhazikika m'dziko limene Iye adalumbira kuti adzapatsa makolo anu.

Zimene Chauta afuna

12Tsono inu Aisraele, tamvani zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Akufuna kuti muzimuwopa ndi kuchita zonse zimene amakulamulani. Muzikonda Chauta, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,

13ndipo muzimvera malamulo ndi malangizo onse a Chauta amene ndikukulamulani lero lino, kuti zinthu zikukomereni.

14Kumwamba ndi zonse zili kumeneko ndi zake za Chauta, pamodzi ndi dziko lapansi pano ndi zonse zili m'menemo.

15Komabe Chauta adakonda makolo anu kwambiri, kotero kuti m'malo mwa kusankha anthu ena, adasankha zidzukulu za makolo anuwo, ndiye kuti inuyo, mpaka lero lino.

16Tsono muchotse zoipa m'mitima mwanu, ndipo mulekeretu kukhala ndi mtima wokanika.

171Tim. 6.15; Chiv. 17.14; 19.16; Ntc. 10.34; Aro. 2.11; Aga. 2.6; Aef. 6.9 Pakuti Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wopambana milungu yonse, ndiponso ndi Ambuye oposa ambuye onse. Ndi wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, sakondera, ndipo salandira ziphuphu.

18Mphu. 35.12-15Amateteza ana amasiye ndi akazi amasiye. Amakonda anthu achilendo amene amakhala pakati panu, ndipo amaŵapatsa chakudya ndi zovala zomwe.

19Tsono muŵakonde anthu achilendowo, chifukwa paja inunso mudaali alendo ku Ejipito.

20Muzimvera Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzipembedza Iye yekha. Muzikhala okhulupirika kwa Iyeyo ndipo muzilumbira m'dzina lake lokha.

21Mtamandeni pakuti ndiye Mulungu wanu, ndipo mwadziwonera nokha zinthu zazikulu ndi zoopsa zimene adakuchitirani.

22Gen. 46.27; Gen. 15.5; 22.17 Pamene makolo anu ankapita ku Ejipito, adaalipo makumi asanu ndi aŵiri okha. Koma tsopano Chauta, Mulungu wanu, wakuchulukitsani ngati nyenyezi zamumlengalenga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help