Mphu. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kulemekeza Nzeru

1Nzeru zimadziyamika zokha

ndipo zimadzinyadira pakati pa anthu ake.

2Nzeru zimalankhula pa msonkhano wa Mulungu

Wopambanazonse,

ndipo zimadzinyadira pamaso pa Mulungu

Wamphamvuzonse.

3Zimati, “Ine ndidatuluka m'kamwa mwa Mulungu

Wopambanazonse,

ndidaphimba dziko lapansi ngati nkhungu.

4 Eks. 33.9, 10 Ndinkakhala m'thambo lakumwamba,

chipilala cha mtambo ndiye chinali mpando wanga

waufumu.

5Ndekhandekha ndidazungulira mlengalenga,

ndipo ndidayenda m'maphompho ozama.

6Ndinkalamulira mafunde a pa nyanja,

ndiponso dziko lapansi,

ndinkalamuliranso anthu a mitundu yosiyanasiyana.

7Monsemo ndidafunafuna popumulira.

8Pamenepo Mlengi wa zinthu zonse,

adandipatsa malangizo,

Iye amene adandilenga ine

adandilozera pomanga hema langa.

Adati, ‘Kakhale m'dziko la Yakobe,

Aisraele akakhale anthu ako.’

9Adandilenga poyambayamba ndithu nthaŵi

isanayambike,

ndipo ndidzakhalapo mpaka muyaya.

10Ndinkamutumikira m'chihema choyera chija,

motero ndidakhazikika m'Ziyoni.

11Tsono adandikhazika mu mzinda

umene ankaukonda,

nkundipatsa ulamuliro mu Yerusalemu.

12Ndidakhazikika pakati pa anthu olemekezeka,

m'chigawo cha Ambuye amene ndi choloŵa chao.

13Kumeneko ndidakula

ngati mkungudza wa ku Lebanoni,

ngati mtengo wa paini wa ku Heremoni.

14Ndidakula ngati mgwalangwa wa ku Engedi

ndipo ngati zitsamba za maluŵa a roza a ku Yeriko.

Ndidakula ngati mtengo wa olivi m'chigwa,

ndidatalika ngati mtengo wamba wookedwa m'mbali mwa mtsinje.

15Ndinkanunkhira bwino ngati mtengo wa kasiya

ndi wa sinamoni.

Fungo langa linkafalikira ngati mure wabwino,

ndiponso ngati zonunkhira za galbanumu, onika ndi stakite.

Ndinali ngati utsi wa lubani wonunkhira bwino

m'chihema choyera chija.

16Ndinkatambalitsa nthambi zanga ngati mtengo wa mbwemba

ndipo nthambi zangazo zinali zokhwima ndi zokongola.

17Ndinkaphukira bwino ngati mpesa,

ndipo maluŵa anga ankabereka zipatso zokoma ndi zochuluka.

18Ine ndine mai wake wa chikondi chokoma,

wa kuwopa, wa nzeru ndi wa chikhulupiriro.

Poti ndine wamuyaya, amandipereka kwa ana onse

amene Mulungu adaŵasankha.

19Bwerani kwa ine inu amene mumakhumbira ine,

dzadyeni zipatso zanga mpaka kukhuta.

20Kukumbukira ine kumakoma koposa kutsekemera kwa uchi,

kukhala ndi ine kumakoma koposa chisa cha uchi.

21Munthu wodya ine adzalakalaka kwambiri kundidyanso.

Munthu womwa ine adzalakalaka kwambiri kundimwanso.

22Munthu womvera Ine sadzagwa m'mavuto,

ndipo otsata zimene ine ndimafuna sadzachimwa.”

Za nzeru ndi Malamulo

23Zonsezi ndi Buku la Chipangano

cha Mulungu Wopambanazonse,

Malamulo amene Mose adapereka,

kuti akhale choloŵa cha magulu a Yakobe.

24Musaleke kulimbika mwa Ambuye,

muphathane nawo kuti akulimbitseni.

Ambuye amphamvuzonse Iwo okha ndiwo Mulungu,

palibenso mpulumutsi wina koma Iwo okha.

25Amatumiza nzeru mosefukira ngati mtsinje wa Pishoni,

kapena ngati mtsinje wa Tigrisi pa nyengo ya

zipatso zoyamba.

26Zimasefukira ngati mtsinje wa Yufurate

kapena mtsinje wa Yordani pa nyengo yokolola.

27Amapereka malangizo osefukira ngati mtsinje wa Nailo,

kapena ngati Gihoni pa nyengo yothyola mphesa.

28Monga amene adayamba kuphunzira za nzeru

sangazimvetse kotheratu,

momwemonso wotsirizira sangazindikire

kuzama kwake.

29Paja maganizo ake ndi aakulu

kupambana nyanja,

ndipo zolinga zake

ndi zozama kupambana phompho lakuya.

30Ine ndakhala ngati ngalande

yotenga madzi amumtsinje,

ngati njira ya madzi yokaloŵa m'dimba.

31Ndidati, “Ndikukathirira munda wanga wa zipatso,

ndikukathirira maluŵa anga.”

Koma mwadzidzidzi ngalande yanga idasanduka mtsinje,

ndipo mtsinje wanga udasanduka nyanja.

32Ndidzaphunzitsanso mwambo wanga

kuti uŵale ngati mbandakucha,

kuŵala kwake kuwoneke patali.

33Ndidzalalikanso maphunzitso a Mulungu ngati zolosa,

ndi kuŵasiyira mibadwo yakutsogolo.

34Zoonadi, sindidadzigwirire ntchito ine ndekha,

komanso ena onse amene amafunafuna nzeru.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help