1 Yos. 1.1—11.23 Yoswa, mwana wa Nuni, anali ngwazi yankhondo,
ndiye amene adaloŵa m'malo mwa Mose pa ntchito
ya uneneri.
Potsata tanthauzo la dzina lake,
adasanduka wotchuka pa ntchito yopulumutsa
osankhidwa a Ambuye.
Adagonjetsa adani amene ankaŵathira nkhondo,
ndi kupatsa Aisraele dziko laolao.
2Anthu ankachita chidwi poona m'mene ankakwezera manja ake,
ndi m'mene ankasamulira lupanga lake
pochita nkhondo ndi mizinda.
3Nkale lonse ndani adaonetsa kulimba mtima ngati kwa iyeyu?
Pajatu ndiye amene ankamenya nkhondo za Ambuye.
4Kodi suja adaaimitsa dzuŵa
mpaka tsiku limodzi lidaatalika ngati masiku aŵiri?
5Adapemphera Mphambe Wopambanazonse
pamene adani ankampanikiza ku mbali zonse,
ndipo Ambuye amphamvu adayankha pemphero lake
pogwetsa matalala oopsa.
6Adakantha anthu a dzikolo
ndipo adaonongeratu adani ake pa Matsitso paja,
kuti mitundu ya anthu adziŵe mphamvu ya zida zake,
poti iye ankamenyera nkhondo Ambuye,
ndipo ankamvera Wamphamvu uja kotheratu.
Kalebe7 Num. 14.6-10; 11.21; Yos. 14.6-11 Pa nthaŵi ya Mose, Yoswa uja ndi Kalebe, mwana wa Yefune,
adakhala okhulupirika polimbana ndi gulu lonse.
Adaletsa anthu kuti angachimwe
nathetsa kudandaula kwao.
8Mwa anthu oyenda pansi 600,000 aŵiri
okhawo ndiwo adapulumuka,
nakaloŵa m'dziko laolao, dziko lamwanaalirenji.
9Ambuye adampatsa nyonga Kalebe,
ndipo iye adakhala nazo mpaka nthaŵi ya
ukalamba wake.
Adakwera m'dziko lamapiri,
nalilanda kuti likhale la zidzukulu zake.
10Tsono Aisraele onse adaona
kuti ndi chinthu chabwino kutsata Ambuye mokhulupirika.
Aweruzi11 Owe. 1.1—16.31 Panalinso aweruzi, aliyense wotchuka pa yekha.
Onsewo adakana kupembedza mafano,
ndipo sadapandukire Ambuye.
Aŵakumbukire moŵalemekeza.
12Mafupa ao apeze moyo watsopano
kuchokera kumanda kumene akugona,
ndipo mbiri ya kutchuka kwao ibukenso mwa adzukulu ao.
Samuele13 1Sam. 3.19, 20; 7.9-11; 10.1; 12.3; 16.13; 28.18, 19 Ambuye adakonda kwambiri Samuele.
Ali mneneri wa Ambuye, adakhazikitsa ufumu,
ndipo adadzoza olamulira anthu ake.
14Nthaŵi zonse adaweruza anthu potsata
Malamulo a Ambuye,
ndipo Ambuyewo adasunga bwino Yakobe.
15Poti Samuele adakhala wokhulupirika,
adaoneka kuti anali mneneri weniweni.
Pa mau ake anthu adazindikira kuti analidi
mneneri woona.
16Adapemphera Ambuye Amphamvuzonse,
pamene adani ankampanikiza ku mbali zonse,
ndipo adapereka nsembe ya mwanawankhosa.
17Pamenepo mau a Ambuye adagunda kumwamba
ngati bingu,
adamveka ndi phokoso lalikulu.
18Adaononga atsogoleri a adani
ndiponso atsogoleri onse a Afilisti.
19Samuele asanakapumule kwamuyaya,
adachita umboni pamaso pa Ambuye ndi pa
wodzozedwa wake kuti,
“Sindidatengepo chinthu cha munthu wina,
ngakhale nsapato,”
ndipo palibe amene adamtsutsa.
20Ngakhale atafa, adalosabe
nachenjeza mfumu Saulo za imfa yake.
Ali m'manda adalankhula mau olosa
kuti machimo a anthu ake afafanizike.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.