1 Am. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Simoni adamva kuti Trifone wasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo, kuti aloŵe ndi kuthira nkhondo dziko la Yudeya.

2Adaona kuti anthu akuchita mantha ndi kuda nkhaŵa, choncho adakwera ku Yerusalemu, nakasonkhanitsa anthu.

3Adaŵalangiza kuti, “Mukudziŵa zonse zimene ine ndi abale anga tidachita chifukwa cha Malamulo ndi Nyumba yathu yopembedzeramo. Mukudziŵa nkhondo ndi zovuta zimene tidapirira.

4Nkuwona abale anga onse adafera Israele, mwakuti ineyo ndatsala ndekha.

5Tsopano ine sindiganiza kupulumutsa moyo wanga pa nthaŵi yovutayi, chifukwa sindili wabwino kupambana abale anga.

6Koma ndidzalipsira chifukwa cha zoipa zimene zidachitikira anthu a mtundu wathu, Nyumba yathu yopempheramo, ndiponso akazi athu ndi ana athu, pakuti anthu onse a mitundu ina asonkhana kuti atiwononge chifukwa chodana nafe.”

7Mitima ya anthuwo idalimbika pakumva mauwo.

8Motero adayankha ndi mau aakulu kuti, “Mtsogoleri wathu ndinu basi m'malo mwa Yudasi ndi mbale wanu uja Yonatani.

9Muzitimenyera nkhondo zathu, ndipo zonse zimene mudzanene tidzazichita.”

10Tsono Simoni adasonkhanitsa ankhondo onse. Adafulumira kutsiriza kumanga malinga a Yerusalemu, naŵalimbitsa ponseponse.

11Pambuyo pake adatuma Yonatani, mwana wa Abisalomu, ku Yopa, pamodzi ndi gulu lankhondo lamphamvu. Iyeyo adapirikitsa asilikali am'menemo, nakhala mumzindamo.

Simoni apirikitsa Trifone

12Trifone adachoka ku Ptolemaisi pamodzi ndi ankhondo ake ochuluka, kuti akathire nkhondo dziko la Yudeya. Adatenga Yonatani ali kaidi womangidwa.

13Simoni adadzamanga zithando zake ku Adida kuyang'anana ndi ku chigwa.

14Trifone adamva kuti Simoni ndiye mtsogoleri m'malo mwa mbale wake Yonatani, ndipo kuti ali pafupi kuyambana naye nkhondo. Tsono adamtumira amithenga kukamuuza kuti,

15“Mbale wako Yonatani tidammanga chifukwa sadapereke ku bokosi la mfumu ndalama zimene adaazipeza pogwira ntchito zake.

16Ndiye iwe utumize tsopano pompano makilogramu 3,000 a siliva, pamodzi ndi ana ake aŵiri ngati zigwiriro, kuti titsimikize kuti sadzatiputanso. Mukatero tidzammasuladi.”

17Simoni adaamvetsa bwino kuti mauwo ngonama. Komabe adaitanitsa ndalama ndi ana aŵiriwo, kuwopa kuti anthu angadane naye, nkumanena kuti,

18“Yonatani wafa chifukwa Simoni sadatumize ndalamazo ndi anawo.”

19Motero adatumiza ana aŵiriwo ndi makilogramu 3,000 aja. Koma Trifone adaphwanya lonjezo lake, sadammasule Yonatani.

20Zitatero, Trifone adasendera kuti athire nkhondo dzikolo ndi kuliwononga. Adayenda mozungulira, nadzera mseu wa ku Adora. Koma Simoni ndi ankhondo ake ankayenda moyang'anana nawo konse kumene ankapitako.

21Ankhondo aja okhala m'boma lankhondo la ku Yerusalemu, adaamutumira amithenga Trifone kumuuza kuti afulumire kubwera podzera njira yakuchipululu, ndipo kuti aŵatumizire chakudya.

22Trifone adakonzera ankhondo ake okwera pa akavalo kuti akafikeko, koma usiku womwewo kudagwa chisanu chambee chambiri zedi, mwakuti sadathe kupitako chifukwa cha chisanu chambeecho. Tsono adachokako napita cha ku Giliyadi.

Trifone apha Yonatani

23Atafika pafupi ndi Baskama, Trifone adapha Yonatani, namuika komweko.

24Kenaka adachoka nabwerera ku dziko lake.

25Tsono Simoni adatuma anthu kuti akatenge mafupa a mbale wake Yonatani, ndipo adaŵaika ku Modini, mzinda wa makolo ake.

26Aisraele onse anali ndi chisoni chachikulu ndipo adalira masiku ambiri.

27Pa manda a makolo ake ndi a abale ake Simoni adamanga chiliza chachitali ndi chooneka kutali, cha miyala yochezimira kutsogolo ndi kumbuyo kwake.

28Adaimiritsanso miyala isanu ndi iŵiri yoyang'anana, wina wa atate ake, wina wa amai ake, ndi ina ya abale ake anai.

29Adaizinga ndi zipilala zazitali. Pazipilalapo adaikapo zithunzi za zida, ngati chikumbutso chosatha. Pafupi ndi zidazo adaikanso zithunzi za zombo, kuti ndi anthu oyenda pa nyanja omwe aziziwona.

30Ndimo m'mene Simoni adamangira chiliza ku Modini, ndipo chikalipobe mpaka lero.

Mfumu Demetriyo ayanjananso ndi Ayuda

31Trifone adachenjereranso Antioko, mfumu yachinyamata ija namupha.

32Adakhala mfumu m'malo mwake, namavala chisoti cha ufumu wa ku Asiya, ndipo adalizunza kwambiri dziko lonse.

33Simoni adamanganso malinga ankhondo ku Yudeya, naikamo nsanja zazitali ndi makoma aatali ndi zitseko za mipiringidzo, nkuikamo zakudya.

34Kenaka adasankhula anthu, naŵatuma kwa mfumu Demetriyo kukapempha kuti aŵakhululukire Ayuda misonkho yao, chifukwa cha machitidwe a Trifone amene adakhala akungolanda zinthu.

35Mfumu Demetriyo adamlembera kalata yomuyankha motere:

36“Ndine mfumu Demetriyo, ndikupereka moni kwa inu Simoni, mkulu wa ansembe ndi bwenzi la mafumu, ndiponso kwa akuluakulu ndi kwa mtundu wonse wa Ayuda.

37Talandira mokondwera chisoti chaufumu chagolide ndi nthambi yagolide yakanjedza, zimene mwatitumizira. Tsono tikufuna kupangana nanu za mtendere weniweni ndi kulembera akapitao athu kuti akukhululukireni misonkho.

38Zonse zimene tidapangana nanu, ndi zolimba ndithu. Malinga ankhondo amene mudaŵamanga akhale anu.

39Tikukukhululukirani zolakwa zanu zonse zimene mwakhala mukuchita mpaka lero, ndiponso ndalama zagolide zimene mukadayenera kutipatsa. Ngati ankakhometsa misonkho inanso ku Yerusalemu, aleke.

40Ngati ena mwa inu ngoyenera kuŵalemba m'gulu lathu la ankhondo, aŵalembe, ndipo mtendere ukhale pakati pa ife.”

41Choncho chaka cha 170, Aisraele adamasuka ku ulamuliro wa anthu a mitundu ina.

42Ndipo anthu adayamba kulemba m'makalata ndi m'mapepala a zipangano zao mau onena kuti, “Chaka choyamba cha Simoni, amene ali mkulu wa ansembe, mkulu wa ankhondo ndi mtsogoleri wa Ayuda.”

Simoni alanda Gazara

43 2Am. 10.32-38 Pa masiku amenewo Simoni adakamanga zithando zake zankhondo pafupi ndi mzinda wa Gazara nauzinga ndi ankhondo ake. Adapanga makina aakulu ankhondo, nabwera nawo pafupi ndi mzinda. Adagumula nawo nsanja yankhondo, nailanda.

44Okhala m'makinamo adalumphira mu mzinda, nasokoneza mzinda wonse.

45Amuna okhala mumzindamo, akazi ao ndi ana ao, adakwera pa malinga, nang'amba zovala zao ndi kupempha Simoni mokweza mau kuti achite nawo mtendere.

46Adapempha kuti, “Musatichitire chilichonse poyang'anira kuipa kwathu, koma potsata chifundo chanu.”

47Pamenepo Simoni adakhululuka, naleka kuchita nawo nkhondo. Koma adachotsa anthu amumzindamo, nayeretsa m'nyumba m'mene munali mafano. Adaloŵa mumzindamo ndi anthu ake akuimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza.

48Atachotsa zoipa zonse mumzindamo, adaikamo anthu otsata Malamulo. Kenaka adaulimbitsa, nadzimangira nyumba yake momwemo.

49Anthu aja okhala m'boma lankhondo la ku Yerusalemu ankasauka kwambiri ndi njala. Ena mwa iwo adafa, chifukwa sankatha kutuluka kupita m'dziko kuti akachite malonda aliwonse.

50Tsono adapempha Simoni ndi mau olira kuti achite nawo mtendere, iyeyo nkuvomera. Koma adaŵatulutsa m'boma, naliyeretsa bomalo pochotsamo zoipa zake.

51Ayuda adaloŵamo pa tsiku la 23 la mwezi wachiŵiri wa chaka cha 171. Adaloŵa akuimba nyimbo zoyamika, nthambi zakanjedza zili m'manja. Ankaliza azeze, ziwaya zamalipenga ndi nsansi, akuimba nyimbo zachimwemwe chifukwa anali atachotsa mdani wamkulu m'dziko la Israele.

52Simoni adalamula kuti tsikulo azidzalikumbukira chaka chilichonse ndi chisangalalo. Adalimbitsa linga la ku phiri kumene kunali Nyumba ya Mulungu, kuyang'anana ndi boma lija lankhondo, nakhala kumeneko iye ndi anthu ake.

53Tsono Simoni ataona kuti mwana wake Yohane wakula, adamupatsa mphamvu zolamulira ankhondo onse. Yohaneyo ankakhala ku Gazara.

Simoni alamulira dziko lake bwino
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help