1 Mt. 3.17; 17.5; Mk. 1.11; Lk. 3.22; 9.35 Mt. 12.18-21 Chauta akuti,
“Nayu mtumiki wanga amene ndimamchirikiza,
amene ndamsankhula, amene ndimakondwera naye.
Ndaika Mzimu wanga mwa iyeyo,
ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
2Sadzafuula kapena kukweza mau,
mau ake sadzamveka mu mseu.
3Bango lopindika sadzalithyola,
moto wozilala sadzauzima.
Adzabweretsa chilungamo mokhulupirika.
4Sadzafookera kapena kutaya mtima,
mpaka atakhazikitsa chilungamocho pa dziko lapansi.
Maiko akutali akuyembekeza malamulo ake.”
5 Ntc. 17.24, 25 Mulungu, Chauta,
adalenga zakuthambo ndi kuziyalika.
Adalenga dziko lapansi ndi zonse zimene limabereka.
Adapatsa mpweya kwa anthu okhala m'dzikomo,
ndi kuninkha moyo kwa onse oyendamo.
Iyeyo akunena kuti,
6 Yes. 49.6; Lk. 2.32; Ntc. 13.47; 26.23 “Ine Chauta ndakuitana
kuti ukhazikitse chilungamo.
Ndakugwira padzanja ndi kukusunga.
Ndakusankhula kuti ukhale chipangano kwa anthu,
ukhale kuŵala kounikira anthu a mitundu ina.
7Udzaŵatsekula maso anthu akhungu,
udzamasula akaidi m'ndende,
udzatulutsa m'ndende anthu okhala mu mdima.
8Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo.
Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense.
Mayamiko oyenera Ine,
sindidzalola kuti mafano alandireko.
9Zinthu zimene ndidalosa zija zachitikadi.
Tsono ndikuuzani zinthu zatsopano,
zisanaoneke ndikukudziŵitsiranitu.”
Nyimbo yotamanda10Imbirani Chauta nyimbo yatsopano.
Mtamandeni, inu okhala m'dziko lonse lapansi!
Mtamandeni, inu zolengedwa zonse zam'nyanja.
Imbani, inu maiko akutali ndi onse okhala kumeneko.
11Chipululu ndi mizinda yake zitamande Mulungu.
Midzi ya Akedara imuyamike.
Okhala mu mzinda wa Sela amuimbire mokondwa,
afuule pa nsonga za mapiri.
12Atamande Chauta, ndipo alalike
ulemu wake ku maiko akutali.
13Chauta akupita ku nkhondo ngati ngwazi,
akuutsa ukali wake ngati munthu wankhondo.
Akukuŵa, akufuula mfuu zankhondo.
Akuwonetsa mphamvu zake pakuposa adani ake.
Mulungu alonjeza kuthandiza anthu ake14Mulungu akuti,
“Ndakhala ndili chete pa nthaŵi yaitali,
ndidangoti phee, osachita kanthu.
Koma tsopano ndikubuula ngati mkazi
pa nthaŵi yake yochira,
ndikupuma modukiza ndipo ndili ŵefuŵefu.
15Ndidzaononga mapiri ndi magomo,
ndidzaumitsa udzu ndi mitengo yonse kumeneko.
Ndidzasandutsa mitsinje kuti ikhale zilumba,
ndipo ndidzaumitsa maiŵe.
16Ndidzatsogolera anthu akhungu
m'miseu imene sadaidziŵe,
ndidzaŵaperekeza pa njira zimene sadadzerepo konse.
Ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwao
kuti ukhale kuŵala,
ndipo ndidzasalaza malo osasalala.
Zimenezi ndidzazichitadi
ndipo sindidzazilekera padera.
17Onse amene akhulupirira mafano,
amene amatchula mafanowo kuti,
‘Ndinu milungu yathu,’ adzatsitsidwa,
ndidzaŵachititsa manyazi kotheratu.”
Aisraele alephera kuphunzira18Chauta akuti, “Mverani, agonthi inu!
Muyang'ane ndipo mupenye, akhungu inu!
19Kodi ndani ali wakhungu osakhala mtumiki wanga?
Ndani ali gonthi ngati wamthenga amene ndikumtuma?
Kodi ndani ali wakhungu ngati wokhulupirika wanga?
Ndani ali gonthi ngati mtumiki wa Chauta?
20Iwe waona zambiri, koma zonsezo sudazisamale.
Makutu ako ndi otsekuka, koma suumva.”
21Chifukwa cha chilungamo chake,
Chauta adafunitsitsa kuti malamulo ake
akhale opambana ndi aulemu.
22Koma tsono anthu ameneŵa aŵalanda
ndi kuŵafunkhira zinthu zao.
Onseŵa adaŵakola m'mbuna,
ndi kuŵabisa m'ndende.
Adaŵafunkhira, popanda wina woŵapulumutsa,
adaŵabera, popanda wina wonena kuti, “Bwezani!”
23Kodi alipo wina mwa inu
amene adzamvetsere zimenezi?
Ndani adzatchere khutu ndi kuzisamala kutsogolo kuno?
24Ndani adapereka Yakobe kwa ofunkha?
Ndani adapereka Israele kwa anthu akuba?
Kodi akuchita zimenezi si Chauta?
Paja tidamchimwira, sitidatsate njira zake,
ndipo sitidamvere malamulo ake.
25Motero adatikwiyira kwambiri,
nativutitsa ndi nkhondo.
Adayatsa moto ponseponse potizungulira,
ife osamvetsa.
Moto udatipsereza,
koma ife osapezapo phunziro ai.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.