1Ku dziko lamapiri la Efuremu kunali munthu wina dzina lake Mika.
2Iyeyu adauza mai wake kuti, “Pamene munthu adaakuberani ndalama zasiliva 1,100, inu mudaamutemberera wakubayo, matembererowo ine ndidaŵamva. Ndalamazo ndi izi, zili ndi ine. Ndine ndidaatenga.” Mai wakeyo adamuuza kuti, “Chauta akudalitse mwana wanga.”
3Tsono iye adabwezera ndalama zonse kwa mai wake, ndipo maiyo pofuna kuchotsa temberero lija, adati, “Ndikuzipatula ndalama zasilivazi kuti zikhale za Chauta. Ndidzazipereka kuti aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Choncho ndikubwezera ndalamazo.”
4Tsono Mika atabweza ndalamazo kwa mai wake, mai wakeyo adatengapo ndalama zasiliva 200 nazipereka kwa mmisiri wosula siliva. Munthuyo adasema fano nasungunula ndalamazo, nakutira fanolo ndi siliva. Ndipo Mika adaliimika m'nyumba mwake.
5Mikayo anali ndi kachisi wakewake, ndipo adapanga chovala chaunsembe cha efodi ndiponso mafano am'nyumba otchedwa terafimu, nakhazika mmodzi mwa ana ake kuti akhale wansembe wake.
6Owe. 21.25Masiku amenewo ku Israele kunalibe mfumu. Munthu aliyense ankangochita zimene zinkamkomera.
7Ku Betelehemu m'dziko la Yuda kunali mnyamata wina wa fuko la Yuda amene anali Mlevi.
8Munthuyo adachoka ku mudzi wa Betelehemu uja ku Yuda, kukafunafuna kwina kokakhala. Akuyenda ulendo wakewo adakafika ku dziko lamapiri la ku Efuremu ku nyumba ya Mika.
9Mika uja adamufunsa kuti, “Kodi inu kwanu nkuti?” Munthuyo adayankha kuti, “Ine ndine Mlevi wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda, ndikufunafuna koti ndikhale nao.”
10Apo Mika adamuuza kuti, “Khalani ndi ine, mukhale mlangizi wanga ndi wansembe wanga, ine ndizikupatsani ndalama zasiliva khumi pa chaka, ndizikupatsaninso zovala ndi zakudya.”
11Mleviyo adavomera kukhala naye munthuyo, ndipo adasanduka ngati mmodzi mwa ana ake.
12Tsono Mika adalonga Mleviyo unsembe, ndipo iyeyo ankakhala m'nyumba mwa Mika.
13Apo Mika adati, “Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta adzandilemeza, popeza kuti Mleviyu ndiye wansembe wanga.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.