1Davide adati, “Pano ndipo pamene padzakhale Nyumba ya Mulungu, ndiponso pano mpamene padzakhale guwa la nsembe zopsereza zimene Aisraele azidzapereka.”
Davide akonzeratu zomangira Nyumba ya Chauta2Davide adalamula kuti asonkhanitse alendo amene anali m'dziko la Israele. Tsono pakati pao adasankhula anthu oti aseme miyala yomangira Nyumba ya Chauta.
3Davide adaperekanso zitsulo zochuluka zopangira misumali ya zitseko zapamakomo ndi nsimbi zomangira. Adaperekanso mkuŵa wochuluka, wokanika kuuyesa.
4Adaperekanso matabwa osaŵerengeka a mtengo wa mkungudza, chifukwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Tiro adaabwera ndi mikungudza yambiri kwa Davide.
5Davide ankati, “Mwana wanga Solomoni akali wamng'ono, wosadziŵa zinthu, ndipo nyumba imene akudzamangira Chauta iyenera kukhala nyumba yaulemerero kwambiri, yomveka ndiponso yoyenera kuichitira ulemu anthu a ku maiko onse. Nchifukwa chake ine ndikuti ndikonzeretu zambiri.” Motero Davide adapezeratu zipangizo zambiri asanamwalire.
6Tsono adaitana Solomoni mwana wake, ndipo adamlamula kuti amangire nyumba Chauta, Mulungu wa Israele.
72Sam. 7.1-16; 1Mbi. 17.1-14 Davide adauza Solomoni kuti, “Mwana wanga, ine ndinkaganiza zakuti ndimangire nyumba Chauta, Mulungu wanga.
8Koma Chauta adandiwuza kuti, ‘Iwe udapha anthu ambiri ndipo udamenya nkhondo zikuluzikulu. Chifukwa cha zimenezi, sindiwe amene udzandimangire nyumba ai.
9Udzabereka mwana wamwamuna. Iyeyo adzakhala munthu wamtendere. Ine ndidzamkhalitsa mwamtendere pakati pa adani ake onse omzungulira. Dzina lake adzatchedwa Solomoni, popeza kuti ndidzabweretsa bata ndi mtendere m'dziko lonse la Israele pa moyo wake wonse.
10Iyeyo ndiye adzandimangire nyumba. Adzakhala mwana wanga, Ine ndidzakhala bambo wake, ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake waufumu m'dziko la Israele mpaka muyaya.’ ”
11Davide adaonjeza kuti, “Tsono mwana wanga, Chauta Mulungu wako akhale nawe, kuti udzathe kummangira nyumba monga m'mene wanenera.
12Komabe Chauta akuninkhe nzeru ndi luntha, kuti akadzakupatsa ulamuliro woyang'anira Israele, udzasunge malamulo a Chauta Mulungu wako.
13Yos. 1.6-9 Ukadzamvera mosamala malamulo ndi malangizo amene Chauta adalamula Mose kuti auze Aisraele, ndiye kuti zinthu zidzakuyendera bwino. Khala wamphamvu, limba mtima, usati uziwopa, usatinso ude nkhaŵa.
14Movutikira kwambiri ine ndaperekera Nyumba ya Chauta matani 3,400 a golide, matani 34,000 a siliva, ndiponso mkuŵa ndi chitsulo zosadziŵika kulemera kwake, poti zinali zochuluka kwambiri. Ndasonkhanitsanso matabwa ndi miyala. Pa zimenezi uwonjezeponso.
15Uli nawo anthu antchito ambirimbiri: amisiri a miyala, amisiri a matabwa, ndiponso anthu a nzeru zosiyanasiyana osaŵerengeka, aluso pa ntchito zao
16za golide, siliva, mkuŵa ndiponso chitsulo. Tiyeko uyambepo ntchito zimenezo. Chauta akhale nawe.”
17Davide adalamulanso atsogoleri onse a ku Israele kuti azithandizana ndi Solomoni mwana wake, adati,
18“Pajatu Chauta Mulungu wanu ali nanu, ndipo adakupatsani mtendere ku mbali zonse. Iye wapereka kwa ine nzika zonse zam'dzikomu, mwakuti zagonjera Chauta ndi inu anthu ake.
19Tsono ikani nzeru zanu ndi mtima wanu pa kutumikira Chauta Mulungu wanu. Muyambepo tsopano kumanga Nyumba ya Chauta kuti muikemo Bokosi lachipangano la Chauta ndiponso ziŵiya zonse zofunikira pa chipembedzo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.