1 Mbi. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zidzukulu za Rubeni

1 ija.

Adzukulu a Manase akuvuma

23Theka la fuko la Manase linkakhala m'dziko lakuvuma kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Heremoni, Seniri ndiponso ku phiri la Heremoni. Anthuwo anali ochuluka.

24Atsogoleri a mabanja a makolo ao anali aŵa: Efere, Isi, Eliyele, Aziriele, Yeremiya, Hodaviya ndiponso Yadiyele. Ameneŵa anali ankhondo amphamvu, anthu omveka, atsogoleri a mabanja a makolo ao.

Mafuko akuvuma atengedwa ukapolo

25Koma anthu aja adachimwira Mulungu wa makolo ao, nadzipereka kwa milungu ya anthu am'dzikomo amene Mulungu adaŵaononga iwowo akufika.

262Maf. 15.19; 2Maf. 15.29; 2Maf. 17.6Motero Mulungu wa Israele adautsa mtima wa Pulo mfumu ya ku Asiriya, amene dzina lake lina linali Tigilati-Pilesere, ndipo adaŵatenga Arubeni, Agadi ndiponso theka la fuko la Manase, napita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help