1Aisraele ali ngati mpesa wokondwa
umene unkabala zipatso zambiri.
Chuma chao chikamanka chichuluka,
chipembedzo chachikunja chinkakulirakuliranso.
Dziko lao likamanka litukuka,
iwo ankakometserakometsera mafano ao
amene ankaŵapembedza.
2Mtima wao ndi wonyenga.
Tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo ao.
Chauta adzagumula maguwa ao ansembe,
ndipo adzaononga miyala yao yoimiritsa yachipembedzo.
3Posachedwa anthuwo adzanena kuti,
“Tilibe mfumu tsopano chifukwa sitidamvere Chauta.
Komabe mfumuyo ikadatichitira chiyani ife?”
4Mafumu akungolankhula mau opandapake.
Amangochita zipangano ndi malonjezo abodza.
Chilungamo chasanduka kusalungama
kumene kumaphuka ngati udzu woipa m'munda.
5Anthu a ku Samariya adzachita mantha,
fano la mwanawang'ombe la ku Betehaveni
likadzaonongedwa.
Anthu ake adzalirira.
Nawonso ansembe ake aja adzalira maliro a mulungu waoyo,
chifukwa ulemerero wake wonse wachokeratu.
6Zoonadi, fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya,
kuti likakhale mphatso yoperekedwa kwa mfumu yaikulu.
Aefuremu adzachita manyazi,
Aisraelewo adzachita manyazi
chifukwa cha malangizo onama amene ankamvera.
7Mfumu ya ku Samariya idzatengedwa kunka kutali
ngati kanthambi koyenda pa madzi.
8 Lk. 23.30; Chiv. 6.16 Akachisi opembedzerako milungu yabodza
amene Aisraele ankachimwirako,
idzaonongedwa.
Minga ndi mitungwi zidzamera pa maguwawo.
Anthu adzauza mapiri kuti, “Tigwereni!”
Adzauza magomo kuti, “Tipsinjeni!”
Aisraele adzagonjetsedwa pa nkhondo9 Owe. 19.1-30 Chauta akuti,
“Kuyambira uchimo wa ku Gibea,
Aisraele akhala akuchimwabe.
Motero adzagonjetsedwa pa nkhondo ku Gibea komweko.
10Ndidzabwera kudzalimbana ndi anthu aupanduŵa
kuti ndiŵalange.
Anthu a mitundu ina adzasonkhana kuti aŵathire nkhondo
chifukwa cha uchimo wao waukulu.
11Kale Efuremu anali ngati ng'ombe yophunzitsidwa
imene inkakonda kupuntha tirigu.
Tsopano m'khosi lake lokongola ndaikamo goli,
kuti agwire ntchito koposa.
Ndifuna kuti Yuda azitipula,
Yakobe azimwanya mauma.
12 Yer. 4.3 Mudzifesere m'chilungamo,
ndipo mudzakolola madalitso
a chikondi changa chosasinthika.
Tipulani tsala lanu
pakuti nthaŵi yofunafuna Chauta yakwana.
Funafunani Chautayo
mpaka atabwera kudzakugwetserani mvula ya madalitso.
13Mudabzala zolakwa,
ndipo mudakolola chilango chake.
Mwadya zotsatira zake za mabodza.
Chifukwa choti mwadalira magaleta anu,
ndi kuchuluka kwa anthu anu a nkhondo,
14adani anu adzakuthirani nkhondo.
Malinga anu onse adzaonongedwa
monga momwe Salamani adaonongera Betaribele
pa tsiku la nkhondo.
Adaphwanya azimai pamodzi ndi ana omwe.
15Momwemo zidzakuchitikirani inu a ku Betele
chifukwa cha uchimo wanu waukulu.
Nkhondo ikadzangoyamba m'mamaŵa,
nayonso mfumu ya ku Israele idzaphedwa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.