Ntc. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Petro afotokozera mpingo wa ku Yerusalemu zimene zidachitika

1Atumwi aja, ndiponso abale onse amene anali ku Yudeya, adamva kuti anthu a mitundu ina nawonso alandira mau a Mulungu.

2Tsono pamene Petro adabwera ku Yerusalemu, a m'gulu lolimbikira za kuumbala adatsutsana naye.

3Iwo adati, “Inu mudaloŵa m'nyumba ya anthu osaumbalidwa, nkudya nawo pamodzi.”

4Apo Petro adayamba kuŵafotokozera mwatsatanetsatane zimene zidachitika. Adati,

5“Ine ndinkapemphera m'mudzi wa Yopa. Ndidaachita ngati kukomoka, ndiye ndidaona ngati kutulo chinthu china chikutsika pansi kuchokera kumwamba. Chinkaoneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai, ndipo chidafika pamene panali ineyo.

6Nditachipenyetsetsa, ndidaonamo nyama zoŵeta ndi zakuthengo ndiponso zokwaŵa ndi mbalame zamumlengalenga.

7Tsono ndidamva mau ondiwuza kuti, ‘Petro dzuka, ipha, udye.’

8Koma ine ndidati, ‘Iyai pepani Ambuye, ine ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa sichinaloŵepo pakamwa pangapa.’

9Koma mau ochokera kumwamba aja adanenanso kachiŵiri kuti, ‘Zimene Mulungu waziyeretsa, iwe usati nzosayera.’

10Zimenezi zidachitika katatu, ndipo zonsezo zinatengedwa kupitanso kumwamba.

11Nthaŵi yomweyo kudafika anthu atatu kunyumba kumene ndinkakhala. Adaatumidwa kwa ine kuchokera ku Kesareya.

12Mzimu Woyera anali atandiwuza kuti ndisakayike konse, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi aŵa nawonso adandiperekeza, ndipo tidakaloŵa m'nyumba ya Kornelio.

13Iyeyo adatisimbira za m'mene adaaonera mngelo ataimirira m'nyumba mwake nkumuuza kuti, ‘Tuma anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni, wotchedwa Petro.

14Iyeyo adzakuuza mau amene iwe udzapulumuka nawo, ndiponso onse a m'banja mwako.’

15Tsono pamene ndidayamba kulankhula, Mzimu Woyera adaŵatsikira iwowo, monga momwe adaatitsikiranso ife poyamba paja.

16Ntc. 1.5Pamenepo ndidakumbukira mau aja amene adaalankhula Ambuye akuti, ‘Yohane adabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’

17Tsono ngati Mulungu adaŵapatsa iwowo mphatso yomweyo imene adapatsa ifeyo pamene tidakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, nanga ine ndine yani kuti ndikadatha kumletsa Mulungu?”

18Pamene otsutsana naye aja adamva zimenezi, adaleka mitsutsoyo. Adatamanda Mulungu adati, “Kodi kani! Ndiye kuti Mulungu wapatsadi ndi akunja omwe mwai woti atembenuke mtima ndi kulandira moyo!”

Za mpingo wa ku Antiokeya

19 Ntc. 8.1-4 Okhulupirira Khristu aja, amene anali atabalalikana chifukwa cha mazunzo omwe adabuka pa nkhani ija ya Stefano, adafika mpaka ku Fenisiya, ku Kipro, ndiponso ku Antiokeya. Sankalalika mau kwa munthu wina aliyense, koma kwa Ayuda okha.

20Koma pakati pao panali ena ochokera ku Kipro ndiponso ku Kirene. Ameneŵa adafika ku Antiokeya nayamba kulankhulanso ndi Agriki nkumaŵalalikira Uthenga Wabwino wonena za Ambuye Yesu.

21Ambuye ankaŵalimbikitsa, mwakuti anthu ambiri adakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.

22Mpingo wa ku Yerusalemu utamva zimene zidachitikazo, udatuma Barnabasi ku Antiokeyako.

23Pamene iye adafika kumeneko nkuwona m'mene Mulungu adaŵadalitsira, adakondwa, nalimbikitsa onsewo kuti atsimikize mtima kukhala okhulupirika kwa Ambuye.

24Barnabasiyo anali munthu wolungama, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro. Choncho anthu ambirimbiri adakopeka nadzipereka kwa Ambuye.

25Pamenepo Barnabasi adapita ku Tariso kukafuna Saulo.

26Atampeza, adabwera naye ku Antiokeya. Iwo adakhala pamodzi mu mpingo umenewo chaka chathunthu, naphunzitsa anthu ambirimbiri. Ndi ku Antiokeya kumene ophunzira adayamba kutchedwa Akhristu.

27Masiku amenewo kudafika aneneri ena ku Antiokeya ochokera ku Yerusalemu.

28Ntc. 21.10Mmodzi mwa iwo, dzina lake Agabu, adaimirira, ndipo ndi mphamvu za Mzimu Woyera adalosa kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lapansi. Njalayo idabweradi pa nthaŵi ya Klaudio.

29Pamenepo Akhristu aja adatsimikiza zotumiza thandizo kwa abale okhala ku Yudeya, ndipo kuti aliyense atumize molingana ndi kupata kwake.

30Zimenezi adachitadi, ndipo anatuma Barnabasi ndi Saulo kukapereka thandizolo kwa akulu a mpingo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help