Ntc. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atumiza Paulo ku Roma

1Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa chombo, adampereka Paulo pamodzi ndi akaidi ena kwa mtsogoleri wa asilikali, dzina lake Julio, wa gulu la asilikali lochedwa gulu la Augusto.

2Tidakwera chombo chochokera ku Adramitio chimene chinali chokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tidanyamuka. Aristariko, Mmasedoni wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe.

3M'maŵa mwake tidafika ku Sidoni, ndipo Julio adakomera mtima Paulo, namlola kupita kwa abwenzi ake kuti akamsamale.

4Kuchokera kumeneko tidadzera kumpoto kwa chilumba cha Kipro chifukwa mphepo inkawomba mopenyana nafe.

5Tidawoloka nyanja mbali ya ku Silisiya ndi Pamfiliya nkumafika ku Mira, mzinda wa ku Likiya.

6Kumeneko mtsogoleri wa asilikali uja adapezako chombo chochokera ku Aleksandriya chimene chinkapita ku Italiya, ndipo adatikweza m'chombo chimenechi.

7Tidayenda pang'onopang'ono pa masiku angapo, nkukafika pafupi ndi Kinido movutikira. Tsono popeza kuti mphepo idaativuta zedi, tidalephera kupitirira ulendo wathu molunjika, choncho tidadzera kumwera kwa chilumba cha Krete, titabzola Salimone.

8Tidayenda movutikira m'mbali mwa chilumbacho, nkukafika ku malo ena otchedwa Madooko Okoma, pafupi ndi mzinda wa Lasea.

9Nthaŵi yaikulu idapita, ndipo ngakhale nthaŵi yosala zakudya inali itapita kale. Nthaŵiyo ulendo wapamadzi unali woopsa. Pamenepo Paulo adaŵachenjeza kuti,

10“Abale, ine ndikuwona kuti pa ulendowu zinthu zambiri zidzawonongeka ndi kutayika, osati katundu yekha ndi chombo ai, komanso moyo wathu.”

11Koma mtsogoleri wa asilikali uja adamvera kapitao wa chombo ndiponso mwiniwake wa chombocho, osati mau a Paulo ai.

12Tsono popeza kuti dooko silinali labwino kukhalako pa nthaŵi yachisanu, ambiri mwa iwo adafuna kuchokako, nayesa kuti angathe kukafika ku Fenikisi nkukakhala kumeneko pa nthaŵi yachisanu. Fenikisi linali dooko la ku Krete, loloza kumwera chakumadzulo, ndiponso kumpoto chakumadzulo.

Akomana ndi namondwe pa nyanja

13Mphepo yakumwera itayamba kuwomba monyengerera, anthu aja adayesa kuti tsopano apeza mpata woti achite zimene ankafuna. Motero adanyamuka ulendo, nayenda m'mbali mwa chilumba chija cha Krete.

14Koma posachedwa mphepo yamkuntho, yotchedwa Yurakulo, idayamba kuwomba kuchokera ku mtunda.

15Idaomba chombo chija, ndiye popeza kuti sitidathe kuchiwongolera moyang'anana ndi mphepoyo, tidaigonjera nkungotengedwa nayo.

16Tidafika pafupi ndi kachilumba kotchedwa Kauda, ku mbali yosawombapo mphepo. Kumeneko movutikira tidatha kuwongolera kabwato kokokedwa ndi chombo chija.

17Kenaka adakweza kabwatoko pa chombo, ndipo pambuyo pake adakulunga chombocho ndi zingwe kuti achilimbitse. Tsono poopa kuti angakagunde ku mchenga wa ku Siriti, adatsitsa mathanga nalola kungotengedwa ndi mphepo.

18Popeza kuti tinkavutika naye kwambiri namondweyo, m'maŵa mwake adayamba kutaya katundu m'madzi.

19Ndipo pa tsiku lachitatu lake adataya m'nyanja ndi zipangizo za chombo zomwe.

20Sitidaone dzuŵa kapena nyenyezi masiku ambiri, koma namondwe ankakalipabe, mpaka tonse tidaatayiratu chikhulupiriro chakuti tipulumuka.

Paulo alimbitsa mtima anzake aulendo

21Pa nthaŵi yaitali anthu aja sadadye kanthu. Tsono Paulo adaimirira pakati pao nati, “Abale, mukadamvera zija ndidaanena inezi, osachoka ku Krete, sibwenzi zinthu zitawonongeka nkutayika chotere.

22Koma tsopano ndikukuuzani kuti mulimbe mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene atayike, koma chombo chokha ndiye chiwonongeke.

23Usiku womwe wathawu kunandibwerera mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake, ndipo amene ndimamlemekeza.

24Mngeloyo anandiwuza kuti, ‘Usachite mantha, Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Mfumu ya ku Roma. Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, walola kuti anzako onse aulendo akhale moyo.’

25Ndiye inu, limbani mtima, pakuti ndikukhulupirira Mulungu, kuti zimene wandiwuzazi zidzachitikadi momwemo.

26Koma tidzatsakamira pa chilumba china.”

Ayandikira ku mtunda

27Pakati pa usiku wa khumi ndi chinai, mphepo ikutikankhabe pa nyanja ya Adriya, antchito apachombo adaganiza kuti akuyandikira mtunda.

28Tsono atayesa kuzama kwa nyanja, adapeza mamita 37. Atayenda pang'ono, adayesanso napeza mamita 27.

29Poopa kuti chombo chingakatsakamire pa matanthwe, adatsitsira anangula anai m'nyanja kumbuyo kwa chombo. Kenaka ankangoyembekeza molakalaka kuti kuche.

30Antchito apachombo aja ankafuna kuthaŵamo m'chombo muja. Choncho adatsitsira kabwato kaja pa madzi, nachita ngati akufuna kutsitsira anangula m'nyanja kutsogolo kwa chombo.

31Apo Paulo adauza mtsogoleri wa asilikali uja, pamodzi ndi asilikali ake omwe kuti, “Ngati anthu aŵa sakhala m'chombo muno, ndithu inu simutha kupulumuka ai.”

32Pamenepo asilikali aja adadula zingwe za kabwato kaja nakaleka kuti kagwe.

Paulo alimbitsanso anzake aulendo

33Kuli pafupi kucha, Paulo adaŵapempha onse aja kuti adyeko kanthu. Adaŵauza kuti, “Mwakhala masiku khumi ndi anai tsopano mitima ili m'malere, nthaŵi yonseyi osadya kapena kulaŵa kanthu.

34Ndikukupemphani tsono mudye kanthu kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzataye ngakhale tsitsi limodzi la kumutu kwake.”

35Atanena zimenezi, Paulo adatenga buledi, nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo adamnyema bulediyo nayamba kudya.

36Pamenepo onse aja adalimba mtima, iwonso nkuyamba kudya.

37Tonse pamodzi tinali anthu okwanira 276 m'chombomo.

38Onse aja atadya nkukhuta, adapeputsa chombo pakutaya tirigu m'nyanja.

Chombo chiwonongeka

39Kutacha, anthu sadazindikire mtundawo, koma adaona bondo la nyanja lamchenga. Tsono adaganiza kuti ngati nkotheka, akakocheze chombo kumeneko.

40Choncho adataya anangula naŵasiya m'nyanja. Nthaŵi yomweyo adamasula zingwe zomangira nkhafi zoongolera, nakweza thanga lakutsogolo, kuti mphepo ikankhe chombo, ndipo adalunjika ku mtunda.

41Koma chombo chija chidakatsakamira pa mchenga wobisika ndi madzi, ndipo chidaima. Mbali yakutsogolo ya chombocho idajima, kotero kuti sichidathe kuyendanso. Ndipo mbali yakumbuyo idaonongeka ndi mphamvu ya mafunde.

42Asilikali aja adaganiza zakupha akaidi, kuwopa kuti ena mwa iwo angasambire kukafika ku mtunda nkuthaŵa.

43Koma mtsogoleri wa asilikali uja adafuna kupulumutsa Paulo, motero adaŵaletsa. Adalamula kuti onse otha kusambira, adziponye m'madzi, asambire kuti akafike ku mtunda.

44Otsalawo adaŵalamula kuti agwire matabwa kapena zina za chombo choswekacho. Motero onse adapulumuka nakafika kumtunda.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help