1 Aro. 10.20 Chauta adati,
“Ndinali wokonzeka kumva mapemphero
a anthu amene sadandipemphere.
Ndinali wokonzeka kuti andipeze anthu
amene sadandifunefune.
Mtunduwo sudapemphere kwa Ine
ngakhale nthaŵi zonse ndinali wokonzeka
kuŵayankha kuti,
‘Ine ndili pano, ndikuthandizani.’
2 Aro. 10.21 Nthaŵi zonse ndakhala wokonzeka kuŵalandira mwaufulu
anthu ondipandukiraŵa, amene amachita zoipa
namatsata njira zao chifukwa cha kuuma mitu kwao.
3Amandikwiyitsa mopanda manyazi.
Amapereka nsembe zachikunja m'minda,
ndipo amafukiza lubani pa maguwa anjerwa achikunja.
4Amakatandala ku manda,
amachezera kumalo obisika usiku.
Amadya nyama yankhumba,
namamwa msuzi wa nyama zoperekera nsembe zachikunja.
5“Amauza ena kuti,
‘Khalani panokha, osatiyandikira,
chifukwa ndife opatulika.’
Sindingathe kupirira nawo anthu otere.
Ukali wanga pa iwo uli ngati moto wosazima.
6Ndatsimikiza kale za chilango chao,
ndipo mlandu wao ndaulemba kale.
Ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.
7Ndidzaŵalanganso chifukwa cha machimo a makolo ao.
Iwowo afukiza lubani pa mapiri a mafano achikunja,
ndipo andinyoza Ine pa zitunda zao.
Nchifukwa chake ndidzaŵalanga potsata zimene achita.”
8Chauta akuti,
“Pamene madzi adakalimo m'mphesa,
anthu amati,
‘Musaziwononge, zokoma zidakalimo.’
Inenso ndidzaŵatero anthu anga,
sindidzaŵaononga onse.
9M'banja la Yakobe ndidzatulutsamo zidzukulu,
ndipo a m'banja la Yuda adzalandira
dziko langa lamapiri ngati choloŵa chao.
Anthu anga osankhidwa adzalilandiradi,
atumiki anga adzakhala kumeneko.
10 Yos. 7.24-26 Chigwa cha Saroni chidzakhala busa la nkhosa,
ndipo Chigwa cha Akori chidzasanduka
malo ousirapo msambi wa ng'ombe,
kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
11Koma inu amene mumakana Chauta,
amene mumaiŵala phiri langa lopatulika,
amene mumapembedza Gadi ndi Meni,
milungu yobweretsa mwai ndi tsoka,
12nonsenu ndidzakufetsani ku nkhondo.
Nonsenu mudzaphedwadi,
chifukwa simudayankhe m'mene ndidakuitanani,
ndipo simudamve m'mene ndidalankhula,
koma mudachita zoipa pamaso panga.
Mudasankha kuchita zoipa m'malo mwa zabwino.”
13Nchifukwa chake Chauta akunena kuti,
“Atumiki anga adzadya,
koma inu mudzakhala ndi njala,
atumiki anga adzamwa,
koma inu mudzakhala ndi ludzu.
Atumiki anga adzakondwa,
koma inu mudzakhala ndi manyazi.
14Iwo adzaimba mokondwa,
koma inu mudzalira kwambiri
chifukwa chovutika mu mtima.
Mudzalira mofuula
chifukwa cha kumva kuŵaŵa mu mtima.
15Anthu anga osankhidwa
adzatchula dzina lanu potemberera,
ndipo Ine Chauta ndidzakuphani.
Koma amene amandimvera
ndidzaŵapatsa dzina lina latsopano.
16Motero wopempha madalitso m'dzikomo,
adzachita zimenezo kwa Mulungu wolankhula zoona.
Ndipo wochita malumbiro m'dzikomo,
adzalumbira m'dzina la Mulungu wolankhula zoona,
chifukwa choti mavuto akale aiŵalika
ndipo achotsedwa pamaso panga.”
Chilengedwe chatsopano17 Yes. 66.22; 2Pet. 3.13; Chiv. 21.1 Chauta akunena kuti,
“Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano
ndi dziko lapansi latsopano.
Zakale sadzazikumbukiranso,
zidzaiŵalika kotheratu.
18Koma inu mukhale osangalala
ndi okondwa mpaka muyaya,
chifukwa cha zimene ndidzalenga.
Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano
wodzaza ndi chimwemwe,
ndipo anthu ake adzakhala okondwa.
19 Chiv. 21.4 Mwiniwakene ndidzakhala wokondwa kwambiri
chifukwa cha Yerusalemu,
ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu ake.
Kumeneko sikudzamvekanso kulira kapena kudandaula.
20Ana sadzafanso ali akhanda,
ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zao zonse.
Amene adzafe ali a zaka zana limodzi zokha
adzaoneka ngati anyamata.
Kufa zisanakwane zaka zana limodzi
kudzasonyeza kutembereredwa.
21Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo.
Adzabzala mipesa,
ndipo adzadyerera zipatso zake.
22Sadzamanga nyumbazo kuti anthu ena azikhalamo,
ndipo sadzabzala mipesayo
kuti anthu ena azidyerera zipatso zake.
Anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo.
Ndipo anthu anga osankhidwa
adzakondwerera ntchito za manja ao nthaŵi yaitali.
23Sadzagwira ntchito pachabe,
kapena kubereka ana kuti aone tsoka,
chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Chauta,
iwowo ndi zidzukulu zao zomwe.
24Ndidzaŵayankha asanatsirize nkomwe kupemphera,
ndidzaŵamva akulankhula kumene.
25 Yes. 11.6-9 Mimbulu ndi anaankhosa zidzadyera pamodzi.
Mkango udzadya udzu monga ng'ombe.
Fumbi ndiye lidzakhale chakudya cha njoka.
Pa phiri langa loyera la Ziyoni
sipadzakhala chinthu chopweteka kapena
choononga,” akuterotu Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.