Lun. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Luntha limafika ndi mphamvu

mpaka ku malire a dziko,

limalongosola zonse mwachifundo ndithu.

Luntha limadzetsa zabwino zonse

2 Mphu. 15.2 Ndidakonda luntha ndi kulifunafuna

kuyambira pa unyamata wanga,

ndidasirira kuti ndilikwatire,

ndinkatengedwa nako mtima kukongola kwake.

3Limasonyeza chiyambi chake chaulemu

pophathana ndi Mulungu.

Ndipo Ambuye, mwini zonse, amalikonda.

4 Miy. 8.27-30 Luntha limamvetsako zimene Mulungu akudziŵa,

ndipo limagwira naye pamodzi ntchito zake.

5Ngati chuma nchofunika pa nthaŵi ya moyo uno,

kodi pali china chakenso chamtengowapatali

koposa luntha limene limachita zonse?

6Ngati kumvetsa zinthu nkothandiza,

nchiyaninso chingathandize kopambana luntha

limene limapanga zinthu zonse?

7Kwa anthu ofunitsa kuyenda molungama,

ntchito za luntha zimadzetsa makhalidwe abwino.

Limaphunzitsa za kudziletsa, za kuchenjera bwino,

za kutsata chilungamo ndi za kulimba mtima;

palibe chinthu china chothandiza anthu pa moyo uno

kupambana makhalidwe ameneŵa.

8Ngati munthu alakalaka kukhala wokhoza zambiri,

luntha limadziŵa zakale,

limalingalira zakutsogolo.

Limamvetsa mau apatali zedi,

limamasula zophiphiritsa.

Limadziŵiratu zizindikiro ndi zodabwitsa sizinafike,

limadziŵiratu zimene zidzachitike pa nyengo zina.

Atsogoleri azikhala ndi luntha

9Nchifukwa chake ndidatsimikiza kuti

luntha lidzakhale mnzanga wokhala naye pa moyo wanga,

podziŵa kuti lidzakhala mlangizi wanga wabwino

ndi msangalatsi wanga pa masautso ndi zovuta.

10Ndidati,

pokhala ndi luntha ndidzatchuka pakati pa anthu,

akuluakulu adzandilemekeza ngakhale ndikali mnyamata.

11Anthu adzazindikira luso langa pa milandu,

akuluakulu omwe pondiwona adzadabwa.

12Ndikadzakhala chete,

adzadikira kuti ndilankhule.

Ndikadzalankhula,

adzatchera khutu.

Ndikadzachulukitsa mau,

adzangoti pakamwa gwirire.

13Chifukwa cha lunthalo, ndidzakhala wosadzafa,

adzukulu anga ndidzaŵasiyira chikumbutso chamuyaya.

14Ndidzalamulira makamu a anthu,

anthu a mitundu ina adzandigonjera.

15Mafumu aukali omwe adzachita mantha, akadzamva za ine.

Ndidzakhala wachifundo pakati pa anthu,

ndi wa mtima wolimba pa nkhondo.

16Ndikadzabwerera kunyumba kwanga,

luntha lidzandithandiza pa mpumulo wanga,

chifukwa okhala ndi luntha

samva ululu kapena zoŵaŵa,

amangokondwera ndi kusangalala.

17Zimene ndidaganiza ndi kulingalira

mumtima mwanga ndi izi:

kuti munthu ukakhala ndi luntha,

umapeza moyo wamuyaya.

18Ukakhala bwenzi la luntha,

umapeza chisangalatso chenicheni.

Ntchito zake zimabweretsa chuma chosaŵerengeka.

Tikagwirizana ndi luntha nthaŵi zonse,

timamvetsa zinthu,

ndipo timakhala otchuka

popindulako ndi mau ake.

Nchifukwa chake ndidayendayenda ponseponse,

kufuna njira yolipezera.

19Ndili mwana, ndinali wa khalidwe labwino,

ndi wa mtima wokoma,

20ai, koma ndinene kuti

poti ndinali wabwino,

ndiye kuti ineyo ndidaadza m'thupi lopanda machimo.

21Komabe ndidazindikira kuti sindikadatha

kuwona luntha pa ndekha,

popanda Mulungu kundipatsa.

Ichinso chinali chizindikiro choonetsa nzeru

kudziŵa kumene luntha limafumira.

Tsono ndidapempha Ambuye ndi mtima wanga wonse kuti,

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help