1Chipangano choyamba chija chinali nawo malamulo okhudza chipembedzo, chinalinso ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu.
2Eks. 26.1-30; Eks. 25.31-40; Eks. 25.23-30Anthu adaamanga chihema, ndipo m'chipinda chake choyamba munkakhala choikaponyale, tebulo, ndi mikate yoperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa “Malo Opatulika.”
3Eks. 26.31-33 Paseri pa chochinga chachiŵiri panali chipinda chotchedwa “Malo Opatulika Kopambana”.
4Eks. 30.1-6; Eks. 25.10-16; Eks. 16.33; Num. 17.8-10; Eks. 25.16; Deut. 10.3-5Chipindachi chinali ndi guwa lagolide lofukizirapo lubani. M'chipindamo munalinso bokosi lachipangano. Bokosi lonselo linali lokutidwa ndi golide. M'bokosimo munali kambiya kagolide m'mene munali mana uja, ndi ndodo ya Aroni, ija idaaphukayi. Munalinso miyala iŵiri ija yolembedwapo mau a chipangano.
5Eks. 25.18-22Pamwamba pa bokosilo panali zithunzi za akerubi oonetsa ulemerero wa Mulungu. Mapiko ao adaaphimbira pa chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nkosatheka tsopano lino kufotokoza zonzezi tsatanetsatane.
6 Num. 18.2-6 Malinga ndi malongosoledwe ameneŵa, ansembe amaloŵa m'chipinda choyamba chija masiku onse pokagwira ntchito zao za chipembedzo.
7Lev. 16.2-34 Koma m'chipinda chachiŵiri chija ndi mkulu wa ansembe onse yekha amene amaloŵamo, nayenso ndi kamodzi kokha pa chaka, ndipo saloŵamo popanda kutenga magazi. Magaziwo ngokapereka kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini, ndiponso chifukwa cha machimo ochita anthu mosazindikira bwino.
8Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera akuphunzitsa kuti njira yoloŵera m'Malo Opatulika Kopambana ndi yosatsekukabe pamene chipinda choyamba chija chilipobe.
9Zimenezi nzofanizira chabe, ndipo zimaloza ku nthaŵi ino. Potsata malongosoledwe ameneŵa mphatso ndi nsembe zimene munthu amapereka sizingathe konse kuusandutsa wangwiro mtima wa wopembedzayo.
10Zimangonena za zakudya, za zakumwa, ndi za miyambo yosiyanasiyana ya kasambidwe. Zonsezo ndi malamulo olinga pa zooneka ndi maso chabe, oikidwa kuti azingokhalapo mpaka nthaŵi imene Mulungu adzakonzenso zonse.
11Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano.
12Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
13Lev. 16.15, 16; Num. 19.9, 17-19 Magazi a atonde ndi a ng'ombe zamphongo, ndiponso phulusa la mwanawang'ombe wamkazi zimawazidwa pa anthu amene ali odetsedwa chifukwa chosasamala mwambo wachiyuda. Zimenezi zimaŵayeretsa pakuŵachotsa litsiro lam'thupi.
14Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.
Ndi magazi ake Khristu adatsimikiza Chipangano chatsopano15Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija.
16Ngati munthu alemba Chipangano chosiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba chipanganocho wamwaliradi.
17Paja chipangano chotere chilibe mphamvu, asanamwalire wochilemba. Chimakhala ndi mphamvu pokhapokha wochilembayo atamwalira.
18Nchifukwa chake ngakhale Chipangano choyamba chija sichidachitike popanda kukhetsa magazi.
19Eks. 24.6-8 Poyamba Mose adaalengeza kwa Aisraele malamulo onse, motsata Malamulo amene Mulungu adaampatsa. Pambuyo pake adatenga magazi a anaang'ombe amphongo ndi madzi, nawaza pa buku la Malamulo ndi pa anthu onse. Adaachita zimenezi ndi kanthambi ka chitsamba cha hisope, ndiponso ndi ubweya wankhosa wofiira.
20Pochita zimenezi adanenerera mau akuti, “Aŵa ndi magazi otsimikizira Chipangano chimene Mulungu walamula kuti mchisunge.”
21Lev. 8.15 Momwemonso Mose adawaza magazi pa chihema ndi pa ziŵiya zonse zogwirira ntchito pa chipembedzo.
22Lev. 17.11 Malinga ndi Malamulo a Mosewo pafupifupi zonse zimayeretsedwa ndi magazi, ndipo machimo sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi.
Nsembe ya Khristu imachotsa machimo23Tsono padaafunika kuti zinthu zongofanizira zenizeni za Kumwamba, ziyeretsedwe ndi miyambo imeneyi. Koma kuti za Kumwamba zenizenizo ziyeretsedwe, padaafunika nsembe zina zoposa zimenezo.
24Paja Khristu sadaloŵe m'malo opatulika omangidwa ndi anthu, malo ongofanizira malo enieni opatulika a Kumwamba. Iye adapita Kumwamba kwenikweniko, kuti tsopano aziwonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
25Mkulu wa ansembe onse amaloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chaka ndi chaka atatenga magazi amene sali ake. Koma Khristu sadaloŵe Kumwamba kuti azidzipereka nsembe kaŵirikaŵiri.
26Zikadatero, akadayenera kumamva zoŵaŵa kaŵirikaŵiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma monga zilirimu, waoneka kamodzi kokha pakutha pake pa nthaŵi yotsiriza, kuti achotse uchimo pakudzipereka yekha nsembe.
27Munthu aliyense amafa kamodzi kokha, pambuyo pake nkumaweruzidwa.
28Yes. 53.12Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.