Gen. 41 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yosefe amasula maloto a mfumu Farao

1Patapita zaka ziŵiri, Farao adaalota kuti waimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo.

2Nthaŵi yomweyo adangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zikutuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango.

3Kenaka mumtsinje momwemo mudatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi zofooka, zimene zidaima pa mtunda pafupi ndi ng'ombe zina zija.

4Tsono ng'ombe zoondazo zidadya zinzake zonenepa zija. Pamenepo Farao adadzuka.

5Atagonanso, adalota enanso maloto. Adaona ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zitabala pa mphesi imodzi, ndipo zinali zakucha ndi zokhwima.

6Kenaka padaphukanso ngala zina zisanu ndi ziŵiri zofwapa ndi zopserera ndi mphepo yamkuntho yakuvuma.

7Ngala zofwapazo zidameza ngala zisanu ndi ziŵiri zokhwima zija. Farao atadzuka, adaona kuti anali maloto chabe.

8Dan. 2.2Kutacha m'maŵa adavutika kwambiri, mwakuti adaitana amatsenga ake onse ndi anthu anzeru onse a ku Ejipito. Onsewo atabwera, Farao adaŵafotokozera maloto akewo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatha kuŵamasula.

9Pomwepo woperekera vinyo uja adauza Farao kuti, “Lero ndiwulule kulakwa kwanga.

10Paja inu mfumu mudaatipsera mtima antchitofe. Ndipo ine ndi wophika buledi tonse mudaatitsekera m'ndende, m'nyumba ya mkulu wa alonda.

11Tsono usiku wina, aŵirife tidaalota maloto. Aliyense mwa ife anali atalota maloto ake, a tanthauzo lakelake.

12M'nyumba momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, mtumiki wa mkulu wa alonda a m'ndende muja. Iyeyo adammasulira bwino aliyense mwa ife tanthauzo la maloto akewo.

13Ndipo zidachitikadi monga momwe adaatimasulira. Ine ndidabwerera pa ntchito yanga, koma wophika buledi uja adampachika pa mtengo.”

14Tsono Farao adaitanitsa Yosefe, ndipo adamtulutsa msanga kundendeko. Iyeyo atameta bwino ndi kusintha zovala, adapita kwa Farao kuja.

15Farao adauza Yosefe kuti, “Ine ndidalota maloto, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akutha kumasula malotowo. Tsono adandiwuza kuti iwe ukamva maloto, ati umadziŵa kumasula kwake.”

16Yosefe adayankha kuti, “Sindine ai, koma Mulungu ndiye amene adzatha kuimasulira mfumu maloto ameneŵa.”

17Apo Farao adati, “Ine ndidaalota ntaimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo.

18Nthaŵi yomweyo ndidangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zitatuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango.

19Kenaka padatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi za maonekedwe oipa kwambiri. Ng'ombe zimenezo zinali zoonda kwambiri kupambana ng'ombe zoonda zonse za m'dziko lonse la Ejipito.

20Ng'ombe zoondazo zidadya zinzake zonenepa zija.

21Koma zitadya zinzakezo, palibe ndi mmodzi yemwe akadazindikira, popeza kuti ng'ombe zoondazo sizidasinthike konse kaonekedwe kake, koma zidangokhala zoonda ndithu monga kale. Tsono ndidadzuka.

22Nditagonanso ndidalota ntaona ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zakucha ndi zokhwima bwino zitabala pa mphesi imodzi.

23Pomwepo padaphukanso ngala zina zatirigu zisanu ndi ziŵiri zofwapa, zopserera ndi mphepo yakuvuma.

24Ngala zofwapazo zidameza zinzake zokhwima zija. Tsono ndidafotokozera amatsenga maloto ameneŵa, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adatha kundimasulira.”

25Apo Yosefe adauza Farao kuti, “Maloto onse aŵiriŵa ali ndi tanthauzo limodzi lokha. Mulungu wakuuziranitu zimene adzachite.

26Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepazo ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Ndipo ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zokhwimazo nazonso ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Kumasula kwake nkumodzi.

27Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zoonda zimene zidabwera pambuyo zija, ndiponso ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zopserera ndi mphepo yakuvuma zija, ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za njala.

28Tsono monga momwe ndanenera, ndiye kuti Mulungu wakuuziranitu zomwe adzachite.

29Padzakhala zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu dzambiri m'dziko lonse la Ejipito.

30Zitapita zaka zimenezo, padzakhalanso zaka zisanu ndi ziŵiri za njala, ndipo zaka zonse zija za dzinthu zidzaiŵalika mu Ejipito monse. Njalayo idzaononga dziko.

31Zaka zonse zija za dzinthu dzambiri sizidzakumbukikanso, chifukwa njala imene idzabwereyo idzakhala yoopsa.

32Poti inu Farao mwalota kaŵiri maloto okhaokhaŵa, zikuwonetsa kuti Mulungu ndiye amene wakonza zimenezi, ndipo azichitadi posachedwa.

33Tsopano inu mfumu sankhulani munthu wodziŵa zinthu ndi wanzeru, mumpatse ulamuliro pa dziko lonse la Ejipito.

34Musankhenso anthu akuluakulu m'dziko lonse lino, ndipo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse za zokolola, azichiika padera pa zaka zisanu ndi ziŵiri za chakudya chochuluka.

35Asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zadzinthu zimene zikubwerazi. Azichita zonsezi ndi ulamuliro wanu, ndipo aziika tirigu padera m'mizinda yonse ndi kumsunga bwino.

36Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha nthaŵi ya njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri imene idzabwere ndithu mu Ejipito muno, kuti choncho anthu a ku Ejipito asadzafe ndi njala.”

Yosefe amsandutsa nduna yaikulu ku Ejipito

37Farao pamodzi ndi nduna zake adavomereza zonse zimene adaanena Yosefe.

38Tsono Farao adafunsa nduna zakezo kuti, “Kodi tingampeze kuti munthu wina woposa uyu amene ali ndi mzimu wa Mulungu?”

39Motero Farao adauza Yosefe kuti, “Popeza kuti Mulungu wakuwonetsa zonsezi, palibenso wina aliyense wodziŵa zinthu ndi wanzeru kupambana iweyo.

40Ntc. 7.10 Iwe ndiwe amene udzalamulira dziko langa, ndipo anthu anga onse adzakumvera. Ine ndidzakupambana pa chokhachi choti ndine mfumu.”

41Tsono Farao adauzanso Yosefe kuti, “Tsopano ine ndakusankhula iweyo kuti ukhale nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito.”

42Dan. 5.29 Atatero, Farao adavula mphete yaufumu ku chala chake, naiveka ku chala cha Yosefe. Adamuvekanso zovala zabafuta ndi ukufu wagolide m'khosi mwake.

43Adamkweza pa galeta lake lachiŵiri laufumu, ndipo alonda ake a Farao adayamba kufuula patsogolo pa galetalo kuti, “Mgwadireni.” Motero Yosefe adalandira ulamuliro, ndipo adakhala nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito.

44Farao adauza Yosefe kuti, “Pali ine ndemwe Farao, iwe ukapanda kulola, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kuchita kanthu kalikonse ngakhale kuyenda kumene m'dziko la Ejipito lonseli.”

45Pamenepo Yosefe uja adamutcha Zafenati-Panea. Ndipo adampatsa mkazi dzina lake Asenati, mwana wa Potifera amene anali wansembe wa mzinda wa Oni. Choncho Yosefeyo adayendera dziko lonse la Ejipito.

46Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene adayamba kugwirira ntchito Farao mfumu ya ku Ejipito. Adanyamuka, nayendera dziko lonse.

47Pa zaka zija za dzinthu dzambiri, m'dziko lonse munali chakudya chochuluka kwambiri.

48Yosefe adasonkhanitsa chakudya pa zaka zisanu ndi ziŵiri, pamene kunali dzinthu dzambirimbiri ku Ejipito, nadzisunga m'mizinda. Mu mzinda uliwonse ankasungamo chakudya cha ku minda yozungulira mzindawo.

49Adasonkhanitsa tirigu wochuluka ngati mchenga wakunyanja. Kunali tirigu wochuluka kotero kuti adaaleka nkumuyesa komwe, popeza kuti kunali kosatheka kumuyesa tirigu yenseyo.

50Zaka zanjala zisanafike, Yosefe adabereka ana aamuna aŵiri mwa Asenati uja, mwana wa Potifera, wansembe wa ku Oni.

51Tsono adati, “Mulungu wandiiŵalitsa kusauka kwanga konse kuja ndiponso banja la atate anga.” Motero mwana wake wachisamba uja adamutcha Manase.

52Ndipo adanenanso kuti, “Mulungu wandipatsa ana m'dziko la masautso anga.” Motero mwana wachiŵiriyo adamutcha Efuremu.

53Zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu zitatha,

54Ntc. 7.11 kudafika zaka zisanu ndi ziŵiri za njala zimene ankanena Yosefe zija. Njala imeneyo inali itafikanso ku maiko ena onse, koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya chambiri.

55Yoh. 2.5 Njalayo itakwanira dziko lonse la Ejipito, anthu ankalirira Farao kuti aŵapatse chakudya. Farao ankaŵauza onse kuti, “Pitani kwa Yosefe, zimene akakulamuleni, mukachite zimenezo.”

56Tsono njalayo itakwanira dziko lonse, Yosefe adatsekula nkhokwe za tirigu zija, namaŵagulitsa Aejipitowo, chifukwa inali itakula ndithu mu Ejipitomo.

57Anthu ankafika ku Ejipito kuchokera ku mbali zonse za dziko lapansi, kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inali itakula koopsa konsekonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help