Lev. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chaka chasabata(Deut. 15.1-11)

1 Eks. 23.10, 11 Chauta adauza Mose pa phiri la Sinai kuti,

2“Uza Aisraele kuti: Mukadzaloŵa m'dziko limene ndikukupatsanilo, nthaka yomwe izikapatulira Chauta chaka chasabata.

3Pa zaka zisanu ndi chimodzi muzikalima minda yanu, ndipo muzikathenera mitengo yanu yamphesa ndi kuthyola zipatso zake.

4Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri chikhale chaka chopumuza nthaka, chaka chopatulikira Chauta, ndipo musalime minda yanu kapena kuthenera mitengo yanu yamphesa.

5Musakolole zimene zidamera zokha m'munda mwanu, ndipo musathyole mphesa za mitengo yanu yosathenera. Chaka chimenechi chikhale chopumuza nthaka.

6Chaka chachisanu ndi chiŵiri chopumulacho chidzakupatsani chakudya chokwanira nonsenu, inuyo ndi akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito anu pamodzi ndi alendo amene akukhala nanu.

7Ng'ombe zanu ndi nyama za m'dziko mwanu zizidzadya zimene nthaka idzabereka.”

Za chaka chaufulu

8“Muziŵerenga masabata asanu ndi aŵiri a zaka, zaka zisanu ndi ziŵiri kuchulukitsa kasanunkaŵiri, kuti nyengo ya masabata asanu ndi aŵiri a zakayo ikwanire zaka 49 pamodzi.

9Tsono pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mulize lipenga mokweza. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo, ndilo tsiku limene mulize lipengalo m'dziko lanu lonse.

10Mupatule chaka cha 50, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu m'dziko lonselo kwa onse amene ali m'menemo. Kwa inu chaka chimenecho chidzakhale chokondwerera zaka 50, pamene aliyense adzayenera kubwerera pa mtunda wake, ndipo aliyense mwa inu abwerere ku banja lake.

11Chaka chimenecho cha 50 chikhale chaka chachikondwererodi. Pa chaka chimenechi musabzale kanthu, kapena kukolola mphulumukwa, kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosathenera.

12Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka 50. Chikhale chaka chopatulika kwa inu ndipo mudye zam'likale.

13“Chaka chimenechi chokondwerera zaka 50, aliyense abwerere pa mtunda wake.

14Ukagulitsa mnzako munda, kapena ukagula munda kwa mnzako, pasakhale kuchenjeretsana.

15Ugule kwa mnzako potsata chiŵerengero cha zaka zimene zidapita kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha 50 chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiŵerengero cha zaka zokolola zimene zatsala.

16Zaka zikachuluka uwonjezere mtengo, zaka zikachepa uchepetse mtengo, poti akukugulitsani potsata chiŵerengero cha zaka zokolola.

17Musachenjeretsane, koma muwope Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”

Zovuta za chaka chasabata

18“Muzimvera malamulo anga ndi kutsata zimene ndikukulamulani, ndipo muzizichitadi. Potero mudzakhala m'dzikomo popanda chokuvutani.

19Nthaka idzakupatsani zipatso zake, mudzazidya mpaka kukhuta, ndipo mudzakhala m'dzikomo popanda chokuvutani.

20Mukafunsa kuti: Kodi pa chaka chachisanu ndi chiŵiri tidzadya chiyani, tikapanda kubzala kapena kukolola dzinthu?

21Ine ndidzalamula kuti mukhale ndi madalitso pa chaka chachisanu ndi chimodzi, kuti nthaka ibale zakudya zokwanira zaka zitatu.

22Pamene mubzala pa chaka chachisanu ndi chitatu muzidzadya sundwe. Mpaka chaka chachisanu ndi chinai pokolola, mudzidzadyabe sundwe.”

Za kubwezera zinthu

23“Mtunda usagulitsidwe mpaka muyaya, pakuti dzikolo ndi langa. Inu ndinu alendo ndiponso oyendayenda okhala ndi Ine.

24M'dziko monse m'mene mudzakhalemo, mudzaloleza anzanu kuwombola mtunda umene unali wao kale.

25“Mbale wanu akakhala wosauka, nagulitsako gawo lina la mtunda wake, wachibale wake abwere kudzaombola mtunda umene mbale wake wagulitsawo.

26Munthu akakhala wopanda mbale woti aombole mtundawo, ndipo pambuyo pake munthuyo nkusanduka wolemera, napeza zokwanira kuti auwombole,

27aŵerenge zaka kuyambira pamene adagulitsa mtundawo. Amubwezere amene adaagulayo ndalama zimene akadayenera kuzipereka mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Atatero, atenge mtunda wake.

28Koma akapanda kukhala nazo zokwanira zoti aombolere, mtundawo udzakhalebe m'manja mwa amene adagulayo, mpaka pa chaka chokondwerera zaka 50. Pa chaka chimenecho mtundawo udzakhala woombola ndipo ubwerere kwa mwiniwake.

29“Munthu akagulitsa nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi linga, angathe kuiwombola chisanathe chaka chathunthu ataigulitsa. Adzatha kuiwombola pa nthaŵi yomweyo.

30Nyumbayo ikapanda kuwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi malingawo idzakhala ya munthu amene adagulayo pa mibadwo yake yonse. Sidzaomboledwa pa chaka chokondwerera zaka 50.

31Koma nyumba zam'midzi, zosazingidwa ndi malinga, achite nazo monga momwe amachitira ndi minda yam'dzikomo. Angathe kuziwombola, ndipo zibwezedwe pa chaka chokondwerera zaka 50.

32Koma kunena za mizinda ya Alevi nyumba zimene zili m'mizinda mwao, Aleviwo angathe kuziwombola nthaŵi iliyonse.

33Mlevi wina akapanda kuwombola nyumba imene idagulitsidwa mumzinda mwaomoyo aibweze pa chaka chokondwerera zaka 50. Pakuti nyumba zimene zili m'mizinda ya Alevi ndi zao za Aleviwo pakati pa Aisraele.

34Koma minda ya m'milaga ya mizindayo singagulitsidwe, pakuti mindayo ndi yao mpaka muyaya.”

Za kukongoza osauka

35 Deut. 15.7, 8 “Mbale wako akakhala wosauka, ndipo sangathe kudzisamala, iweyo umthandize. Uzikhala naye monga ngati mlendo, ndiponso monga ngati munthu wokhala nao kanthaŵi.

36Usalandire chiwongoladzanja pa ndalama zimene adakongola, kapena kuwonjezerapo zina, koma uziwopa Mulungu wako, ndipo ulole mbale wakoyo kuti akhale nawe.

37Eks. 22.25; Deut. 23.19, 20 Musakongoze mnzanu ndalama zanu kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumpatsa chakudya kuti mupeze phindu.

38Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito kuti ndikupatseni dziko la Kanani, ndipo kuti ndikhale Mulungu wanu.”

Za mbale wodzigulitsa kuti akhale kapolo

39 Eks. 21.2-6; Deut. 15.12-18 “Mbale wako amene ukukhala naye akakhala wosauka nadzigulitsa kwa iwe, usamuyese kapolo wako.

40Akhale ngati wantchito wako, ndiponso ngati mlendo wako. Azikugwirira ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka 50.

41Pambuyo pake achoke kwa iwe, pamodzi ndi ana ake omwe, apite ku banja lake, ndi kubwerera ku choloŵa cha makolo ake.

42Aisraele ndi atumiki anga amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, asagulitsidwe ngati akapolo.

43Usaŵalamule mwankhalwe, koma uziwopa Mulungu wako.

44Kunena za akapolo aamuna kapena aakazi oti muzikhala nawo, mungathe kuŵagula kwa mitundu ina ya anthu okuzungulirani.

45Mungathenso kuŵagula pakati pa alendo amene akukhala pakati panu ndiponso pakati pa mabanja okhala nanu amene adabadwira m'dziko mwanu. Amenewo angathe kukhala anu.

46Akapolowo mungathe kuŵasiya m'manja mwa ana anu, inu mutafa, kuti akhale choloŵa chao nthaŵi zonse. Amenewo mungathe kuŵayesa akapolo, koma abale anu Aisraele musaŵalamule mwankhalwe.

47“Mlendo kapena munthu wodzangokhala nanu akalemera, ndipo mbale wanu wokhala naye pafupi akakhala wosauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendoyo kapena kwa munthu wodzangokhala nanu uja, kapena kwa aliyense wa banja la mlendolo,

48mbale wanu wodzigulitsayo angathe kuwomboledwa. Wina mwa abale ake angathe kumuwombola,

49kapena mbale wa bambo wake, kapena mwana wa mbale wa bambo wake, kapena wachibale wa pabanja pake, onseŵa angathe kumuwombola. Koma wodzigulitsayo akalemera, angathe kudziwombola yekha.

50Aŵerengerane ndi munthu adamgulayo kuyambira chaka chimene adadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Mtengo wa kuwomboledwa kwake ukhale wolingana ndi chiŵerengero cha zakazo. Nthaŵi imene anali ndi mbuyakeyo iŵerengedwe monga ngati nthaŵi ya munthu wantchito.

51Zaka zikakhala kuti zikadalipo zambiri, pa mtengo umene adalipira pomgula, iye abweze mtengo womuwombolerawo.

52Zikangotsala zaka zoŵerengeka kuti chifike chaka chokondwerera zaka 50, aŵerengerane ndi mbuye wake, ndipo potsata zaka zotsala mpaka cha 50, abweze ndalama za kuwomboledwa kwake.

53Azikhala naye ngati wantchito wolembedwa, chaka ndi chaka. Asamlamule mwankhalwe, iwe ukupenya.

54Akapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, adzaomboledwa pa chaka chokondwerera zaka 50, iyeyo pamodzi ndi ana ake.

55Ndithudi kwa Ine Aisraele ndi atumiki anga amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help