1 Mphu. 29.14-20 Mwana wanga,
kodi udalonjeza kumlipirira mnzako chikole,
kodi udaperekera mlendo chigwiriro?
2Kodi udakodwa ndi mau a pakamwa pako pomwe,
kodi udagwidwa ndi mau olankhula iwe wemwe?
3Ndiye iwe mwana wanga,
popeza kuti wadziponya m'manja mwa mnzako,
chita izi kuti udzipulumutse:
nyamuka, pita msanga, ukampemphe kuti akumasule.
4Usagone tulo,
usaodzere,
5Dzipulumutse monga imadzipulumutsira mphoyo kwa mlenje,
monga imadzipulumutsira kwa wosaka.
6Pita kwa nyerere, mlesi iwe.
Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru.
7Ilibe ndi mfumu yomwe,
ilibe kapitao kapena wolamulira.
8Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe,
ndipo imatuta chakudyacho m'masika.
9Kodi ukhalabe uli gone pamenepo mpaka liti, mlesi iwe?
Kodi titha liti tulo takoto?
10 Miy. 24.33, 34 Ukati ndingogonako pang'ono,
ndingoodzerako pang'ono chabe,
ndingopinda manja okhaŵa kuti ndipumuleko,
11umphaŵi udzakugwira ngati munthu wachifwamba,
usiŵa udzakufikira mwadzidzidzi ngati mbala.
12Munthu wachabechabe, munthu woipa,
amangoyendayenda nkumalankhula zabodza.
13 Mphu. 27.22 Amatsinzinira masoŵa nkumakwekwesa pansi mapazi ake,
amalozaloza ndi chala chake.
14Amalingalira zoipa ndi mtima wake wopotoka,
amangokhalira kuvundula madzi pakati pa anthu.
15Nchifukwa chake tsoka lidzamgwera modzidzimutsa.
Pa kamphindi kochepa adzaonongedwa, osapulumuka konse.
16Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi
zimene Chauta amadana nazo,
makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa:
17maso onyada, pakamwa pabodza,
manja opha munthu wosalakwa,
18mtima wokonzekera kuchita zoipa,
mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,
19mboni yonama yolankhula mabodza,
ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.
20Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako,
usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako.
21Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse,
uzimangirire m'khosi mwako.
22Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira.
Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda.
Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.
23Paja malamulowo ali ngati nyale,
maphunzitsowo ali ngati kuŵala,
madzudzulo a mwambo aja ndiwo mkhalidwe weniweni
pa moyo wa munthu.
24Zimenezi zidzakupulumutsa kwa mkazi woipa,
zidzakuthandiza kuti usamvere mau osalala
a mkazi wachiwerewere.
25Mumtima mwako usamakhumbira kukongola kwake,
usakopeke nawo maso ake.
26Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi,
koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe.
27Kodi munthu angathe kufukata moto,
zovala zake osapsa?
28Kodi munthu angathe kuponda makala amoto,
mapazi ake osapserera?
29Ndizo zimamchitikira wokaloŵerera mkazi wamwini.
Aliyense wokhudza mkazi wotero adzalangidwa.
30Paja anthu sainyoza mbala,
ikaba chifukwa cha njala.
31Komabe ikangogwidwa, imalipira kasanunkaŵiri,
mpaka mwina kulandidwa katundu yense wa m'nyumba mwake.
32Amene amachita chigololo ndi wopanda nzeru,
amangodziwononga yekha.
33Adzangolandira mabala ndi manyozo,
ndipo manyazi ake sadzamchoka ai.
34Paja nsanje imakalipitsa mwini mkaziyo,
sachita chifundo akati alipsire.
35Savomera dipo lililonse,
sapepeseka ngakhale umpatse mphatso zochuluka chotani.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.