1 1Maf. 4.32 Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse.
Nyimbo YoyambaMkazi
2Undimpsompsone ndi milomo yako,
chifukwa chikondi chako nchoposa vinyo kukoma kwake.
3Mafuta ako odzola ngonunkhira bwino,
dzina lako likundikumbutsa za mafuta otsanyukako.
Nchifukwa chaketu, atsikana sangaleke kukukonda.
4Tenge, ndizikutsata, tiye tifulumire.
Iwe mfumu yanga, kandiloŵetse m'chipinda mwako.
Tizisangalala kwambiri ndi kukondwa limodzi.
Chikondi chako tichitamande kupambana vinyo.
Akazi onse amakukondera kaone!
5Inu akazi a ku Yerusalemu,
ine ndine wakuda inde,
komatu wokongola tsono.
Ndine wakuda ngati mahema a ku Kedara,
komabe wokongola ngati makatani
a m'nyumba ya Solomoni.
6Musandiyang'ane monyoza
chifukwa cha kudaku,
ndi dzuŵatu lidandidetsali.
Alongo anga adandikwiyira,
mpaka kukandigwiritsa ntchito m'minda yamphesa.
Koma munda wangawanga, osatha kuusamala.
7Tandiwuza, iwe wokondedwa wanga wapamtima,
kumene umadyetsa ziŵeto zako,
kumene umazigoneka masana.
Nanga ndizingokhala ndili zunguliruzunguliru
ku magulu a ziŵeto za abusa anzako!
Mwamuna
8Iwe wokongola koposa akazi onsewe,
ngati sukukudziŵa,
uzingotsata m'makwalala a msambi wa ziŵeto,
uzidyetsa mbuzi zako pambali pa mahema a abusawo.
9Iwe bwenzi langa,
kukongola kwako, ngati akavalo a magaleta a Farao.
10Masaya ako akukongola
ndi ndolo zam'makutuzi.
Khosi lakonso likukongola
ndi mikanda ya miyala yamtengowapatali.
11Tidzakupangira ukufu wagolide,
wokhala ndi timakaka tasiliva.
Mkazi
12Pamene mfumu inali gone podyera pake,
mafuta anga onunkhira adapereka kafungo kachikoka.
13Wokondedwa wanga ndikumuwona
ngati kathumba ka mure,
kamene kamakhala pakati pa maŵere angaŵa.
14Wokondedwa wanga ndikumuwona
ngati chipukutu cha maluŵa ofiira
a m'munda wamphesa wa ku Engedi.
Mwamuna
15Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola,
ndiwe chiphadzuŵa.
Maso ako akunga ngati nkhunda.
Mkazi
16Wokondedwa wanga, nawenso ndiwe wokongola,
wokongoladi zedi.
Malo athu ogonapo ndi msipu wobiriŵira.
17Mitanda ya nyumba yathu ndi yamkungudza,
phaso lake ndi la mtengo wa paini.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.