Yak. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za lilime

1Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.

2Mphu. 5.9-15; 14.1; 28.13-26Paja tonsefe timalakwa pa zinthu zambiri. Ngati alipo amene salakwa pakulankhula, ndiye kuti ndi wangwirodi ameneyo, mwakuti angathe kulamuliranso thupi lake lonse.

3Timaika kachitsulo m'kamwa mwa kavalo kuti atimvere, ndipo tingathe kumaongolera thupi lake lonse.

4Onaninso zombo. Ngakhale nzazikulu kwambiri, ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, komabe tsigiro laling'onong'ono ndi limene limaziwongolera kulikonse kumene woyendetsa akufuna.

5Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu.

Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto.

6Mphu. 5.13; 28.22Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.

7Munthu angathe kuŵeta mtundu uliwonse wa nyama, wa mbalame, wa zokwaŵa, ndi wazam'nyanja, ndipo adaziŵetapodi.

8Koma lilime palibe munthu amene angathe kuliŵeta. Ndi loipa, silidziŵa kupumula, ndipo ndi lodzaza ndi ululu wakupha.

9Gen. 1.26Ndi lilime lomwelo timayamika Ambuye, amenenso ndi Atate, komanso ndi lilime lomwelo timatemberera anthu anzathu amene Mulungu adaŵalenga ofanafana naye.

10Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika.

11Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi?

12Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka.

Za nzeru zochokera Kumwamba

13 Mphu. 19.20-30 Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.

14Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza.

15Nzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma ndi nzapansipano, ndi za anthu chabe, ndiponso nzochokera ku mizimu yoipa.

16Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse.

17Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.

18Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help