1 Sam. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Saulo akumana ndi Samuele.

1Panali munthu wina wotchuka, wa ku dera la Benjamini, dzina lake Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, wa fuko la Benjamini.

2Iyeyo anali ndi mwana dzina lake Saulo, mnyamata wokongola. Pakati pa Aisraele onse panalibenso mnyamata wokongola kupambana iyeyo. Anali wamtali kotero kuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa.

3Tsiku lina Kisi adaona kuti abulu ake asoŵa. Choncho adauza Saulo kuti, “Tenga mmodzi mwa anyamata antchitoŵa, munyamuke, mukaŵafunefune abuluwo.”

4Iwo adabzola dziko lamapiri la Efuremu ndi la Salisa, koma osaŵapeza. Kenaka adabzola dziko la Salimu, koma kumeneko kunalibenso. Adabzolanso dziko la Benjamini, koma osaŵapezabe.

5Atafika ku dziko la Zufu, Saulo adauza mnyamata wake amene anali naye kuti, “Tiye tizibwerera, kuwopa kuti bambo wanga angaleke kusamala za abulu ndi kudera nkhaŵa za ife.”

6Koma mnyamatayo adati, “Mumzindamu muli munthu wa Mulungu, munthu amene onse amamchitira ulemu. Zonse zimene amanena zimachitikadi. Bwanji tipite kumeneko. Mwina mwake angathe kutiwuza za ulendo wathuwu.”

7Saulo adafunsa mnyamata wakeyo kuti, “Tsono tikapita, timtengere chiyani munthuyo? Buledi amene adaali m'matumba mwathu watha, ndipo tilibe ndi mphatso yomwe yoti tingampatse munthu wa Mulunguyo. Kodi tili ndi chiyani?”

8Mnyamatayo adayankha kuti, “Pano ndili ndi kandalama kakang'ono kasiliva, ndipo ndikapereka kwa munthu wa Mulunguyo, kuti atiwuze kumene kwapita abuluwo.”

9(Kale ku Israele, munthu akamapita kukapempha nzeru kwa Mulungu, ankati, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene tsopano amamutchula mneneri, kale ankatchulidwa mlosi).

10Tsono Saulo adauza mnyamata wakeyo kuti, “Chabwino. Tiye tizipita.” Choncho adapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulunguko.

11Pamene ankakwera phiri kupita kumzindako, adakumana ndi atsikana akutuluka mumzindamo kukatunga madzi, ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?”

12Iwo adayankha kuti, “Inde, alipo. Akunka patsogolo panupa. Fulumirani. Wangofika tsopano apa mumzindamu, chifukwa anthu akukapereka nsembe lero ku kachisi ku phiri.

13Mukangoloŵa mumzindamo, mumpeza asanapite kukachisiko kuti akadye. Anthu sangayambe kudya mpaka iye atabwera, poti ayenera kuyamba waidalitsa nsembeyo. Pambuyo pake ndiye anthu oitanidwa adzayamba kudya. Tsono pitani, mukumana naye posachedwa.”

14Choncho adapita kumzindako. Poloŵa mumzindamo, adaona Samuele akutuluka kumene, alikudza kwa iwo pa njira yopita kukachisi kuja.

15Koma chadzulo, Saulo asanabwere, nkuti Chauta atamdziŵitsiratu Samuele kuti,

16“Maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzakutumizira munthu wa ku dera la Benjamini, udzamudzoze kuti akhale mfumu ya anthu anga Aisraele. Adzapulumutsa anthu kwa Afilisti. Ndaona kuzunzika kwao, ndipo ndamva kulira kwao.”

17Samuele ataona Saulo, Chauta adamuuza kuti, “Ndi ameneyu munthu ndidakuuza uja. Ndiye amene adzalamulire anthu anga.”

18Tsono Saulo adayandikira Samueleyo ku chipata namufunsa kuti, “Zikomo, kodi kunyumba kwa mlosi nkuti?”

19Samuele adamuyankha kuti, “Mlosiyo ndine. Tsogolaniko ku kachisi, poti lero mudya nane, ndipo m'maŵa ndikuuzani zonse zimene zili mumtima mwanu, kenaka ndidzakulolani kuti mupite.

20Musadandaule za abulu anu amene akhala akusoŵa masiku atatu apitaŵa, poti adapezeka kale. Kodi ndani amene Aisraele akumfunitsitsa? Kodi sindiwe ndi banja lonse la bambo wako?”

21Saulo adayankha kuti, “Komatu ine ndine Mbenjamini, fuko laling'ono pakati pa mafuko onse a Aisraele. Kodi banja langa sindiye laling'ono kwambiri pakati pa mabanja a fuko la Benjamini? Chifukwa chiyani mukundilankhula zotere?”

22Tsono Samuele adatenga Saulo ndi mnyamata wake uja, ndipo adaloŵa nawo m'chipinda chachikulu, naŵapatsa malo kutsogolo kwa anthu oitanidwa, amene onse pamodzi anali ngati anthu makumi atatu.

23Adauza wophika kuti, “Bwera nayo nthuli yanyama ija ndidaakupatsayi. Paja ndidaakuuza kuti uiike pambali.”

24Choncho wophika uja adatenga mwendo wa nyama naupereka kwa Saulo. Ndipo Samuele adati, “Nayi nyama imene ndidaakusungira. Idya, chifukwa ndidaakuikira padera kuti pa nthaŵi yake ino, uidye pamodzi ndi anthu amene ndidaŵaitana.” Choncho Saulo adadya ndi Samuele tsiku limenelo.

25Ndipo pamene adatsika kuchokera kukachisi kuja kukaloŵa mu mzinda, adamukonzera Saulo pogona pamwamba pa denga, ndipo iye adagona pamenepo.

Samuele adzoza Saulo.

26Tsono mbandakucha Samuele adaitana Saulo padengapo kuti, “Dzuka, ndikuperekeze, ndikutule apo.” Pompo Saulo adadzuka, ndipo onse aŵiriwo adakaloŵa mu mseu.

27Atafika kothera kwake kwa mzindawo, Samuele adauza Saulo kuti, “Uza mnyamatayu kuti abatsogola, iwe wekha uime pang'ono, kuti ndikuuze mau ochokera kwa Mulungu.” Mnyamata uja adatsogola.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help