Yer. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Israele ndi wosakhulupirika

1Chauta akuti,

“Munthu akasudzula mkazi wake,

mkaziyo nkuchoka,

nakakwatiwa ndi mwamuna wina,

kodi mwamuna woyambayo angathe kumtenganso mkaziyo?

Kodi atachita zotero,

sindiye kuti dzikolo laipitsidwa kwambiri?

Tsono iwe Israele, wachita zadama ndi abwenzi ambiri.

Kodi ungabwererenso kwa Ine?

2Uyang'ane ku zitunda zonse zachipembedzo.

Mpoti pamene sudachitepo zadama?

Unkakhala m'mbali mwa njira kumadikirira zibwenzi zako,

ngati Mluya wobisalira anthu m'chipululu.

Waipitsa dziko ndi mkhalidwe wako woipa wachiwerewere.

3Nchifukwa chake Chauta adaimitsa mvula,

ndi mvula yam'masika yomwe sidagwe.

Komabe maonekedwe ako onse nga mkazi wachiwerewere,

ndipo ulibe ndi manyazi omwe.

4Kodi si tsopano apa wakhala ukundiwuza kuti,

‘Atate, ndinu bwenzi la unyamata wanga,’

numadzifunsa kuti,

5‘Kodi Chauta adzandipsera mtima nthaŵi zonse?

Kodi adzakwiya mpaka muyaya?’

Umu ndimo m'mene unkalankhulira.

Komabe iwe udapitiriza kuchita zoipa

monga momwe unkathera.”

Ayuda akatembenuka mtima, Chauta adzaŵakhululukira

6 2Maf. 22.1—23.30; 2Mbi. 34.1—35.27 Pa nthaŵi ya mfumu Yosiya, Chauta adati, “Kodi waona zimene wosakhulupirika uja Israele adachita? Ankakwera kukapembedza pa phiri, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Motero kumeneko ankakachita zadama.

7Ndidaaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sadabwerere. Tsono Yuda, mbale wake wosakhulupirika uja, adaziwona zimenezo.

8Adaona kuti Israele wosakhulupirika uja ndidamsudzula ndi kumpirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda, mbale wake, sadaope. Iyenso adakhala wosakhulupirika, adapita kukachita zadama.

9Dama la Israele linali lochititsa manyazi, kotero kuti potsiriza pake adaipitsa dziko. Adachita chigololo popembedza mafano amiyala ndi amitengo.

10Komabe atachita zonsezi, Yuda mbale wake wosakhulupirika uja sadabwerere kwa Ine ndi mtima wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akuterotu Chauta.

11Chauta adandiwuzanso kuti, “Israele wosakhulupirika uja kupalamula kwake nkochepa, kuyerekeza ndi Yuda wosakhulupirika uja.

12Pita ukalalike kumpoto uthenga uwu wakuti,

“ ‘Israele wosakhulupirikawe, bwerera,’

akuterotu Chauta.

‘Ukali wanga sudzapitirira,

poti ndine wachifundo.

Sindidzakukwiyira mpaka muyaya.

13Ungovomera kulakwa kwako.

Vomera kuti udaukira Chauta Mulungu wako,

kuti udapembedza nao milungu yachilendo

patsinde pa mitengo yogudira,

ndiponso kuti sudamvere mau anga,’ ”

akuterotu Chauta.

14“Bwererani inu anthu osakhulupirika,

pakuti mbuye wanu ndine.

Ndidzakutengani kupita nanu ku Ziyoni,

mmodzi kuchokera ku mzinda uliwonse,

aŵiri kuchokera ku banja lililonse.

15“Kumeneko ndidzakupatsani abusa a kukhosi kwanga. Adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha.

16Masiku amenewo mukadzachulukana m'dzikomo, anthu sadzalankhulanso za bokosi lachipangano la Chauta. Sadzaliganizira kapena kulikumbukira kapena kulisoŵa, ndipo sadzapanganso lina.

17Nthaŵi imeneyo Yerusalemu adzatchulidwa Mpando waufumu wa Chauta. Ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana kumeneko pamaso pa Chauta. Sadzaumiriranso kutsata mtima wao woipa.

18Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphathana ndi fuko la Israele. Onse pamodzi adzachokera ku dziko lakumpoto kupita ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, kuti likhale choloŵa.”

Kusakhulupirika kwa Aisraele

19Chauta akunena kuti,

“Iwe Israele, ndikadakonda kukukhazika

pakati pa ana anga,

ndi kukupatsa dziko lokoma,

choloŵa chokongola kwambiri

kupambana maiko a mitundu ina ya anthu.

Ndidaganiza kuti udzanditchula ‘Atate’,

ndipo kuti sudzaleka kumanditsata.

20Ndithu, monga momwe mkazi wosakhulupirika

amasiyira mwamuna wake,

iwenso Israele wakhala wosakhulupirika kwa Ine,”

akuterotu Chauta.

21Pakumveka liwu pa magomo,

Aisraele akulira ndiponso akupempha chifundo,

pakuti atsata njira zoipa,

ndipo aiŵala Chauta, Mulungu wao.

22“Bwererani kwa Ine, inu anthu anga osakhulupirika.

Ndidzakuchiritsani kuti mukhale okhulupirika.”

Inu mukuti, “Tikubwera kwa Inu,

poti ndinu Chauta, Mulungu wathu.

23Kupembedza pa magomo sikuthandiza,

kuchita maphwando pa mapiri kulibenso ntchito.

Zoonadi, mwa Chauta, Mulungu wathu

ndiye muli chipulumutso cha Israele.

24“Kuchokera pa chiyambi cha mtundu wathu, Baala, mulungu wochititsa manyazi uja, wakhala akutiwonongetsa phindu la ntchito ya makolo athu, ndiye kuti nkhosa ndi ng'ombe zao, ana ao aamuna ndi ana ao aakazi.

25Tsono tigone pansi mwamanyazi, ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe. Paja tidachimwa ife pamodzi ndi makolo athu, kuchimwira Chauta Mulungu wathu, kuyambira ubwana wathu mpaka lero lino. Sitidamvere mau a Chauta Mulungu wathu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help