1“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Efeso umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa uja wanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m'dzanja lake lamanja, ndi kuyenda pakati pa ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide zija.
2Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti mwakhala mukugwira ntchito kolimba, ndipo kuti muli ndi kupirira kosatepatepa. Ndikudziŵanso kuti anthu ochimwa simungaŵalekerere. Anthu amene amadzitcha atumwi, pamene sali atumwi konse, mwaŵayesa, ndipo mwaŵapeza kuti ngonama.
3Ndinudi opirira kolimba, ndipo mwasauka kwambiri chifukwa cha Ine, osatopa.
4Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mwasiya chikondi chimene munkandikonda nacho poyamba paja.
5Kumbukirani tsono kuti munali okwera kwambiri musanagwe; nchifukwa chake mutembenuke mtima, muzichitanso zija munkachita poyambazi. Mukapanda kutero, ndidzabwera nkudzachotsa ndodo ya nyale yanu pamalo pake.
6Komabe chokomera chanu ndi ichi chakuti, mumadana ndi zochita za Anikolai, zimene inenso ndimadana nazo.
7 mboni yanga, munthu wanga wokhulupirika. Paja iye uja adamuphera kwanu komwe, kumene amakhala Satana.
14Num. 22.5, 7; 31.16; Deut. 23.4; Num. 25.1-3 Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo.
15Chimodzimodzi inuyo, muli nawonso anthu ena otsata chiphunzitso cha Anikolai.
16Mutembenuke mtima tsono. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa, ndipo ndidzakuthirani nkhondo ndi lupanga lotulukira m'kamwa mwanga lija.
17 Eks. 16.14, 15; 16.33, 34; Yoh. 6.48-50; Yes. 62.2; 65.15 “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.
“Amene adzapambane, ndidzampatsako chakudya chobisika cha mana. Ndidzampatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziŵa iye yekha, osati wina aliyense.”
Kalata yolembera mpingo wa ku Tiatira18“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Tiatira umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa Mwana wa Mulungu, uja ali ndi maso onyezimira ngati malaŵi a moto, ndi mapazi onga chitsulo choŵala.
19Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa chikondi chanu, kukhulupirika kwanu, kutumikira kwanu, ndi kupirira kwanu kosatepatepa. Ndikudziŵa kuti ntchito zanu zatsopano nzabwino koposa zoyamba zija.
201Maf. 16.31; 2Maf. 9.22, 30 Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mumamlekerera mkazi uja Yezebele, amene amadzitcha mneneri. Iye uja amanyenga atumiki anga nkumaŵaphunzitsa kuti azichita dama ndi kumadya zansembe zoperekedwa kwa mafano.
21Ndidampatsa nthaŵi kuti atembenuke mtima, koma safuna kutembenuka ndi kuleka kusakhulupirika kwake.
22Tsono ndidzamgwetsa m'matenda, ndipo ochita naye dama lakelo, ndidzaŵagwetsa m'masautso aakulu, akapanda kutembenuka mtima ndi kuleka zoipa zonse zimene ankachita naye.
23Mas. 7.9; Yer. 17.10; Mas. 62.12Ana akenso ndidzaŵapha. Motero mipingo yonse idzazindikira kuti Ine ndine uja ndimadziŵa za m'mitima mwa anthu ndi za m'maganizo mwao. Aliyense mwa inu ndidzachita naye molingana ndi ntchito zake.
24“Koma enanu a ku Tiatira simudatsate nao chiphunzitso choipachi, ndipo simudaphunzireko zimene iwo amati zinsinsi zozama za Satana. Kwa inu mau anga ndi akuti sindikuwonjezerani malamulo ena,
25koma inu, mungogwiritsa zimene mudaphunzira, mpaka Ine ndidzabwere.
26Mas. 2.8, 9Amene adzapambane ndi kuchita mpaka potsiriza zimene ndamlamula, ndidzampatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu.
27Adzailamulira ndi ndodo yachitsulo, nadzaiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi womwe Ine ndidaulandira kwa Atate.
28Ndidzampatsanso Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa ija.
29“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.