Lk. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu auka kwa akufa(Mt. 28.1-10; Mk. 16.1-8; Yoh. 20.1-10)

1M'mamaŵa pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, azimai aja adapita ku manda, atatenga zonunkhira zimene adaakakonza.

2Adapeza chimwala chija chili chogubuduza kale kuchoka pakhomo pa manda aja.

3Adaloŵa m'mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu.

4Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu aŵiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo.

5Akazi aja adachita mantha naŵeramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa?

6 kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.”

45Tsono adaŵathandiza kuti amvetse bwino Malembo.

46Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu,

47kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.

48Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi.

49Ntc. 1.4Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.”

Yesu akwera Kumwamba(Mk. 16.19-20; Ntc. 1.9-11)

50 Ntc. 1.9-11 Atatero Yesu adaŵatsogolera kuchokera mumzindamo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake naŵadalitsa.

51Mphu. 50.20Akuŵadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba.

52Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.

53Tsono ankasonkhana m'Nyumba ya Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi akutamanda Mulungu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help