Yud. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Maganizo a Yuditi

1Yuditi adaŵauza kuti, “Mverani, abale anga. Tengani mutuwu, mukaupachike pamwamba pa linga lanu.

2Tsono kukangocha, dzuŵa likutuluka, anthu nonse amphamvu mutenge zida zanu, mutuluke mu mzinda. Muike mtsogoleri patsogolo panu kuchita ngati mukufuna kutsikira ku chigwa kukamenyana nkhondo ndi Aasiriya, koma musapiteko.

3Apo Aasiriya atenga zida zao zankhondo nkupita ku zithando kukadzutsa atsogoleri ao ankhondo. Iwowo athamangira ku hema la Holofernesi, koma sakampeza. Onsewo adzachita mantha nkuthaŵa.

4Ndiye inuyo ndi onse okhala m'malire a Israele, muŵathamangitse ndipo muŵaphe akuthaŵa.

5Koma muyambe mwaitana Akiyore, Mwamoni uja, kuti abwere kuno, adzaone ndi kuzindikira mutu wa munthu amene ankanyoza Israele, natuma iyeyo kwa ife poganiza kuti adzafera kuno pamodzi ndi ife.”

Akiyore atembenuka mtima

6Motero adamuitana Akiyore ku nyumba ya Uziya. Atabwera nkuwona mutu wa Holofernesi uli m'manja mwa munthu wina pakati pa anthupo, adagwa pansi, nakomoka.

7Atamuutsa, iye adagwada ku mapazi a Yuditi nati, “Akuimbireni nyimbo zokutamandani ku zithando zonse za Yuda. Pakati pa mitundu ina ya anthu, onse amene adzamva dzina lanu adzadzidzimuka.

8Tsopano mundisimbire zonse zimene mwachita masiku apitaŵa.” Apo Yuditi adamuuza zonse kuchokera tsiku limene adachoka mpaka nthaŵi imeneyo, anthu onse alikumva.

9Atangomaliza kufotokoza, anthu adayamba kufuula kwambiri, ndipo mzindawo udadzaza ndi phokoso lachimwemwe.

10Akiyore atamva zonse zimene Mulungu wa Israele adachita, adakhulupirira Mulungu kotheratu. Tsono adaumbalidwa nasanduka Mwisraele. Ndipo adzukulu ake ali nafe mpaka lero lino.

Mavuto ku chithando cha Holofernesi

11Kutacha, adapachika mutu wa Holofernesi pa linga. Tsono anthu onse adatenga zida zankhondo, napita m'magulumagulu ku mipata ya m'mapiri.

12Aasiriya ataŵaona, adatumiza uthenga kwa atsogoleri ao. Iwowo adapita kwa olamulira ankhondo, nduna zao ndi akuluakulu onse.

13Adapita ku hema la Holofernesi nauza kapitao wake kuti, “Kamdzutse mbuye wathu. Akapolo aja akufuna kutithira nkhondo, akungofuna pofera.”

14Bagowasi adapita naomba m'manja ali pafupi ndi nsalu yotsekera pa hema la m'kati. Ankaganiza kuti Holofernesi akugona ndi Yuditi.

15Ataona kuti sakuyankha, adakankha nsaluyo naloŵa m'chipinda chogona. Adangoona chithupi chokha chitagwera pansi, chopanda mutu, mutuwonso palibe.

16Adayamba kufuula ndi kulira kwamphamvu, nang'amba zovala zake.

17Kenaka adakaloŵa m'hema la Yuditi. Ataona kuti mulibe, adathamangira kumene kunali anthu nati,

18“Akapolo aja atigwira m'maso. Mkazi mmodzi Wachihebri wachititsa manyazi ufumu wa Nebukadinezara. Onani Holofernesi wafa, ndipo wamdula mutu.”

19Mau akewo adatayitsa mtima akuluakulu ankhondo a ku Asiriya. Adang'amba zovala zao, ndipo mudachitika phokoso loopsa m'zithandomo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help