1Ndiwe wokongola, iwe wokondedwa wanga!
Ndithuditu, ndiwe wokongoladi!
Kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo
maso ako akuwoneka oŵala ngati nkhunda.
Tsitsi lako likuchita pekupeku
ngati mbuzi zoti zikutsetsereka
pa mapiri a ku Giliyadi.
2Mano ako ali mbee ngati nkhosa zometa
zoti angozisambitsa kumene.
Mano onsewo ngoyang'anana bwino,
palibe chigwelu nchimodzi chomwe.
3Milomo yako ili ngati mbota yofiira,
ndipo pakamwa pako mpokongola zedi.
Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo,
masaya ako, akuwoneka ngati mabandu a makangaza.
4Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide,
yomangidwa bwino ndipo yosalala.
Mkanda wako wam'khosi, ngati zishango 1,000
zokoloŵeka kuzungulira nsanjayo.
5Maŵere ako ali ngati mbaŵala ziŵiri,
ngati mphoyo zamapasa
zimene zikudya pakati pa akakombo.
6Pamene kamphepo kamadzulo kakuyamba kuuzira,
ndipo mithunzi ikuthaŵa,
ndidzapita mofulumira ku phiri la mure,
ndi ku chitunda cha lubani.
7Ndiwe wokongola kwabasi,
iwe wokondedwa wanga.
Ulibe nkachilema komwe.
8Tiye tichokeko ku Lebanoni,
iwe mkazi wanga.
Tiye tichoke ku Lebanoni kuno,
utsagane ndi ine.
Utsikepo pa nsonga ya phiri la Amana,
pa nsonga ya phiri la Seniri ndi la Heremoni.
Uchokemo m'mapanga a mikango,
uchokeko ku ngaka za akambuku.
9Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga,
wangoti mtima wangawu kwe!
Wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako,
ndiponso ndi mphande imodzi
ya mkanda wa m'khosi mwako.
10Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga,
chikondi chako nchosangalatsa.
Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo,
mafuta ako ndi onunkhira bwino
kupambana zonunkhira zabwino zonse.
11Iwe mkazi wanga,
milomo yako ili uchi mvee!
Kunsi kwa lilime lako
kuli ngati uchi ndi mkaka.
Fungo la zovala zako
likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
12Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga,
uli ngati munda wopiringidza,
ngati munda wopiringidza,
ngati kasupe wochingidwa.
13Kumeneko mbeu zimakondwa bwino.
Munda wake, ngati dimba la makangaza
lokhalanso ndi zipatso zokoma zamitundumitundu,
ndi maluŵa amitundumitundu.
14Kuli mitengo ndi zitsamba zosiyanasiyana
zopangira zonunkhira zabwino kwambiri.
15Iwe uli ngati kasupe wothirira munda,
ngati chitsime cha madzi abwino,
ngati mitsinje yamadzi yochokera ku Lebanoni.
Mkazi
16Dzuka, iwe mphepo yakumpoto,
bwera kuno, iwe mphepo yakumwera.
Uuzire pa munda wanga
kuti fungo lake lokoma likwanire ponseponse.
Wokondedwa wanga aloŵe m'munda mwake,
adye zipatso zake zokoma.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.