1 Num. 1.1-46 Utatha mliriwo, Chauta adauza Mose ndi Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti,
2“Uchite chiŵerengero cha mpingo wonse wa Aisraele, kuyambira anthu aamuna a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, potsata mabanja a makolo ao, anthu onse a m'dziko la Israele amene angathe kumenya nkhondo.”
3Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adalankhula ndi atsogoleri m'zigwa za ku Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko, adati,
4“Muchite chiŵerengero cha anthu, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo,” monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Aisraele amene adatuluka m'dziko la Ejipito anali aŵa:
5Fuko la Rubeni. Rubeni anali mwana wachisamba wa Israele. Ana aamuna a Rubeni anali aŵa: Hanoki anali kholo la banja la Ahanoki. Palu anali kholo la banja la Apalu.
6Hezironi anali kholo la banja la Ahezironi. Karimi anali kholo la banja la Akarimi.
7Ameneŵa, anthu okwanira 43,730, ndiwo anali a m'mabanja a Rubeni, amene adaŵerengedwa.
8Mwana wa Palu anali Eliyabu,
9ndipo ana a Eliyabu anali Nemuwele, Datani ndi Abiramu. Ameneŵa anali omwe aja amene adasankhidwa mu mpingo, amenenso adakangana ndi Mose ndi Aroni pogwirizana ndi Kora, pamene adatsutsana ndi Chauta.
10Ndipo nthaka idang'ambika ndi kuŵameza onsewo pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lao lidafa pamene moto udapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo.
11Komabe a m'banja la Kora sadafe onse.
12Ana aamuna a Simeoni potsata mabanja ao ana aamuna a Simeoni anali aŵa: Nemuwele anali kholo la banja la Anemuele. Yamini anali kholo la banja la Ayamini. Yakini anali kholo la banja la Ayakini.
13Zera anali kholo la banja la Azera. Shaulo anali kholo la banja la Ashaulo.
14Ameneŵa, anthu okwanira 22,200, ndiwo a m'mabanja a Simeoni, amene adaŵerengedwa.
15Potsata mabanja ao ana aamuna a Gadi anali aŵa: Zefoni anali kholo la banja la Azefoni. Hagi anali kholo la banja la Ahagi. Suni anali kholo la banja la Asuni.
16Ozini anali kholo la banja la Aozini. Eri anali kholo la banja la Aeri.
17Arodi anali kholo la banja la Aarodi. Areli anali kholo la banja la Aareli.
18Ameneŵa, anthu okwanira 40,500, ndiwo anali a m'mabanja a Gadi, amene adaŵerengedwa.
19Ana aamuna a Yuda anali Ere ndi Onani, koma iwowo adafera m'dziko la Kanani.
20Potsata mabanja ao ana ena aamuna a Yuda anali aŵa: Sela anali kholo la banja la Asela. Perezi anali kholo la banja la Aperezi. Zera anali kholo la Azera.
21Tsono ana aamuna a Perezi anali aŵa: Hezironi anali kholo la banja la Ahezironi. Hamuli anali kholo la banja la Ahamuli.
22Ameneŵa, anthu okwanira 76,500, ndiwo anali a m'mabanja a Yuda, amene adaŵerengedwa.
23Potsata mabanja ao ana aamuna a Isakara anali aŵa: Tola anali kholo la banja la Atola. Puva anali kholo la banja la Apuva.
24Yasubu anali kholo la banja la Ayasubu. Simeoni anali kholo la banja la Asimeoni.
25Ameneŵa, anthu okwanira 64,300, ndiwo anali a m'mabanja a Isakara, amene adaŵerengedwa.
26Potsata mabanja ao ana aamuna a Zebuloni anali aŵa: Seredi anali kholo la banja la Aseredi. Eloni anali kholo la banja la Aeloni. Yaleele anali kholo la banja la Ayaleele.
27Ameneŵa, anthu okwanira 60,500, ndiwo anali a m'mabanja a Zebuloni, amene adaŵerengedwa.
28Potsata mabanja ao ana aamuna a Yosefe anali aŵa: Manase ndi Efuremu.
29Ana aamuna a Manase anali aŵa: Makiri anali kholo la banja la Amakiri. Makiri anali bambo wa Giliyadi. Giliyadi anali kholo la banja la Agiliyadi.
30Ana aamuna a Giliyadi anali aŵa: Iyezere anali kholo la banja la Aiyezere. Heleki anali kholo la banja la Aheleki.
31Ndipo Asiriele anali kholo la banja la Aasiriele. Sekemu anali kholo la banja la Asekemu.
32Semida anali kholo la banja la Asemida. Hefere anali kholo la banja la Ahefere.
33Koma Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi okhaokha. Ana aakazi a Zelofehadi anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.
34Ameneŵa, anthu okwanira 52,700, ndiwo anali a mabanja a Manase, amene adaŵerengedwa.
35Potsata mabanja ao ana aamuna a Efuremu anali aŵa: Sutela anali kholo la banja la Asutela, Bekeri anali kholo la banja la Abekeri. Tahani anali kholo la banja la Atahani.
36Ndipo ana aamuna a Sutela anali aŵa: Erani anali kholo la banja la Aerani.
37Ameneŵa, anthu okwanira 32,500, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a ana aamuna a Efuremu, zidzukulu za Yosefe potsata mabanja ao.
38Potsata mabanja ao ana aamuna a Benjamini anali aŵa: Bela anali kholo la banja la Abela. Asibele anali kholo la banja la Aasibele. Ahiramu anali kholo la banja la Aahiramu.
39Sefufamu anali kholo la banja la Asefufamu. Hafamu anali kholo la banja la Ahufamu.
40Ndipo ana aamuna a Bela anali Aradi ndi Namani. Aradi anali kholo la banja la Aaradi. Namani anali kholo la banja la Anamani.
41Ameneŵa, anthu okwanira 45,600, ndiwo anali a m'mabanja a Benjamini, amene adaŵerengedwa.
42Potsata mabanja ao ana aamuna a Dani anali aŵa: Suhamu anali kholo la banja la Asuhamu. Ameneŵa ndiwo mabanja a Dani potsata mabanja ao.
43Anthu oŵerengedwa pa mabanja onse a Suhamu adakwanira 64,400.
44Potsata mabanja ao ana aamuna a Asere anali aŵa: Imina, anali kholo la banja la Aimina. Isivi anali kholo la banja la Aisivi. Beriya anali kholo la banja la Aberiya.
45Ana aamuna a Beriya anali aŵa: Hebere anali kholo la banja la Ahebri. Malikiele anali kholo la banja la Amalikiele.
46Mwana wamkazi wa Asere anali Sera.
47Ameneŵa, anthu okwanira 53,400, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a Asere.
48Potsata mabanja ao ana aamuna a Nafutali anali aŵa: Yazeele anali kholo la banja la Ayazeele. Guni anali kholo la banja la Aguni.
49Yezere anali kholo la banja la Ayezere. Silemu anali kholo la banja la Asilemu.
50Ameneŵa, anthu okwanira 45,400, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a Nafutali.
51Chiŵerengero chonse cha Aisraele chinali 601,730.
52 Num. 34.13; Yos. 14.1, 2 Chauta adauza Mose kuti,
53“Uŵagaŵire dziko anthu ameneŵa, kuti likhale choloŵa chao, molingana ndi chiŵerengero cha maina ao.
54Fuko lalikulu ulipatse choloŵa chachikulu, fuko laling'ono choloŵa chaching'ono. Fuko lililonse lilandire choloŵa chake molingana ndi chiŵerengero cha anthu ake.
55Koma dzikolo uligaŵe mwamaere. Alandire choloŵa chao potsata kuchuluka kwa maina a mafuko a makolo ao.
56Choloŵa chaocho, uchigaŵe pakati pa fuko lalikulu ndi laling'ono mwamaere.”
57Potsata mabanja ao chiŵerengero cha Alevi chinali motere: Geresoni anali kholo la banja la Ageresoni. Kohati anali kholo la banja la Akohati. Merari anali kholo la banja la Amerari.
58Mabanja a Alevi anali aŵa: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amahali, banja la Amusi, banja la Akora. Kohati anali bambo wa Amuramu.
59Mkazi wa Amuramu anali Yokebede mwana wa Levi, amene adabadwira ku Ejipito. Yokebedeyo adamubalira Amuramu ana aŵa: Aroni, Mose ndi Miriyamu mlongo wao.
60Num. 3.2 Aroni adabala Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
61Lev. 10.1, 2; Num. 3.4 Koma Nadabu ndi Abihu adafa chifukwa adaapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta.
62Onse amene adaŵerengedwa mwa Aleviwo anali 23,000, kuyambira ana aamuna a mwezi umodzi ndi opitirirapo. Iwowo sadaŵaŵerengere kumodzi ndi Aisraele, chifukwa sadapatsidwe choloŵa pakati pa Aisraele.
63Ameneŵa ndiwo anthu amene adaŵerengedwa ndi Mose ndi wansembe Eleazara. Iwowo adaŵerenga Aisraelewo ku zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani, ku Yeriko.
64Koma pakati pa anthu ameneŵa panalibe ndi mmodzi yemwe wamoyo amene adaaŵerengedwa kale ndi Mose ndi wansembe Aroni, pamene ankaŵerenga Aisraelewo ku chipululu cha Sinai.
65Num. 14.26-35 Paja za iwowo Chauta adati, “Adzafera m'chipululu.” Sadatsale ndi mmodzi yemwe mwa iwo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.