1Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama.
2Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
3Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa.
4Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.
5Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.
6Munthu akamati amakhala mwa Mulungu, zochita zake zizilingana ndi zimene Yesu ankachita.
Za lamulo latsopano7 Yoh. 13.34 Inu okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lakale lomwe lija, limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi. Lamulo lakalelo ndi mau amene mudaŵamva kale.
8Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Zimene lamuloli likunena, zidachitikadi mwa Yesu, ndipo zikuchitikanso mwa inu. Pajatu mdima ulikutha, ndipo kuŵala kwenikweni kwayamba kale kuti ngwee.
9Munthu akamati ali m'kuŵala, komabe nkumadana ndi mnzake, akali mu mdima ameneyo.
10Koma munthu wokonda mnzake, amakhala m'kuŵala, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.
11Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso.
12Inu ana, ndikukulemberani popeza kuti Mulungu wakukhululukirani machimo anu chifukwa cha dzina la Khristu.
13Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja.
14Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja.
15Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.
16Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
17Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Za woukira Khristu18Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi.
19Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu.
20Koma inuyo, mudadzozedwa ndi Woyera uja, ndipo nonse mukudziŵa.
21Ndakulemberani, osati chifukwa chakuti simudziŵa choona, koma chifukwa chakuti mumachidziŵa, ndipo mukudziŵanso kuti bodza silichokera ku choona.
22Wabodzayo ndani? Kodi si amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Wokana Atate ndi Mwana, ameneyo ndiye Woukira Khristu.
23Aliyense wokana Mwana, alibenso Atate. Wovomereza Mwana, alinso ndi Atate.
24Koma inu, zimene mudamva kuyambira pa chiyambi, zikhalebe m'mitima mwanu. Zimene mudamva kuyambira pa chiyambi zikakhalabe m'mitima mwanu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndi mwa Atate.
25Ndipo chimene adalonjeza nchimenechi: moyo wosatha.
26Ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuuzeni za iwo aja amene amafuna kukusokeretsani.
27Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
28Tsono ananu, khalani mwa Iye, kuti tikakhale olimba mtima Iye akadzaoneka, ndipo tisadzachite manyazi Iye akadzabweranso.
29Ngati mukudziŵa kuti Khristu ndi wolungama, musapeneke konse kuti aliyense wochita chilungamo, ndi mwana wa Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.