Mphu. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za ukulu wa Mulungu

1Amene ali ndi moyo wamuyaya,

ndiye amene adalenga zonse.

2Ambuye okha ndiwo olungama,

palibenso wina koma Iwo okha.

3Amayendetsa dziko lapansi ndi chala chokha,

ndipo zinthu zonse zimamvera malamulo ao.

Paja Iwo ndi Mfumu ya zinthu zonse,

amaonetsa mphamvu zao polekanitsa zinthu zoyera ndi

zinthu wamba.

4Palibe munthu amene Ambuye adamtuma

kuti akalalike ntchito zao.

Ndani angathe kufufuza bwino ntchito zao zodabwitsa?

5Palibe ndi mmodzi yemwe amene angathe kudziŵa

kukula kwa mphamvu zao.

Palibenso amene angathe kufotokoza mbiri yonse ya

ntchito zao zachifundo.

6Munthu sangathe kuwonjezera pa ntchitozo kapena kuchotsapo,

nkosatheka kuzitsata bwino zodabwitsa zonse za Ambuye.

7Pamene munthu wamaliza nkhani imeneyi,

ndiye kuti wangoyamba kumene,

ndipo akalekeza, amangotibe kakasi.

Zakuti munthu si kanthu konse

8Kodi munthu nchiyani, ndipo ali ndi ntchito yanji?

Kodi ntchito zake zabwino ndi zoipa zimaonetsa chiyani?

9Masiku a moyo wake mwina angakwanire zaka 100,

akatero ndiye kuti wafika patali.

10Tikazilinganiza ndi nthaŵi yamuyaya,

zaka za moyo wake zili ngati kadontho kamodzi

m'nyanja kapenanso ngati kamchenga kamodzi.

11Nchifukwa chake Ambuye amaŵalezera mtima anthu,

ndipo amaŵachitira chifundo.

12Amaona ndi kudziŵa tsoka limene litha kuŵagwera.

Nchifukwa chake amaŵakhululukira kaŵirikaŵiri.

13Munthu amachitira chifundo anzake okha,

koma Ambuye amachitira chifundo zolengedwa zonse.

Amazidzudzula, amaziphunzitsa ndi kuzilangiza,

amazibweza monga m'mene mbusa amazichitira nkhosa zake.

14Amachitira chifundo onse otsata malangizo ao,

ndi amene amamvera mwachangu malamulo ao.

Za luso la kupatsa

15Mwana wanga, uzichitira anzako zabwino

mosatonzera,

ndipo ukapereka kanthu, usanenepo mau oŵaŵa.

16Kodi suja mame amaziziritsa kutentha?

Chimodzimodzinso mau angathe kupambana mphatso.

17Zoonadi mau abwino amapambana mphatso yaikulu,

munthu wokoma mtima ali ndi ziŵiri zonsezo.

18Chitsiru chimangonyoza ndi kunyodola anzake,

mphatso ya munthu womana imaŵaŵitsa maso.

Za kuganizira bwino ndi kuwoneratu zam'tsogolo

19Usanalankhule uyambe waganizira bwino,

ndipo udzisamale usanayambe kudwala.

20Asanakuweruze, uyambe wadzifunsitsa bwino,

ndipo udzapeza chikhululukiro akakuzenga mlandu.

21Udzichepetse usanayambe kudwala,

ndipo ukachimwa ulape msangamsanga.

22Chilichonse chisakuletse kuchita zimene udalumbira,

ndipo usadikire mpaka imfa kuti ukonze zinthu.

23Usanalumbire, uyambe waganiza bwino,

usakhale ngati munthu woyesa Ambuye.

24Uganiziretu za ukali umene udzakumane nawo pa

nthaŵi ya kufa,

ndiponso za chilango chimene udzachiwone

ngati Ambuye adzakufulatira.

25Pa nthaŵi uli ndi zakudya zambiri,

uzikumbukira nthaŵi ya njala,

ndipo pa nthaŵi uli ndi umphaŵi ndi ya usiŵa,

uzikumbukira nthaŵi ya chuma.

26Kuchokera m'maŵa kufikira madzulo, pakatipa

zinthu nkusintha.

Zoonadi zinthu zimasinthika msanga pamaso pa Ambuye.

27Munthu wanzeru amakhala tcheru nthaŵi zonse,

ndipo pa masiku oipa amasamala kuti asachimwe.

28Munthu aliyense wanzeru amaphunzira luntha,

ndipo amalemekeza amene adalipeza.

29Anthu omvetsa zisudzo

amasanduka aluntha iwo omwe,

ndipo amakamba miyambi yoyenera.

Za kudziletsa

30Usamvere mapendekero ako oipa,

ndipo uletse zilakolako zako zosayenera.

31Ukatsata zilakolako zako,

adani ako adzakuseka.

32Usakonde zosangalatsa zamtengowapatali,

kuti ungaonongeretu ndalama zako.

33Usasanduke mmphaŵi pobwereka ndalama zochitira

maphwando pamene m'thumba mwako mulibe kanthu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help