1Kutada, atumiki a Holofernesi adatuluka mofulumira. Bagowasi adatseka hema chakubwalo, naletsa atumiki onse kuti asaloŵemo m'hema la mbuye wake. Kenaka onse adapita kukagona, chifukwa phwando lidaatenga nthaŵi yaitali kotero kuti onsewo adaatopa zedi.
2Yuditi adatsala yekha m'hemamo, ndipo Holofernesi anali atagona tulo tofa nato, chifukwa choti adaaledzera kwambiri.
3Yuditi adauza mdzakazi wake kuti ayambe wakhala kunja kwa chipinda chogona ndi kumdikira mpaka atuluke kuti akapemphere, monga ankachitira masiku onse. Anali atamfotokozeranso Bagowasi zomwezo.
4Tsono onse atapita, osatsalapo ndi mmodzi yemwe, Yuditi adakaimirira pafupi ndi bedi la Holofernesi, nayamba kupemphera chamumtima kuti, “Inu Ambuye, Mulungu wamphamvuzonse, tsopano mundithandize pa zimene ndikufuna kuchita, kuti mzinda wa Yerusalemu ukhale ndi ulemerero.
5Tsopano ndiye nthaŵi yake yoti mupulumutse anthu anu, ndipo kuti mundikhozetse pa zimene ndakonza, zoti ndiwononge adani amene atiwukira.”
6Atatero, adapita ku bedi pafupi ndi mutu wa Holofernesi, namsolola lupanga lake.
7Adasendera pafupi ndi bedi nkumugwira tsitsi nati, “Inu Ambuye, Mulungu wa Israele, mundipatse mphamvu tsopano.”
8Pamenepo adatema Holofernesi pa khosi kaŵiri ndi mphamvu zake zonse, namdula mutu.
9Adachotsa mtembowo pa bedi, nakhulula nsalu zochingira bedi zija. Kenaka adatuluka ndi mutu wa Holofernesi, naupatsira mdzakazi wake.
10Iyeyo adaulonga m'thumba lake la zakudya.
Yuditi ndi mdzakazi wake abwerera ku BetuliyaTsono akazi aŵiriwo adapita pamodzi monga momwe ankachitira nthaŵi zonse pokapemphera. Adabzola zithando zankhondo za Aasiriya. Adazungulira chigwa, nakwera phiri mpaka kukafika pa zipata za Betuliya.
11Yuditi akali kutali adaitana alonda apazipata kuti, “Tsekulani, tsekulani chipata. Ambuye, Mulungu wathu, akali nafebe, ndipo akutiwonetsa mphamvu zake ndi nyonga zake polimbana ndi adani athu, monga momwe watichitira lero.”
12Anthu amumzinda atamva mau a Yuditi, adathamangira ku chipata, naitana akuluakulu amumzinda.
13Aliyense, wamkulu ndi wamng'ono, sadathe kukhulupirira kuti Yuditi adabwerera. Adatsekula chitseko naŵaloŵetsa akazi aŵiriwo. Adasonkha moto kuti aŵaone, nasonkhana moŵazungulira.
14Tsono Yuditi adakweza mau nati, “Tamandani Mulungu, mtamandeni ndithu. Tamandani Mulungu amene sadaleke kuchitira chifundo Aisraele, koma watswanya adani athu kudzera mwa ine usiku womwe uno.”
15Atatero, adatulutsa mutu wa Holofernesi uja m'thumba nausonyeza kwa anthu. Adati, “Onani mutu wa Holofernesi, mtsogoleri wamkulu wa ankhondo a ku Asiriya. Nazinso nsalu zimene anachingira bedi lake atagona ali chiledzerere. Ambuye amkantha ndi dzanja la munthu wamkazi.
16Tsono ndikulumbira pali Ambuye amene andipulumutsa pa njira yonse imene ndayenda, kuti ngakhale nkhope yanga idaamuchititsa kaso Holofernesi, ndithu sadachite nane zoipa. Choncho sindidaipitsidwe, ndipo sindingachite konse manyazi.”
17Anthu onse adadabwa kwambiri ndipo adapembedza Mulungu moŵeramitsa mitu pansi. Onse pamodzi adati, “Mutamandike, Inu Ambuye, Mulungu wathu, amene mwaonongeratu adani a anthu anu lero.”
18Owe. 5.24; Lk. 1.28, 42Tsono Uziya adauza Yuditi kuti, “Mwana wanga, Mulungu Wopambanazonse wakudalitsa koposa akazi onse pa dziko lapansi. Alemekezeke Ambuye Mulungu amene adalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, amene adakutsogolera podula mutu wa mtsogoleri wamkulu wa adani athu.
19Ndithu chikhulupiriro chako mwa Mulungu sichidzaiŵalika m'mitima ya anthu, akamalingalira za mphamvu za Mulungu.
20Mulungu akulemekeze kosalekeza chifukwa cha zimene wachita, ndipo akudalitse. Sudaope kupereka moyo wako chifukwa cha dziko lathu, pamene linali pa mavuto. Watipulumutsa ku chiwonongeko cha mtundu wathu ndipo monsemo wayenda molunjika pa njira ya Mulungu.” Pamenepo anthu onse adati, “Inde momwemo! Inde momwemo!”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.